“Pitani tsono, nanunso muzikachita chimodzimodzi.” Luka 10:37
Kuyambira chaka cha 1992, Mpingo wa Katolika, wakhala ukukondwerera Tsiku Lokumbukira Odwala pa 11 February, lomwenso ndi tsiku lomwe Mpingo umakondwerera chaka cha Amai Maria a ku Lourdes. Tsiku Lokumbukira Odwalali liri ndi mfundo zitatu. Choyamba, ndi kukumbutsa Akhristu kuti azipemphera molimbika ndi mokhulupirika, kupempherera odwala. Chachiwiri, pa tsiku limeneli, Akhristu amapemphedwa kuti asinkhesinkhe ndi kuchitapo kanthu pothandiza odwala. Ndipo chachitatu, tsiku ili ndi lokumbukira ndi kuyamikira onse amene amagwira ntchito yosamalira ndi kutumikira odwala. Chaka chili chonse pa tsikuli, office ya zaumoyo ku Vatican, ya Pontifical Council for Health Pastoral Care, imatumiza uthenga wochokera kwa Apapa wotikumbutsa za tsikuli.
Nawu tsono uthenga wochokera kwa Apapa wa chaka chino pa tsiku lokumbukira anthu odwala lomwe tikulikondwerera pa 11 February, 2013.
Okondeka Abale ndi Alongo,
- Pa 11 February, 2013, ndi tsiku lokumbukira Amai Maria a ku Lourdes (Our Lady of Lourdes), ndipo pa tsiku limeneli kudzakhala chikondwerero cha nambala 21 cha tsiku lokumbukira odwala pa dziko lonse. Mwambo waukulu wa tsikuli ukachitikira ku Shrine ya Amayi Maria ku Alotting (Marian Shrine of Altotting). Pa tsiku limeneli, anthu odwala, ogwira ntchito zaumoyo, akhristu ndi anthu ena onse akufuna kwabwino amakhala ndi “nthawi yopambana yopemphera, yogawana, ndi kulolela kuvutika kaamba kofunira Mpingo zabwino ndipo imeneyi ndi nthawi yoti anthu onse aone ndi kuzindikira nkhope ya Khristu mwa abale ndi alongo ao amene akuvutika ndi kusautsidwa kaamba ka matenda osiyanasiyana, komanso azindikire kuti pamene Khristuyo adazunzika, naafa ndi kuuka kwa akufa, anadzetsa chipulumutso ku mtundu wonse wa anthu” (adatero Yohane Paulo Wachiwiri, m’kalata yake yokhazikitsa tsiku lokumbukira odwala, pa 13 May, 1992, 3).
Pa mwambo okumbukira odwalawu ndikumva kukhudzidwa nanu limodzi, inu abwenzi anga, amene pogwira ntchito yosamalira odwala m’zipatala kapena kunyumba, mukukumana ndi zokhoma zochuluka kaamba ka mazunzo ndi matenda. Choncho ndikufuna kukulimbitsani ndi mau a nthumwi za ku msonkhano wachiwiri wa Vatikani onena kuti, “simuli nokha, simunatayike, simunalekereredwe ndiponso sindinu opanda pake”, akuthuzitseni mtima. Mwaitanidwa ndi Khristu ndipo ndinu chithunzi cha moyo wake” (adalembedwa mu Uthenga opita kwa osauka, odwala ndi ozunzika).
- Pofuna kukhala nanu muuzimu pa ulendo wochokera ku Lourdes, amene ali malo opatsa chiyembekezo komanso chisomo, kupita ku Shrine ya Amayi Maria ku Alotting; ndifuna kukuemphani kuti muganizire ndi kusinkhasinkha za fanizo la Msamaria Wachifundo (Onani Luka 10:25 – 37). Fanizo la mu Mthenga Wabwino limeneli ndi chitsanzo chimodzi cha zinthu zosiyanasiyana zochitika m’moyo wathu tsiku ndi tsiku, zomwe Ambuye Yesu akutithandizira nazo kuti timvetse mozama za chikondi cha Mulungu pa munthu aliyense, makamaka pa iwo amene akuzunzika ndi ululu ndiponso matenda osiyanasiyana.
