1
CHIFUNDO CHA MULUNGU NGATI NJIRA YA CHIYEMBEKEZO
Za Momwe Zinthu Zilili m’Malawi pa za Chuma ndi Ndale
Uthenga Wapadera 13th March 2016
Bungwe la Aepiskopi Akatolika M’dziko muno (ECM)
2
Kalata ya Bungwe la Aepiskopi Akatolika M’dziko la Malawi
Kwa Akhristu Akatolika ndi Anthu Onse Akufuna Kwabwino
Tikupereka mafuno abwino kwa inu nonse m’dzina la Ambuye athu Yesu Khristu
yemwe ndi nkhope ya chifundo cha Mulungu Atate. “Mulungu ndi wachifundo
chachikulukulu” (Aefeso 2:4). Adadziwulula kwa Mose kuti ndi “Mulungu wachifundo
ndi wokoma mtima, wosakwiya msanga, wodzaza ndi chikondi chosasinthika ndiponso
wokhulupirika kwa anthu ake” (Eksodo 34:6). “Koma nthawi itakwana” (Agalatia 4:4),
Yesu wa ku Nazarete adasonyeza nkhope ya chifundo cha Mulungu Atate kudzera
m’mau, m’zochita ndiponso m’moyo wake wonse (cf. Misericordiae Vultus, 1).
Kasupe wa chimwemwe, mtendere ndi kudekha kwa Mkhristu ndi chifundo. Poyamba,
izi zili chonchi chifukwa ndi chinthu chachikulu chimene Mulungu adachita pofuna
kudzakhala pakati pathu ngati munthu mzathu. Kachiwiri, chifundo ndi chimene
chimatiunikira m’mitima mwathu tikayang’anitsitsa anzathu pa ulendo wa moyo wao.
Potsiriza, chifundo ndi ulalo umene umatilunzanitsa ndi Mulungu ndi kutipatsa
chiyembekezo chakuti Iye adzatikonda nthawi zonse ngakhale kuti ndife anthu
ochimwa amene timakomana ndi zopinga zambiri pa moyo wathu (cf. Misericordiae
Vultus, 2). Mulungu amaona ndi kukhudzidwa ndi chimwemwe ndi chiyembekezo
chathu komanso mavuto ndi zonse zotidetsa nkhawa. Amazindikira zokhoma zomwe
timakumana nazo masiku onse. Kudzera m’Chifundo chake, Ambuye satisiya tokha ai.
Iye amasamalira aliyense wa ife ndipo amatifunira zabwino ndi kulakalaka kuti tonse
tizikondwera ndi kukhala ndi chimwemwe komanso mtendere. Iyi ndi njira imene
chifundo cha chikondi cha Chikhristu chathu chiyenera kutsata (cf. Misericordiae
Vultus, 9).
Mau Otsogolera
Ife, Aepiskopi Akatolika a Bungwe la Episcopal Conference of Malawi (ECM),
mounikiridwa ndi Kalata yapadera ya Papa Francis yofotokoza za Chaka Chopatulika
cha Jubile ya Chifundo cha Mulungu, (Misericordiae Vultus), imene imatsindika za
chifundo cha Mulungu makamaka kwa anthu amene akuvutika ndi zokhoma zambiri
m’moyo wao, tikukhulupirira kuti ino ndi nthawi yabwino yoti tipereke uthenga
wachiyembekezo komanso wotithandiza ife tonse kuganizira bwino moyo wathu kuti
tiyanjane poyamba ndi Mulungu komanso anzathu ndiponso chilengedwe chonse (cf.
Misericordiae Vultus). Jubilee ya Chifundo ikutipatsa chiyembekezo, mwai wotha
kukonzanso ndi kuyambanso mwatsopano zochitika pakati pathu potsogoleredwa ndi
Chifundo cha Mulungu mokhulupirira kuti Mulunguyo ndi Atate amene sangatisiye
tokha (Malaliko a Pope Francis ku Casa Santa Marta, pa 14 December 2015).
