Uthenga Ochokera kwa a Papa pa tsiku lokumbukira anthu odwala – 11 February, 2012)

‘Nyamuka, pita. Chikhulupiliro chako chakuchiritsa’ (Lk 17:19)
Okondedwa abale ndi alongo,
Pa tsiku lokumbukira anthu odwala lomwe lagwa pa tsiku la 11 February, 2012, lomwenso ndi tsiku lokumbukira Mai wathu wa ku Lourdes, ndafuna ndilumikizane ndi anthu onse odwala omwe ali mzipatala kapenanso kunyumba kwao, ndicholinga chofuna kuwawonetsa  kukhuzidwa ndi chikondi cha mpingo wonse. Pozindikira ndi kukondwera ndi umoyo wa munthu, makamaka kwa odwala ndi ofowoka, akhristu amachitira umboni Uthenga Wabwino potsatira mapazi a Khristu amene adamva zowawa za moyo wa Thupi ndi wa Uzimu pofuna kutipulumutsa.
1. Chaka chino, pamene tikuyamba kukonzekera mwambo waukulu okumbukira anthu odwala onse padziko lapansi,  womwe udzachitike pa 11 February, 2013 ku Germany, wosogoleredwa ndi mau a mu Uthenga wabwino wa Luka,  za Msamaria wa chifundo (cf. Lk 10:29-37), ndafuna kutsindika za ‘masakramenti ochiritsa’ pamene tikukamba za ma sakramenti a Kulapa ndi Kudzodza omwe amafika pake penipeni mu Sakramenti la Ukaristia.
Mu nkhani ya Yesu ndi anthu khumi odwala nthenda ya khate monga adalembera Luka woyera (cf. Lk 17:11-19), makamaka poyang’ana mawu omwe Yesu akuwuza m’modzi wa iwo akuti: ‘‘Nyamuka, pita. Chikhulupiliro chako chakuchiritsa’ (v. 19), zitithandize ife kumvetsa kufunika kokhala ndi chikhulupiliro  maka kwa iwo amene akumva zowawa chifukwa cha matenda, kuti potero Ambuye sakhala nawo kutali. Pokhala pafupi nawo, odwala amazindikira kuti okhulupilira Yesu sakhala yekha. Mulungu mwa mwana wake satitaya ife pa mavuto athu ndipo amakhala pafupi nafe, kutithandiza ndi kutichiritsa ku zotivuta  mitima yathu. (cf. Mk 2:1-12).
Chikhulupiliro cha wakhate m’modzi uja, yemwe, mosiyana ndi anzake ena aja, atawona kuti wachiritsidwa, ndipo atadzadzidwa ndichisangalalo komanso kuzizwa, adabwerera kwa Yesu kukathokoza. Izi zikutiphunzitsa ife kuti; kuchira kumatenda kuli ndi tanthauzo lakuya koposera kupeza mphamvu za moyo wathu wa nthupi. Ndi chidzindikiro cha chipulumutso chathu chimene Mulungu amachipereka kudzera mwa Yesu Khristu, chotsimikidziridwa mu mau a Iye mwini; ‘chikhulupiliro chako chakupulumutsa’. Iye amene apemphera pa nthawi ya matenda ndi mavuto, amakhulupilira kuti sadzalephera kuona chikondi cha Mulungu ndi cha mpingo wonse, womwe ndi dzanja lake pansi pano. Kuchiritsidwa kwa mu thupi ndi chidzindikiro chooneka ndimaso cha chipulumutso cha munthu yense wathuthu, thupi ndi mzimu pamodzi. Motero, Sakramenti lirilonse, limatisonyeza chifupi cha mphamvu ya Mulungu pakati pathu, komano kudzera mu dzinthu zooneka ndi maso athu. (Homily, Chrism Mass, 1 April 2010). Kulumikizana kwa chilengedwe ndi kuwomboledwa kumawoneka chamaso kudzera mu njira zoterezi. Masakramenti ndi zizindikiro zolongosolera momveka bwino zinsinsi cha chikhulupiliro chathu, popeza amafotokozera za umodzi wa thupi ndi mzimu wa munthu. (Homily, Chrism Mass, 21 April 2011).
