Cholinga cha mafunsowa ndi kuthandiza Mpingo kuti mwa ufulu ufotokoze za m’mene ukuwonwre za moyo wa achinyamata ndi kuunikira bwino m’mene akuthandizidwira kuvomera kuitanidwa kwawo kuti pakutero tikhale ndi mfundo zabwino zotiwongolera, instrumentum laboris.
Pozindikira kuti tikuchokera malo kapena madera osiyanasiyana, pali mafunso atatu a padera amene afunsidwa mogwirizana ndi delaro ndipo afunsidwa pambuyo pa funso la 15 kuti choncho Mpingo wakumenekonso ukhale ndi chidwi ndikutengapo mbali pa nkhaniyi.
Kuti ntchitoyi iyende bwino, magulu onse okhudzidwa akupemphedwa kuti zokambilana zawo zilembedwe pa tsamba limodzi lokha basi pa mafunso wofuna kupeza kalembera. Tsamba limodzi lowunika za m’mene kuderalo kuliri ndi lina lokhudza moyo wa kuderalo. Ngati nkoyenera mfundo zina zikhozanso kulembedwa ngati ndemanga pa zomwe zafufuzidwazo.
1. Kalembera
Ngati nkotheka, musonyeze komwe mwapeza kalembera wanu pamodzi ndi chaka chake. Ndipo mfundo zina zonse zofunikira muziike pamodzi kuti choncho zithandize kumvetsa bwino lomwe zomwe zikuchitika m’maiko osiyanasiyana.
– Chiwerengero cha anthu olowa m’dziko kuchokera kwina kapenanso chiwerengero cha m’mene anthu akuberekerana.
– Chiwerengero cha achinyamata (a zaka 16 mpaka 29) m’dziko/m’maiko
– Chiwerengero cha Akatolika m’dziko/m’maiko
– Zaka zomwe achinyamata ambiri akulowera m’banja (zaka 5 zapitazo) poyerekeza amuna ndi akazi, komanso zaka zomwe akupita ku Seminare ndi kulowa m’moyo wa nzipani za mu mpingo poyerekeza amuna ndi akazi.
– Pakati pa a zaka 16 – 29, omwe ambiri ndi ana a sukulu ndi a pantchito, ngati nkotheka munene ntchito yomwe ambiri akugwira komanso amene sali pa ntchito.
2. Kuunikira mmene zinthu zilili
a) Achinyamata, mpingo ndi mudzi
Mafunso awa akukhudza achinyamata womwe ali ndi chidwi ndi kutengapo gawo pa zochitika mu Mpingo ndi amene satekeseka ndi za Mulungu.
1. Kodi Mpingo umakhudzidwa bwanji ndi moyo wa achinyamata ku deralo?
2. Kodi ndi mavuto akulu-akulu ati omwe achinyamata akukumana nawo ? Nanga ndi ziti zimene zingatukule moyo wa achinyamata m’dziko mwanu lero/kwathu kuno ku Malawi?
3. Kodi ndi magulu ati kapena malo ati amene achinyamata amakumanako amene akuthandiza kutukula moyo wa achinyamata mu mpingo, nanga mukuganiza kuti nchifukwa chiyani?
4. Kodi ndi magulu ati kapena malo ati amene achinyamata amakumanako amene akuthandiza kutukula moyo wa achinyamata kunja kwa mpingo, nanga mukuganiza kuti nchifukwa chiyani?
5. Ndi chiyani chenicheni chimene achinyamata amayembekeza kuchokera ku Mpingo m’dziko/m’maiko mwanu?
6. Kodi achinyamata ali ndi mwayi wotani wotengako mbali pa kayendetsedwe ka mpingo m’dziko mwanu/m’maiko mwanu?
7. Mukuchitapo chani, nanga pali njira zanji zothandizira achinyamata amene sapita ku Tchalitchi kawirikawiri?
b) Ntchito zolimbikitsa mayitanidwe kwa Achinyamata
8. Kodi mabanja ndi miphakati/malimana akutenga nawo mbali bwanji pa za moyo wosinkhasinkha za mayitanidwe wa Achinyamata?
9. Kodi sukulu( za pulayimale ndi sekondale) ndi sukulu zaukachenjede( za mpingo ndi boma) zikuthandiza bwanji pa moyo wosula Achinyamata pa za kuitanidwa?
10. Kodi tikulandira bwanji kusintha kwa chikhalidwe komwe kwadza chifukwa cha kutukuka kwa makina a zowulutsawulutsa(digital world) ?
11. Kodi zaka/miyambo ya Achinyamata pa dziko lonse lapansi kapena misonkhano ina yochitika m’maiko ndi dziko lonse lapansi zingatenge gawo lanji polimbikitsa moyo wauzimu wa Achinyamata?
12. Kodi Diocese yanu ikuchita bwanji pa zolimbikitsa moyo wa mayitanidwe wa Achinyamata.
c) Utumiki wa Atsogoleri a Mpingo kwa Achinyamata
13. Kodi tikuyesetsa motani nanga pali njira yanji imene Atumiki a Mulungu ndi atsogoleri ena akuwongolera achinyamata pa moyo wawo wa uzimu?