Kodi ndi anthu angati amene akukumana ndi zokhoma ndi zotayitsa mtima pakati
pathu masiku ano? Ndi ochepa okha amene angathe kulephera kuzindikira kuti pali
kusiyana kokhumudwitsa pakati pa anthu olemera amene ali ndi zonse zowayenera
pa moyo wao ndi anthu osauka amene ali m’mizinda ngakhalenso kumadera aku
3
midzi ya m’dziko lathu lino. Chokhumudwitsa kwambiri ndi chakuti izi ziri chonchi
chifukwa chisankho cholakwika cha ndondomeko za chuma chomwe amachita anthu
amene ali pautsogoleri. Ndi chachidziwikire kuti kusowa kwa chilungamo sivuto
lokhalo losowa kuti tilikonze; komanso pali mavuto ena monga kusankhana mitundu
kapena chigawo chimene tikuchokera, kusowa kwa makhalidwe abwino pa
kagwiritsidwe ka ndalama, kulowa pansi kwa maphunziro, kuba ndi kusowetsa
ndalama za Boma, kusadziwa chenicheni chomwe tikufuna, kulowa pansi kwa
zintchito zotumikira anthu, kukwera mtengo kwa zinthu komanso njala yosatha ndi
mavuto enanso amene tiyenera kuwaganizira ndi kuwakonza. Nkhawa zimenezi
zatipangitsa ife kuti tifunse ngati Malawi monga dziko kuti kodi tili nao maganizo
kapena njira zimene zingathandize kukonza zinthuzi kuti zisinthe ndi kukhalanso
bwino? Chinthu chimodzi chodziwikiratu ndi chakuti; tikukhala ngati sitikudziwa
kumene tili kupita ndi zomwe tikufuna kukwaniritsa pofuna kuthetsa mavuto amenewa.
Ngati Abusa anu, tikufuna kunenetsa pano kuti sibwino ndipo ino sinthawi yakuti
titayiretu mtima ndi kumangodikira imfa, ai. M’chaka Choyerachi, ndi udindo wathu kuti
tilalike mthenga ndi kuchita zinthu zothunzitsa mtima anthu osauka, kudzetsa
chipulumutso kwa onse opezeka mu ukapolo watsopano umene wadza chifukwa cha
kusintha kwa zinthu, kuthandiza iwo amene akulephera kuona choonadi chifukwa
akungodziganizira iwo eni komanso kubwezeretsa ulemelero wa aliyense amene
saganiziridwanso kuti ndi anthu (cf. Yesaya 61:1-2). Ngakhale kuti tikukumana ndi
zokhoma zambiri pa moyo wathu ngati Fuko, tikupemphedwa kuti tikhale anthu a
chiyembekezo chomwe ndi mphatso ya mtengo wapatali yofumira kwa Mulungu.
Mphatso ya chiyembekezo imatithandiza kuti timasangoona mavuto,
zowawa,zokhoma ndi machimo athu okha ai. Chiyembekezo chimatithandiza kuona
Chifundo cha Mulungu ndipo monga Paulo Woyera amanenera; “pokhulupirira,
timapulumuka” (Aroma 8:24). Tiyeni tizikumbukira nthawi zonse kuti, chifukwa cha
ubwino wa Chifundo chake, Mulungu atha kutikhululukira machimo athu, kuchiza
matenda athu, kupulumutsa moyo wathu ndi kutipatsa mphotho ya chikondi ndi
chifundo chake chosasinthika (cf. Salimo 103: 3-4).
Pachifukwa ichi, ndi mtima wa chiyembekezo womwewu, tikufuna kuyamba ndi
kuyamikira zabwino zonse za chitukuko zomwe zachitika m’dziko lathu lino zomwe
zingathe kusintha moyo wathu ngati zitalandira thandizo ndi chisamaliro chokwanira.
Tikupemphanso Fuko lonse la Malawi ndi onse amene ali ndi maudindo osiyanasiyana
kuti aganizire mozama ndi kupeza ndondomeko zochepetsera kusiyana kwakukulu
kumene kulipo pakati pa anthu olemera ndi osauka. Tikupempha akatswiri athu pa
nkhani ya za chuma m’dziko lino kuti ayankhe mwachilungamo funso lotsatirali: “Kodi
nkotheka kuti nkhani ya za chuma ndi ndondomeko zoyendetsera dziko iganizirenso
anthu osauka? Tikukumbukira mau achilimbikitso a Papa Francis kwa Akatolika ndi
kwa anthu onse akufuna kwabwino akuti, tiyenera kukonda dziko lathu ndi
kumadzipereka kwathunthu pofuna ubwino wa munthu aliyense (Malaliko a Papa
Francis, Mkatolika Wabwino Amatenga Nao Mbali pa Ndale, Vatican, 16 September
4
2013). Tikupempha Akatolika ndi anthu onse akufuna kwabwino kuti akwaniritse
udindo wao motsimikiza pofuna kumanga Fuko lachilungamo ndi lamtendere, lomwe
anthu ake adzalemekeza chilengedwe, ulemelero wa munthu aliyense, moyo wa
aliyense, ulemelero wa banja ndipo kuti anthu osauka ndi oponderezedwa
adzaganirizidwa poyang’anira ubwino wa munthu aliyense.