Tikawona mawu wotsiriza mu fanizo la Msamaria Wachifundoli, “Pitani tsono, nanunso muzikachita chimodzimodzi” (Luka 10:37), Ambuye Yesu akutiwonetsa m’mene munthu aliyense wotsatira Khristu, akuyenera kuganizira, kuwonera ndiponso momwe akuyenera kuchitira kwa anthu ena, makamaka kwa iwo amene ali osowa. Tikuyenera kuphunzira kuchokera ku chikondi cha Mulungu, kudzera pokhala naye mu ubale pakupemphera kwambiri; kuti pa moyo wathu wa tsiku ndi tsiku, tizikhudzidwa kwambiri, monga adachitira Msamaria Wachifundo, ndi anthu amene akudwala m’nthupi ndi muuzimu, iwo amene akusowa thandizo lathu, owadziwa ndiponso osawadziwa, komanso mosayang’anira kusauka kwao. Izi ndi zoona osati kwa okhawo amene amagwira ntchito zaumoyo kapena ntchito yolalikira ndi kufalitsa Mau a Mulungu, komanso aliyense ngakhale amene akudwala, amene akudutsa m’zipsinjo ndi chikhulupiriro. “sipakuthawa kapena pakudzipatula ku zovuta za ena pamene timachiritsidwa, koma pamene tilimba mtima, kuvomereza, kukhwima m’maganizo ndi kupeza tanthauzo pakukhala amodzi ndi Khristu, amene adazunzika kaamba ka chikondi.” (Spe Salvi, 37)
- Atsogoleri osiyanasiyana a mu Mpingo, adaona nkhope ya Yesu Khristu mwa Msamaria Wachifundo uja, ndipo mwa munthu amene adakumana ndi achifwamba uja adaona nkhope ya Adamu, kuyimira umunthu wathu wovulazidwa ndi wosokonezedwa kaamba ka machimo (Onani Ulaliki wa Origen wokhudza Mthenga Wabwino pa Luka 34: 1-9: ndemanga za Ambrose pa Mthenga Wabwino wa Luka Woyera, 71-84; Ulaliki wa Augustino, nambala 171). Yesu ndi Mwana wa Mulungu, Iye amene amatiwonetsa chikondi cha AAtate ake, chikondi chokhulupirika, chamuyaya ndi chopanda malire. Komanso Yesu ndi amene anasiya umulungu wake pofuna kukhala amodzi ndi anthu. (Onani Afilipi 2:6-8), nkulola kusauka monga anthu ena onse mpaka kufa ndi kukalowa m’limbo monga timanenera mu pemphero la Kumvera kwa Apostoli pofuna kudzetsa chiyembekezo ndi kuwala. “Iyeyu anali ndi umulungu chikhalire, komabe sadayese kuti kulingana ndi Mulungu ndi chinthu choti achigwiritse. (Afilipi 2:6), koma podzazidwa ndi chifundo, adayang’ana kuzunzika kwa anthu pofuna kuti apereke mafuta achithuzitso ndi vinyo wachiyembekezo.
- Pa nthawi ino pomwe tilinso mu Chaka cha Chikhulupiriro tikuyenera kulimbikitsa ntchito zachifundo m’maparishi ndi m’miphakati ndiponso m’mabanja mwathu, pofuna kuti aliyense mwa ife asanduke Msamaria wa Chifundo kwa anzake, makamaka kwa iwo amene tayandikana nawo. Pano, ndifuna nditchulepo za anthu ena mu Mpingo amene anathandiza odwala kuti apeze machiritso ndi kukhalanso ndi moyo wamphamvu ndi wathanzi. Anthu otere ali chitsanzo chotilimbikitsa. Ena mwa iwo ndi monga
- Tereza Woyera wa Mwana Yesu ndi Nkhope Yoyera, amene anali kadaulo wa sayansi ya chikondi cha Mulungu (scientia amoris) (Onani Novo Millennio Ineunte, 42). Iyeyu anali ndi chaulere chokhudzidwa mozama ndi masautso a Ambuye Yesu omwe ndi matenda amene anamutengera ku imfa atadutsa m’masautso aakulu kwambiri (Onani mau amene analankhulidwa kwa anthu ochuluka pa 6 April, 2011).