Ntchito yayikulu ya mpingo ndiyo kulalika za Ufumu wa Mulungu, ‘kulalika kumene kuyenera kubweretsa machiritso: ‘thunzitsani onse osweka mitima’ (Is 61:1)” (ibid.), udindo womwe Yesu adatsiira ophunzira ake (cf. Lk 9:1-2; Mt 10:1,5-14; Mk 6:7-13). Mgwilizano wa machiritso a thupi ndi chiyambi cha moyo wina watsopano pambuyo pa kukhulukuzika ndi matenda, zimatithandiza ife kumvetsa za ‘masakramenti a machiritso’.
2. Kambiri,  Sakramenti la kulapa lakhala liri chithime cha kutsinkhasinkha kwa atsogoleri a mpingo, makamaka chifukwa cha kufunikira kwake pa moyo wa tsiku ndi tsiku wa akhristu, ndipoganiziranso kuti, ‘ Mphamvu za sakramentili zimatilumikizitsa ife ku chifundo cha Mulungu, ndinso kutithandiza kuphathana naye ngati abwenzi ake enieni. (Katekisimu wa Katolika, 1468). Pamene mpingo ukupitilira kulalika za chikhululukiro ndi chiyanjano, umalimbikitsa anthu onse mosalekeza za chiphunzitso cha kutembenuka ndi ndi kukhulupilira Uthenga Wabwino. Monga Paulo mpositoli, nawonso umabwereza kunena kuti:  ‘Tsono ndife akazembe oimirira Khristu, ndipo kudzera mwa ifeyo, Mulungu mwini ndiye akulankhula nanu mokudandaulirani. Tikukupemphani m’dzina la Khristu kuti muvomere kuyanjananso ndi Mulungu.’ (2 Akor. 5:20). Yesu Khristu ali pansi pano adalalika ndi kuwonetsa chifundo cha Mulungu Atate. Iye sadabwere kudzaweruza koma kudzakhululukira ndi kupulumutsa, kudzapereka chiyembekezo mthawi ya mdima wa mavuto ndi uchimo, kudzapereka moyo wosatha; kudzera mu sacrament la kulapa, mu mankhwala a kukhululukira machimo,  uchimo sutitayitsa mtima kotheratu, koma  m’malo mwake timakomana ndi chikondi chomwe chimakhululuka ndi kutisintha. (cf. John Paul II, Post-Synodal Apostolic Exhortation Reconciliatio et Paenitentia, 31).
Mulungu, ‘wachifundo chachikulukulu’ (Eph 2:4), monga bambo mu fanizo la m’Malembo Oyera (cf. Lk 15:11-32), saumitsira  mtima ana ake, koma amawadikira, amawasakasaka, nkuwapeza mu ukapolo wa kudzikana ndi kudzipatula kwawo, ndipo amawaitana ku thebulo lake kuti akondwelere mphatso chikhululukiro ndi chiyanjano. Nthawi ya mavuto, imene anthu amatha kukhala ndi zinyengo zofuna kutaya mtima ndi kugwetsedwa mphwayi, imeneyi itha kukhala nthawi ya zaulere za Mulungu ndi kudzibweza ku maganizo oyipa ngati  mwana wosokera uja, amene anaganizanso bwino za moyo wake, polingalira zolephera ndi zofowoka, ndi kulakalaka kutsata njira yobwerera kwa Atate. Ndipo Atate mwa chikondi chawo chachikulukulu , nthawi zonse amakhala tcheru ndipo amayembekezera kudza  kwa ana ake, kuti choncho awapatse mphatso ya chikhululukiro ndi chimwemwe.
3.  Powerenga  mau a mu Uthenga Wabwino, zikuwonekeratu kuti Yesu ankakhuzidwa ndi anthu odwala. Sadangowatuma ophunzira ake kuti akapoletse mabala awo (cf. Mt 10:8; Lk 9:2; 10:9) koma adawakhazikitsira sakramenti la padera; sakramenti la kudzodza. Kalata ya Yakobe ikutsimikiziranso za sakramentili pamasiku a akhristu oyamba (cf. Mt 10:8; Lk 9:2; 10:9): Podzodza odwala, motsogozedwa ndi mapemphero a akulu a mpingo, odwala onse amakhala mchisamaliro cha  Yesu wonzunzidwa ndi wa ulemerelo, kuti choncho awachotsere mavuto awo ndi kuwapulumutsa; mpingo umawathandiza kulumikizana ndi masautso ndi imfa ya Khristu ndipo pakutero athe kutumikira mbumba ya Mulungu.