1. Zabwino Zina Zomwe Zachitika
Ngati nzika za dziko lino, tili ndi zifukwa zokwanira kuti tikondwere chifukwa cha
chitukuko chabwino chomwe chachitika m’zaka zapitazi. Tikuyamikira Amalawi onse
chifukwa chozindikira kufunika kukhala ndi Boma lotha kugwira ntchito yake mwa
ukadaulo. Izi zidaonekera poyera pamene mudatenga nawo mbali pa nthawi ya
masankho apatatu omwe adachitika m’chaka cha 2014, nthawi imene tidasankha
Prezidenti watsopano, Aphungu ndi Makhansala.
Tikuyamikira Boma ndi Mabungwe ena omwe si a Boma chifukwa chothandiza
mwansanga anthu omwe adaakhudzidwa ndi kusefukira kwa madzi. Zomwe
zidachitika ndi zotamandika ndi zoyera kuziyamika kwambiri. Mwapadera, tikuthokoza
Akhristu Eniake Akatolika amene adasonyeza mtima wa umodzi ndi onse omwe
adakhudzidwa ndi kusefukira kwa madzi popereka thandizo la zinthu zosiyanasiyana
kuphatikizapo ndalama. Zomwe zidachitikazi ndi umboni wabwino ndi wokwanira kuti
tikukwaniritsa zomwe Mulungu amafuna kuti tikhale anthu amene timasamalira abale
ndi alongo athu ovutika (Genesisi 4:9). Pochita zimene zija, inu Akhristu mudasonyeza
kuti “chifundo si ntchito ya Mulungu Atate okha ai, komanso ndi mulingo wodziwira
amene ndi ana ake enieni a Mulungu (cf. Misericordiae Vultus, 9). Chifundo
chimatiunikira za moyo watsopano ndipo chimatilimbitsa mtima kuti tione tsogolo lathu
ndi chiyembekezo (Misericordiae Vultus, 10).
Tikutsatira ndi chidwi zomwe Boma likuchita pofuna kukonzanso zintchito ndi
ndondomeko zotumikira nzika za dziko lino mwa njira yothandiza ndi ya ukadaulo.
Poyerekeza ndi Maboma am’mbuyomu, amene adali ndi alembi akulu ambiri, Boma
latsopanoli lachepetsa chiwerengero chao. Ena mwa iwo adatumizidwa kukagwira
zintchito zina ndipo ena adalandira peshoni. Chokondweretsa china ndi chakuti,
ndondomekoyi ikukhudza makampani ena Aboma kuti nawonso akonze njira
zatsopano zoyendetsera ntchito zao potumikira anthu mwaukadaulo. Awa ndi
makampani monga a zintchito zopereka madzi, magetsi ndi zina zotero. Tikufuna
kutsindikanso pano kuti tikusowadi kuti zinthu zisinthe makamaka mkhalidwe wandale
umene umachititsa anthu kuti azigwiritsa ntchito makampani Abomawa pofuna
kungokwaniritsa zolinga zao. Potengera zimene Utsogoleri wa dziko lino ukuchita
pofuna kukometsa kagwiridwe ka ntchito ka onse Am’boma, tikuona kuti izi
zitatsatidwa mokhulupirika, kusintha komwe kukusoweka kwambiri pakati pathu kutha
kuchitika pa ntchito yotumikira anthu zomwe zingathandize kuti anthu ayambenso
kulikhulupirira Boma. Izi ndi zabwino zosonyeza kuti tayamba kutsata njira yabwino
yoyendetsera dziko. Kusinthaku kutha kuthandiza anthu kukhala ndi mtima wolimbikira
5
pogwira ntchito, kudzilemekeza komanso kuthandiza Amalawi tonse kuti tikonde dziko
lathu osati Am’boma okha ai.
Ife, Aepiskopi a Mpingo wa Katolika ku Malawi, tikudziwa za kukula kwa chintchito ndi
kuvuta kwa zinthu zimene Boma lapirira mpaka pano zomwe zikuchitika chifukwa cha
maiko ndi mabungwe ena akunja omwe amafuna kupereka chithandizo chao ali ndi
cholinga chokwaniritsa zomwe iwo amafuna ndi mchitidwe wao womwe nthawi zina
umakhala wotsutsana ndi chikhalidwe chathu. Tikuyamika zomwe Boma lasonyeza
mpaka pano poonetsetsa kuti tisagonjere ku m’chitidwe wa anthu akunjawa monga
kukwatirana amuna kapena akazi okhaokha ndinso kutaya pakati. Tikufuna
kutsimikiza pano kuti mchitidwe woterewu sungotsutsana ndi chikhalidwe chathu
chokha ai, komanso umatsutsana ndi malamulo ndinso zikhulupiriro zathu.