14. Kodi pali njira zina kapena mwayi wina zomwe zidakhazikitsida zothandiza achinyamata kuvomera bwino kuitanidwa kwawo?
15. Kodi pali upangiri wanji womwe ukuperekedwa ku ma Seminare/ ku sukulu zosulira ansembe?
d) Mafunso olingana ndi dela
AFRICA
a. Kodi pali njira zanji ndi dongosolo lanji lomwe linayikidwa lothathiza achinayamata pa zakuitanidwa kwawo ku dera lanu?
b. Kodi mau woti ulangizi pa za uzimu (spiritual fatherhood) amatanthauza chani ku dera limene munthu wakula popanda mlangizi (father figure)? Nanga amathandizidwa motani?
c. Kodi achinyamata amauzidwa zotani pa ntchito yomanga tsogolo la Mpingo?
AMERIKA
a. Kodi dera lanu likusamalira bwanji Achinyamata amene akukumana ndi mavuto ngati; kukhala m’magulu auchigandanga, ukayidi, mankhwala osokoneza bongo, kulowa m’banja mokakamizidwa? Nanga akuthandizidwa bwanji pa moyo wawo wa tsiku ndi tsiku?
b. Kodi ndi nsulo wanji womwe ukuperekedwa pothandiza Achinyamata kuti atenge nawo mbali mu dera lanu pofuna kupitititsa patsogolo ubwino wa anthu onse?
c. Mu dziko lapansi lomwe lalowa chikunja, ndi ntchito ziti zomwe zingapititse patsogolo moyo wauzimu popitiliza moyo wachikhulupiliro womwe umayamba pamene munthu walandira masakaramenti a chinamwali/Masakramenti oyamba achikhristu(Ubatizo,Ukaristia, Ulimbitso)?
MAIKO ACHIMWENYE, ACHILUYA NDI APA NYANJA ZIKULUZIKULU ZAMCHERE
a. Kodi nchifukwa chiyani ndipo ndi njira iti imene imapangitsa kuti misonkhano yachipembedzo ya amene siakatolika idzikopa Achinyamata?
b. Kodi ndi zikhalidwe ziti zomwe tingazisakanize ndi maphunzitso achikhristu posasokoneza moyo wodziyeretsa?
c. Kodi chiyankhulo chomwe achinyamata akugwiritsa ntchito lero chikugwiritsidwa bwanji ntchito posamalira moyo wauzimu wa Achinyamata maka pazowulutsa mawu, pa masewero osiyanasiyana ndi mu nyimbo?
KU ULAYA
a. Kodi ndi chithandizo chanji chomwe chikuperekedwa kwa achinyamata pa za tsogolo lawo ndi chikhulupiliro komanso chiyembekezo, potengera ndi m’mene maziko achikhristu alili ku ulaya?
b. Achinyamata nthawi zambiri amawona ngati akusalidwa pa za ndale, zachuma ndi pa moyo wawo wa tsiku ndi tsiku. Kodi mukuchitapo chani potenga nkhawa za achinyamata kuti ziwathandiza kutengapo mbali pa zochitika?
c. Kodi ubale wa mibadwo yosiyanasiyana ukugwira bwanji ntchito? Ngati palibe chomwe chikuchitikapo, tingabwezeretse bwanji ubale umenewu?
3. Kugawa Ntchito
1) Tchulani zigawo zikuluzikulu za ntchito za moyo wauzimu ndi za moyo osinkhasinkha za mayitanidwe zomwe zikuchitika mu nthawi ino
2) Sankhani zinthu zitatu zomwe mukuziwona kuti ndi zosangalatsa ndi zofunika kugawana ndi mpingo wonse mayi wathu Ekklezia katolika, ndipo muzifotokoze motere(ntchito iliyonse ilembedwe pa tsamba lake).
a. Kufotokoza: m’mizere yochepa fotokozani ntchito. Akutsogolera ndi ndani? Ntchito ikuchitika bwanji? Ntchito ikuchitikira kuti? ndi zina ndi zina.
b. Kuwunikira: zukutani ntchito momveka bwino, kuti nfundo zikuluzikulu zimveke bwino: kodi zolinga/zofuna zathu ndi ziti? Kodi maziko ake ndi ati? Ndi nfundo ziti zomwe zili zopatsa chidwi/zosangalatsa? Nanga kuti zifike pano zadutsa motani? ndi zina ndi zina.
c. Kuwona phindu la ntchito yathu: kodi zolinga/zofuna zathu ndi ziti? Ngati talephera kukwaniritsa zolinga zathu, chapangitsa ndi chiyani? Ndi pati pomwe zili bwino nanga tafowoka pati? Kodi zotsatirazi zikukhudza bwanji moyo wathu, pa chikhalidwe ndi mu mpingo? Kodi ndi chifukwa chani ndipo ndi mu njira yanji ntchitoyo ili yofunikira?