Sakramenti limeneli limatithandiza kumvetsa bwino za zozizwitsa ziwiri zomwe zidachitika pa phiri la Olivi, pamene Yesu mwanjira yodabwitsa adawona zonse zomwe Atate adamukonzera monga kunzunzika kwake komanso  chikondi cha Atate ake, chomwe anachivomera kwathuthu. Mu nthawi ya zovuta ija, iye anakhala mkhalapakati wathu, ‘ povomera mazunzo onse adziko la pansi, adatembenuza kulira kwathu ndi kukhala nthawi ya kuomboledwa. (Lectio Divina, Meeting with the Parish Priests of Rome, 18 February 2010).
Komanso, ‘munda wa Olivi ndi malo omwe iye adanyamukira kubwerera kwa Atate ake kumwamba, choncho ndi malo a kuwomboledwa kwathu…… Zozizwitsa ziwiri zimenezi zikupitilira kugwira ntchito mu mpingo, mu mafuta omwe amagwira ntchito popereka masakramenti…… chizindikiro cha zabwino za Mulungu  kwa ife, (Homily, Chrism Mass, 1 April 2010). Podzodza anthu odwala, mafuta odzodzera amapatsidwa kwa ife ngati mankhwala a Mulungu………amene akutikumbutsa za kukoma mtima kwake, kutipatsa mphamvu ndi kutithunzitsa mitima, komanso kutiwululira zazikulu zomwe zilipo patsogolo pa kuchiritsidwa ku matenda athu, zazikulu za kuwukanso ndi moyo wina (cf. Jas 5:14)” (ibid.).
Sakramenti limeneli ndilofunika kuliganizira bwino masiku ano poyang’anira mbali zonse zokhudza kumvetsa za Mulungu komanso mu utumiki wathu kwa anthu odwala. Potsata mapemphero omwe timagwiritsa ntchito popempherera odwala, osati pokhapokha pamene munthu ali pafupi kufa (cf. Catechism of the Catholic Church, 1514), sakramenti la kudzodza lisamawoneke ngati laling’ono pofananiza ndi masakramenti ena. Kudzipereka ku ntchito yosamalira ndi kulalikira iwo amene akudwala ndi chizindikiro cha kukoma mtima kwa Mulungu kwa anthu omwe akuvutika, komanso kumabweretsa mwai kwa ansembe komanso akhristu eniake kuti zomwe tikuwachitira anthu ovutika, tikuchitiranso Yesu mwini (cf. Mt 25:40).
4. Ndipo pokamba za sakramenti la machiritso, Augustino woyera akutsindika kuti: “ Mulungu amachiritsa matenda anu onse. Choncho, musakhale ndi mantha, zolakwa zanu zonse zidzakhululukidwa……Muyenera kumulola kuti akuchiritseni ndipo musaletse dzanja lake kuti likukhudzeni”  (Exposition on Psalm 102, 5; PL 36, 1319-1320). Izi ndi zida za chifundo cha Mulungu zomwe zimathandiza munthu wodwala kuti amvetse za misteri za imfa komanso kuwuka kwa Yesu Khristu.
Mogwirizana ndi masakramenti awiriwa, ndikufuna kutsindikenso za sakramenti la Ukalistia. Polandila Ukaristia pamene  munthu akudwala, Thupi ndi Magazi a Yesu Khristu amatilumikiza ndi iye ku nsembe yomwe adaipereka yopulumutsira anthu onse. Mpingo wonse, makamaka iwo amene ayandikana ndi ma parishi, ayenera kumayesetsa kumalandira sakramenti la Ukalistia pafupipafupi, ndiponso kuyesetsa kufikira anthu omwe chifukwa cha matenda kapena ukalamba sangathe kuyenda kuti alandire sakramentili kawirikawiri. Mu njira imeneyi, abale athuwa amapatsidwa mwai wolimbikitsa ubale wao ndi Yesu Khristu yemwe adafa ndi kuwuka, ndipo pakutero amatenga nawo mbali potukula chikondi cha Yesu mu mpingo wake. Ndipo pa mfundo imeneyi, nkofunika kuti ansembe amene amagwira ntchito yawo mzipatala ndi m’malo ena oyang’anira odwala, ngakhale mnyumba za anthu odwalawo, azidziwa kuti ndi antchito ake a Yesu omwe akufikira anthu omwe akuvutika. (Message for the XVIII World Day of the Sick, 22 November 2009).