Tikudziwa chidwi chomwe Boma likuonetsa pofuna kuti chakudya chisamasowe
m’dziko lino kudzera mu ulimi wothilira wotchedwa Greenbelt Initiative. Izi ndi zinthu
zotamandika kwambiri. Tikupempha Boma ndi mabungwe ena kuti aikirepo mtima pa
nkhani ya ulimi wothilira m’masikimu akuluakulu popeza dziko lathu la Malawi
limakumana ndi vuto la madzi osefukira komanso chilala kawirikawiri. Iyi ndi njira
yokhayo imene ife m’maganizo athu tikuona kuti ingathe kuthandiza kuthetsa vuto la
kusowa kwa chakudya ndi njala m’dziko lathu lino. Kuonetsetsa kuti nzika iliyonse ili
ndi mwai wopeza chakudya ndi njira imodzi yothandiza kuti ulemelero wa munthu
aliyense ukulemekezedwa ndi kutetezedwa. “Maufulu okhala ndi chakudya ndi
okhalira munthu aliyense padziko lonse lapansi ndipo wina sayenera kuwasintha
kapena kuwaphwanya” (Compendium of the Social Doctrine of the Church – CSDC,
153).
2. Zina Zodetsa Nkhawa Kwambiri
Titafotokoza zina mwa zabwino zimene takwaniritsa m’dziko lathu lino, tikufunanso
kutsindika mwachisoni kuti dziko lathuli silinakwaniritsebe zomwe timafuna kuti tikhale.
Poyamba, ife ngati Abusa anu, sitingathe kumangoonelera zinthu zikulowa pansi
monga ku mbali ya ntchito yotumikira anthu, kusiyana pakati pa anthu olemera ndi
osauka kumene kukunka kulirakulira tsiku ndi tsiku, kugwiritsa ntchito mosakaza
chuma cha Boma, kugwiritsa ntchito chuma cha Boma pa zinthu zosathandiza
kwenikweni pamene anthu akuvutika kwambiri, etc. Zonsezi ndi zofunika kuti tichitepo
kanthu. Kachiwiri, tikuda nkhawa chifukwa anthu akuuzidwa uthenga wolakwika
wosagwirizana ndi m’mene zinthu ziliri wofotokoza za m’mene chuma chikuyendera
makamaka kwa anthu amene amapeza ndalama pang’onopang’ono. Ndife
okhudzidwa kwambiri chifukwa dziko lathu silikuchita bwino pa nkhani ya za chuma.
Kachitatu, ife tikudandaula kwambiri chifukwa cha kusowa kwa chimanga m’dziko
lathu lino ndipo ndi zomvetsa chisoni kuti anthu ndi mavenda amene ali nacho
apezerapo mwai womachigulitsa pa mtengo wodula kwambiri. Potsiriza, ndife
okhudzidwa kwabasi ndi zomwe zikuchitika zatsopano pakati pathu poona anthu ena
akuchita kampeni kuti amai azitaya pathupi womwe ndi m’chitidwe ndi mkhalidwe
6
wokonda imfa m’malo mokonda moyo. Pachifukwa ichi, ukwati ndi moyo wa banja
pakati pa mwamuna ndi mkazi zili pa chiopsezo chifukwanso cha anthu amene
akuchita kampeni kuti amuna kapena akazi okhaokha azikwatirana.
2.1 Kampeni Yotaya Mimba
Polankhulapo za kuipa kwa mchitidwe wolimbikitsa kutaya mimba, ife tadaafotokoza
mwachimvekere maganizo athu m’Kalata yomwe tidakulemberani m’chaka cha 2013
yotchedwa Maphunzitso a Mpingo wa Katolika pa za Amuna Kapena Akazi
Okwatirana Okhaokha, Kuchotsa Mimba Ndiponso Njira Za Kulera. Pamene tsopano
anthu ayipinda nkhani yotaya mimbayi m’kampeni yao nkuitchula dzina latsopano loti
‘Uchembere Wabwino’, tawumirizidwa kuti titsindikenso maganizo athu pa nkhaniyi
pofuna kuthandiza anthu amene nkhaniyi ikuwasokoneza m’moyo wao.
Tikubwerezanso kunena mwachimvekere maganizo athu pankhani yakuti aliyense ali
ndi ufulu wokhala moyo ndi ulemelero wa moyo wamunthu (CSDC, 153). M’dziko,
limene anthu ake, pang’onopang’ono salemekezanso ulemelero wa moyo wa munthu,
Mpingo wa Katolika umalalika ndi kutsindika kuti moyo wa munthu ndi chinthu choyera
ndipo kuti ulemelero wa munthu ndizo maziko ndi masomphenya a makhalidwe
abwino pakati pa anthu. Timakhulupiriranso kuti kuyera ndi ulemelero wa moyo
munthu ndiye maziko a mfundo za Maphunzitso okhudza umunthu wathu. Kudzera
mwa anthu ndi mabungwe amene akulimbikitsa m’chitidwe ndi mkhalidwe wokonda
imfa pofuna kuti kukhale lamulo lovomereza kutaya mimba, moyo wa munthu uli pa
chiopsezo chachikulu.