- Wolemekezeka Luigi Novarese, amene anthu akumkumbukirabe mpaka lero; yemwe kudzera mu utumiki wake, anazindikira kufunikira kopempherera odwala ndiponso kufunikira kopemphera limodzi ndi odwala ndi osautsidwa. Kawirikawiri ankatsagana nawo popita ku ma shrine a Amayi Maria (Marian shrines), makamaka ku goloto la ku Lourdes.
- Ndipo Raoul Follereau, pokhudzidwa ndi chikondi chokonda mnzako monga udzikondera, anapereka moyo wake ku ntchito yosamalira anthu odwala nthenda yakhate yotchedwa “Hansen’s disease” ndipo iye anafikira anthu otere ku madera akutali kwambiri. Mpaka anafika pokhzazikitsa tsiku lokumbukira odwala khate.
- Tereza Wodala wa ku Calcutta, amene poyamba pa tsiku lirilonse ankayamba kukumana ndi Ambuye Yesu mu Ukaristia kenaka nkumapita kukakumana ndi anthu osauka amene ankakhala m’mbali mwa miseu, kwinaku iyeyo akuchita mapemphero a korona. Ankapeza ndi kusamalira odwala makamaka iwo amene analibe “owasamalira, osakondedwa ndiponso ooneka ngati otayika”.
- Anna Schaffer Woyera wa ku Mindelstetten, iyenso anaona mavuto ake ngati ofanana ndi a Khristu: “Chipinda chake chodwaliramo chinasanduka ngati ndende ndipo kuzunzika kwake kunali ngati utumiki. Koma molimbikitsidwa ndi Ukaristia womwe anali kulandira tsiku ndi tsiku, anasanduka ngati mkhalapakati kudzera m’mapemphero ake ndiponso anali ngati chithunzi cha chikondi cha Mulungu kwa anthu ochuluka amene anadza kwa iye kudzafuna uphungu” (Onani ulaliki wa pa tsiku lomutchula Woyera, 21 October, 2012).
- Mu Mthenga Wabwino tikuwonanso Amayi Maria Virgo Wodala akutsagana ndi mwana wawo wozunzidwa mpaka ku Gologota. Iwo sanataye mtima konse ndipo anakhulupirira chigonjetso cha Mulungu pa tchimo, ululu ndi pa imfa, ndipo amadziwa kuvomereza mwachikhulupiriro ndi mwachikondi za Mwana wa Mulungu wobadwira ku Betelehemu amene anafera pamtanda. Chikhulupiriro chawo cholimba mwa mphamvu ya Mulungu, chinaoneka poyera kudzera m’kuuka kwa Khristu kwa akufa, chinthu chimene chinapereka chiyembekezo kwa onse ozunzika ndi kukulitsa chikondi ndi chithuzitso cha Ambuye.
- Potsiriza, ndifuna kuyamika ndi kulimbikitsa athu ogwira ntchito zaumoyo ndi magulu ena onse a m’madayosizi ndi m’miphakati, a m’zipani zamumpingo amene amatanganidwa ndi ntchito zosamalira odwala, mabungwe a anthu ogwira ntchito zachipatala ndiponso onse ogwira ntchito mongodzipereka. Onse a zindikire kwathunthu kuti, Mpingo umagwira ntchito zake mwachikondi ndi mwachifundo komanso movomereza ndi molandira munthu wina aliyense, makamaka iwo amene ali ofooka ndi odwala.(Christifideles Laici,38).
Ndikupereka tsiku ili la nambala 21, Lokumbukira Anthu Odwala, mu uneneri wa A Mai Maria a Zaulere, omwe akulemekezedwa ku Altotting, kuti nthawi zonse azikhala pambali pa iwo amene amafunafuna mtendere ndi chiyembekezo. Ndikupempha kuti Amai Mariawo athandize onse amene akutengapo gawo mu utumiki wachifundo, kuti asanduke Asamaria Achifundo kwa abale ndi alongo ao osautsidwa ndi matenda osiyanasiyana.
Ndikupereka kwa inu nonse, madalitso a Upostoli wanga.
Papa Benedicto wa sixteen.