Polumikizana ndi mbiri ya chipulumutso chathu mwa Yesu Khristu, zomwe timazichitanso pamene tikulandira chakudya cha moyo wa uzimu, timafika pa chithimethime chake pamene tikulandila Ukalistia ngati ‘kamba wa paulendo’. Pa nthawiyi, mau awa a Ambuye Yesu akuti “Aliyense odya thupi langa ndi kumwa magazi anga adzakhala ndi moyo wosatha, ndipo ndidzamuwukitsa kwa akufa pa tsiku lomaliza” (Jn 6:54), amakhala akupereka tanthauzo lake momveka bwino. Ukalistia, makamaka ngati ‘kamba wa paulendo’ monga adafotokozera Ignasio woyera wa ku Antiokea, “ndi mankhwala otipezesa moyo osatha ndi chitetezo chotichinjiriza ku imfa” (Letter to the Ephesians, 20: PG 5, 661); sakramentili ndi njira yotichotsa ku imfa kupita ku moyo, kuchoka ku moyo uno kupita kwa Atate, amene akudikira anthu onse mu Yerusalemu ya kumwamba.
5. Mutu womwe ukutitsogolera poganizira za anthu odwala wakuti “Nyamuka, pita. Chikhulupiliro chako chakuchiritsa’  ukutipatsa chithunzithunzi cha chaka cha chikhulupiliriro chomwe chizatsekuliridwe  pa 11 October 2012, imene izakhala nthawi yabwino yodzikumbusanso za mphamvu ndi kukoma kwa chikhulupiliro, ndikuchita kawuniwuni wa zenizeni zake za chikhulupiliro, komanso kuchitira umboni chikhulupilirocho m’moyo wathu wa tsiku ndi tsiku (cf. Apostolic Letter Porta Fidei, 11 October 2011).
Ndikufuna kulimbikitsa onse odwala ndi ovutika kuti nthawi zonse azipeza chilimbikitso mu chikhulupiliro, chomwe chimakula pakumvetsera mawu a Mulungu, popemphera komanso polandira masakramenti, pamenenso ndikupempha atumiki a mu mpingo kuti nthawi zonse adzifikira anthu odwalawa. Potsatira nkhani ya m’busa wabwino, ndipo ngati otsogolera nkhosa zomwe zidapatsidwa kwa iwo, ansembe ayenera kukhala osangalala, kumvetsera iwo amene ali ofowoka, onyozeka ndi ochimwa, kuwawonetsa chifundo cha Mulungu ndi mawu a chilimbikitso m’chikhulupiliro (cf. Saint Augustine, Letter 95, 1: PL 33, 351-352).
Kwa onse ogwira ntchito za umoyo, ndi onse omwe akuwona nkhope ya Yesu Khristu  wodzuzika mwa abale awo, ndikupitiliza kuwathokoza ndi kuthokoza m’malo mwa mpingo onse, chifukwa mu ukadaulo ndi mkupilira kwawo, ngakhale pamene sakutchula dzina la Khristu,  amachitirabe iye umboni mu njira yowona (cf. Homily, Chrism Mass, 21 April 2011).
Mwa Maria, mai wa chifundo ndi ubwino wa anthu odwala, tikukweza maso athu a chikhulupiliro ndi pemphero lathu; tikupempha kuti ndi chifundo chanu cha umai, chomwe chidawoneka pa nthawi imene mudaimilira pansi pa mtanda wa mwana wanu, muthandize ndi kulimbikitsa chikhulupiliro cha odwala onse ndi ovutika pa ulendo wa machiritso a zowawa za moyo wawo wa thupi komanso wa mzimu.
Ndikukutsimikizirani nonse kuti ndizikukumbukirani m’mapemphero, ndipo ndikukudalitsani nonsenu ndi mphamvu za utsogoleri wanga.
Kuchokera ku Vatican, pa 20 November 2011, tsiku lokumbukira Yesu Mfumu ya dziko lonse.
BENEDICTUS PP. XVI

Leave a Comment

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Scroll to Top
× How can we help you?