Tikufuna kubwerezanso kunena kuti moyo wa munthu wina aliyense ndi wa mtengo
wapatali ndipo kuti anthu ndi ofunika koposa zinthu zomwe timafuna kukhala nazo.
Kulemekeza moyo wa munthu aliyense ndiye mulingo umene tingadziwire m’mene
mkhalidwe wa anthu oopa Mulungu. Pachifukwa ichi, tikupempha Aphungu athu aku
Nyumba ya Malamulo amene tidawasankha kuti ateteze moyo wa munthu pokana
kuvotera lamulo lovomereza kuphali. Potero, adzasonyeza kuti, ngakhale mwana
amene asanabadweyo, ali ndi ufulu wokhala moyo osati mai wake yekhayo, ai.
Mayeso aakulu kwa ife Akhristu siongoti ‘kodi tidasunga chikhulupiriro chathu, ai’,
koma kuti kodi tidachigawana bwanji ndi anzathu powathandiza kukhala ndi moyo.
M’Chaka ichi cha Jubile ya Chifundo, ndi udindo wathu ngati Abusa kupempha onse
amene akuvutika ndi maganizo chifukwa adatayako mimba kuti apemphe chifundo
cha Mulungu. “Pamene tikumva ululu mumtima mwathu chifukwa cha tchimo, Mulungu
amatimvera ndi kutiyankha mwachifundo chake chodzaza. Chifundo cha Mulungu ndi
chopambana tchimo lirilonse ndipo palibe amene angaike malire pa chikondi cha
Mulungu amene ali wokonzeka kutikhululukira nthawi zonse” (Misericordiae Vultus, 3).
7
2.2 Ulemelero wa Banja ndi Ufulu wa Ofuna Kukwatirana Amuna
Kapena Akazi Okhaokha
Masiku ano moyo wa banja uli pa chiopsezo chifukwa cha kampeni imene ikuchitika
ya ufulu wa anthu ofuna kukwatirana amuna kapena akazi okhaokha. Ngakhale kuti
zinthu zili chonchi, zotsutsana ndi maphunzitso a m’Malembo Oyera pa nkhani ya
ukwati, womwe umayenera kuchitika pakati pa mwamuna ndi mkazi, ife tikufuna
kutsindikanso mwachimvekere Maphunzitso a Mpingo wa Katolika kuti Banja ndi
lofunikira kwambiri pakati pa anthu ndipo ndi loyenera kutetezedwa, kuthandizidwa ndi
kulimbikitsidwa m’malo momalipeputsa. Anthu amakulira m’mabanja pakati pathu ndi
kukwaniritsa zomwe amafuna m’moyo wao. Komanso, ndi m’banja la mai ndi bambo
m’mene munthu amaphunziramo mfundo ndi makhalidwe oyenera kuti akhale nzika
yodalirika m’dziko.
M’Kalata yathu ya m’chaka cha 2013, tidafotokozamo maphunzitso a Mpingo wa
Katolika pa nkhani ya anthu ofuna kukwatirana amuna kapena akazi okhaokha.
Tsopano, popeza kuti nkhaniyi yabukanso, tikufuna kutsindikanso maganizo athu
omwe aja. Tikubwerezanso kunena kuti, munthu amene amakhala ndi chilakolako
chofuna kugonana ndi mwamuna kapena mkazi mzake, ali ndi vuto koma osati kuti
vutoli ndi tchimo pa lokha, ai. Tikunenanso kuti, ngati munthu wa chilakolako chotere
ngakhalenso munthu amene alibe, zikachitika kuti wagona ndi mwamuna kapena
mkazi mzake, mchitidwe wotere tiwuone kuti ndi woipa ndiponso wosavomerezeka.
Mpingo suweruza munthu amene ali ndi pendekero kapena vuto limeneli kuti ndi
wolakwa pamene sadachite tchimolo. Ndi zoona kuti kukhala ndi chilakolako chofuna
kugonana ndi mwamuna kapena mkazi mzako ndi vuto koma vutoli si tchimo palokha,
ai. Koma pamene wina achitadi zogonana kaya kukwatirana amuna kapena akazi
okhaokha, Mpingo siupsyatira Chichewa kunena poyera kuti: uku nkulakwa ndipo ndi
mchitidwe wosavomerezeka mpang’ono pomwe.
Poyang’anira zimene tanenazi, ife tikuona kuti Boma lidalakwitsa poyimitsa kaye
malamulo okhudza nkhani za anthu ogonana amuna kapena akazi okhaokha. Izi
zikutanthauza kuti anthu amene akuchita mkhalidwe woterewu sangazedwe mulandu,
ai. Boma lidangonjera kampeni ya anthu amene amatithandiza ndi ndalama zao
komanso mabungwe olimbikitsa maufulu a anthu akunja ndi a m’dziko lathu muno.
Ngati Abusa, tikuona njira imene tayamba kutsatayi ngati zomvetsa chisoni kwambiri.
Izi zikusonyeza kuti anthu amene akutitsogolera adatipusitsa pogulitsa dziko lathu ku
mkhalidwe woipa wakunja womwe ndi wotsutsana ndi kufuna kwa Mulungu chifukwa
cha ndalama. Nkhani iyi ili m’kamwam’kamwa, tikukumbukira zimene adaanena Papa
Wopuma Benedicto XVI zakuti, “Choonadi sichitengera kuchuluka kwa mavoti amene
anthu aponya, ai” (Light of the World: The Pope, the Church and the Signs of Times,
November 24, 2010). Tikupempha Akatolika ndi anthu onse akufuna kwabwino kuti
asafowoke pogwiritsitsa mfundo zokhazo zomwe zili zabwino ndi zolondola
makamaka masiku ano pamene pakuchitika kampeni ya ndalama zankhaninkhani
8
zofuna kupititsa patsogolo maufulu ndi mchitidwe wogonana amuna kapena akazi
okhaokha.
Ngakhale kuti sitivomereza mchitidwe wogonana amuna kapena akazi okhaokha
chifukwa kuteroko nkuchimwa, ife tikudzudzula mwamphamvu ndithu zomwe zakhala
zikuchitika masiku apitawa zomazunza kapena kuchitira nkhanza anthu amene
akukhudzidwa ndi nkhani za mtundu umenewu. M’Chaka ichi cha Jubile ya Chifundo,
tikukumbukira moyamika mau a Yohane XXIII Woyera omwe amatisonyeza ife njira
yoyenera kutsata ngati anthu okhulupirira Mulungu akuti: “Tsopano Mpingo wa Khristu
ukufuna kugwiritsa ntchito chifundo ngati mankhwala m’malo motenga zida
zoopsezera za nkhondo” (Gaudet Mater Ecclesia, 11). Ambuye akutipempha kuti
tisamaweruze kapena kuimba ena mlandu kuti ngolakwa (cf. Luka 6:37-38). Ngati
wina akufuna kupewa chiweruzo cha Mulungu, apewe kuweruza abale ndi alongo ake
kuti ngolakwa. Kuonjezera apa, Jubile ya Chifundo ikupereka mwai kwa onse
ochimwa kuphatikizapo amene amagonana amuna kapena akazi okhaokha wotha
kulandira chifundo cha Mulungu makamaka kudzera m’Sakramenti la Kulapa. Papa
Francis akuti Khomo Loyera la Chikondi lithandize aliyense m’chaka chimenechi kuti
aone ndi kumva chikondi cha Mulungu amene amathunzitsa mtima, amakhululukira
ochimwa ndi kupereka chiyembekezo kwa onse otaya mtima (cf. Misericordiae Vultus,
3). Choncho, kukhala achifundo monga Atate athu a Kumwamba ali achifundo ndiye
malangizo ndi mfundo yotitsogolera m’Chaka chimenechi.
2.3 Kutsika Kapena Kuperewera Kwa Zosoweka M’dziko Lathu
Maphunzitso a Mpingo opezeka m’buku la Gaudium et Spes amafotokoza za ‘Ubwino
Wokhalira Anthu Onse kuti ndi mfundo yofunikira kwa munthu aliyense, mabanja,
mabungwe, etc. pofuna kuti aliyense akwaniritse moyo ndi umunthu wake mokwanira
komanso mosavuta’ (GS, 26). Ndi zomvetsa chisoni; kuti kaya ndi chifukwa chosachita
chisankho chabwino pa nkhani ya za chuma, kaya ndi chifukwa chosagwiritsa bwino
ntchito chumachi m’Boma, m’dziko lathu lino zinthu zambiri zofunika pa moyo wa
anthu zalowa pansi kwambiri. Tikumva masiku onse kuti ndalama zothandizira
nthambi za Boma kutumikira ndi kuthandiza anthu mwanjira zosiyanasiyana zikunka
zicheperachepera tsiku ndi tsiku. Mwachitsanzo, zotsatira za kuchepa kapena kusowa
kwa ndalamaku zachititsa kuti zipatala zambiri zilephere kuthandiza anthu odwala
mokwanira chifukwa magalimoto a ambulasi komanso mankhwala ndi chakudya
kulibe.
Kulowa pansi kwa zintchito ndi thandizo m’zipatala zathu zonse m’dziko muno, ndi
kosoweka kuti Boma lichitepo kanthu mwansanga. Ndi zoona kuti tili ndi anthu amene
adaphunzira mokwanira ndipo ali ndi ukadaulo wosiyanasiyana m’magawo onse a
Boma lathu. Pachifukwa ichi, Boma likuyenera kudzudzulidwa pamene anthu amene
lidawatumawa kuti atumikire anthu m’zintchito zosiyanasiyana akulephera
kukwaniritsa udindo wao. M’mene zinthu zilili m’zipatala zathu masiku ano ndi
zomvetsa chisoni pa umunthu wathu komanso ndi zosavomerezeka.
9
Tili ndi nkhawa pozindikira kuti m’dziko lathu lino mulibe chipatala chomwe chili ndi
zoyenereza kuthandiza mwaukadaulo anthu odwala matenda a khansa. Amai ambiri
sakupeza mwai woti ayesedwe ndi kudziwa ngati ali ndi khansa wa bere chifukwa
chosowa zipangizo zoyenerera. Amai osowa thandizo lotere akuyenera kulipira
ndalama zambiri m’zipatala za pulaiveti. M’mene zinthu zilili panopa, tikupempha
Boma kuti lisonyeze utsogoleri pofuna kuthetsa mavuto amenewa m’maunduna ndi
m’magawo ena osiyanasiyana amene akulephera kukwaniritsa udindo ndi ntchito yao.
Papa Francis akutipempha kuti titsekule maso athu ndi kuzindikira mavuto amene ali
pakati pathu komanso zopweteka zomwe abale ndi alongo athu akukumana nazo
polephera kupeza thandizo losowekera pa umunthu wao ndipo ife tonse timvetsere
mwachifundo kudandaula kwao (Misericordiae Vultus, 15).
Tikukumbutsa Utsogoleri wa dziko lino kuti Amalawi ambiri osauka amadalira thandizo
ndi zipatala zomwe zimagwira ntchito ndi ndalama za Boma. Motero, kuchepa kaya
kusowa kwa ndalama zikutanthauza kuti anthu oterewa akutchinjirizidwa kukhala ndi
mwai wolandira thandizo labwino pa nkhani ya maphunziro, umoyo, malimidwe,
madzi, pongofuna kutchulapo mathandizo ena ochepa. Izi zimalepheretsa munthu kuti
akwaniritse ufulu wake wa chitukuko ndinso mwai woti nzika zonse m’Malawi zikhale
ndi moyo wabwino. Mulingo wa ndondomeko za ntchito ndi mfundo za Boma
umadziwika poona m’mene Bomalo likupititsira patsogolo, kuteteza ndi kuthandiza
aliyense kuti akhale ndi moyo woyenerera pa umunthu wake, makamaka moyo wa
anthu osauka ndi ovutikitsitsa.
2.4 Malipiro Ochepa
Tikumvetsa kuti kuimitsa kwa thandizo lochokera ku maiko akunja ndi chinthu
chimodzi chomwe chachititsa kuti zinthu zilowe pansi m’dziko lino. Komabe apa
pasakhale pozembera pa zimene zikuchititsa kuti Amalawi ambiri apitirire kuvutika
m’matawuni ndi m’madera akumidzi omwe. Ngakhale kuti tikadasowabe thandizo
kuchokera ku maiko akunja, ife tikuganiza kuti palibe wina angatitukulire dziko lino
kupatula ife eni Amalawi tonse pogwira ntchito molimbika zomwe zingachititse kuti
chuma chotolera m’dziko lomwe lino chithandize kuti zinthu ziyende bwino. Chimene
ife ngati Amalawi tingathe kukwaniritsa, ndi thandizo kaya popanda thandizo
lochokera kunja, ndi kuonetsetsa kuti tikugwira ntchito mwakhama kuti tipeze ndalama
zokwanira m’dziko lomwe lino ndipo kuti Boma ligwiritse bwino ntchito ndalamazi
makamaka poganizira ubwino wa munthu aliyense.
M’mene zinthu zililimu, tawumirizidwa kuti tifotokozepo kuti Amalawi timvetsetse za
kusoweka kwake koti tonse tithandize Boma lathu kudzera m’misonkho yomwe
tiyenera kupereka. Komabe ngakhale tanena izi, ife tikuganiza kuti Boma silidayike
ndondomeko zokwanira kuti dziko lathu lizitha kutolera chuma chosowekera kuti
zinthu ziyende. Izi zimachititsa kuti anthu ena ndi mabungwe kapena kampani zina
zizembe osalipira msonkho womwe ukadathandiza dziko kuti zosoweka za anthu
zipezeke. Nkofunika kuti Bungwe Lotolera Msonkho (Malawi Revenue Authority)
10
lithandizidwe kukhala ndi zoyenereza kuti likwaniritse udindo wake mwaukadaulo.
Tikupemphanso nzika zonse za m’Malawi muno kuti tizipereka msonkho wathu ngati
chizindikiro chakuti timalikonda dziko lathu lino.
Polankhulapo pa za chuma chomwe timapeza m’dziko, takumbukira mau omwe Papa
Leo XIII adaanena akuti: “Dziko limatukuka ndi kupita patsogolo kudzera…misonkho
ya chilungamo imene anthu amayenera kupereka. Nzika zonse popanda kupatula,
ziyenera kusonkha kanthu kuti ubwino wa anthu onse ukwaniritsidwe ngakhale kuti
onse sangapereke msonkho mofanana. Pa chifukwa ichi, chilungamo chimalola kuti
Boma lionetsetse ndi kutolera msonkho kwa onse amene akugwira ntchito. Ndi njira
yokhayi imene imathandiza kuti ngakhale anthu amene sali pa ntchito apeze nao
phindu pa chuma m’dziko popeza nawonso amathandiza kuti dziko likhale ndi chuma
(Rerum Novarum, 34).
2.5 Kusakaza Chuma cha Dziko
Maphunzitso a Mpingo wa Katolika amafotokoza momveka bwino ndithu kuti ngati
anthu tifuna kukwaniritsa ubwino wa munthu aliyense (Common Good), tikuyenera
kugwiritsa bwino ntchito zinthu zapansi pano ngati akapitawo. Izi zikutanthauza kuti
aliyense akuyenera kuzindikira cholinga cha zinthu zimene Mulungu adatilengera
m’dziko lino la pansi. “Aliyense ali ndi ufulu wodyerera zinthu zomuyenerera m’moyo
wake pokwaniritsa mfundo ya Ubwino wa Munthu Aliyense” (CSDC, 167). Nchifukwa
chake ife tikufuna kukumbutsa Amalawi onse kuti, angakhale chuma cha dziko lathuli
chitachuluka chotani, zinthu sizingapite patsogolo ngati chumacho chikungosakazidwa
mosasamala. Ife ndife okhudzidwa mokhumudwa ndi malipoti omwe akumveka akuti
akuyamba kusakaza chuma cha dziko mosaganizira bwino ndi akuluakulu a Boma ndi
a maudindo osiyanasiyana. Ngakhale zikunenedwa kuti tonse tigwiritse ntchito
mosamala chuma cha dziko lino, tikuona kuti a maudindo akuchulukitsabe maulendo
osowa ndalama zambiri ndipo akuyenda ndi chigulu cha anthu ambirimbiri.
Tikuonanso kuti kugulira magalimoto odula kwambiri Nduna za Boma, aku Nyumba ya
Malamulo, aku Makhothi, ndi akuluakulu ena, sichinthu chimene chinayenera kuchitika
nthawi inoyi pamene dziko lathu likunzunzika chifukwa cha vuto losowa chuma.
Kusakaza chuma cha dziko mwa njira imeneyi nkulakwira anthu ambirimbiri osauka
m’Malawi muno.
Komanso, ndife odandaula kwambiri, kuti pamene chuma ndi chosakwanira kuti nzika
zonse zilandire thandizo losiyanasiyana kudzera m’Maunduna a Boma ambiri,
ndalama zambiri zikusakazidwa pa zinthu zosafunikira kwenikweni. Palibe uyo
anganene kuti nkulondola kumakonza maphwando pogwiritsa ntchito chuma cha
Boma pongofuna kukondwerera kuti bajeti yavomerezedwa ndi Parliamenti. Zinthu
zosaganizira mavuto a anthu ena ngati izi makamaka pamene anthu ambiri m’dziko
lino ngosauka kodetsa nkhawa zimapangitsa kuti anthu akhumudwe ndipo kuti amve
ululu mumtima. Tikukumbunsanso Boma ndi Amalawi tonse kuti tiyenera kumagwiritsa
ntchito ndalama osapitirira mulingo wa zomwe tili nazo.
11
“Mulungu adapereka dziko lapansi kwa mtundu wonse wa anthu kuti aliyense athe
kukhala ndi moyo wabwino, mosakondera kapena kupatula wina aliyense” (CSDC,
171). Nthawi yafika yakuti kulira kwa anthu ovutika ndi osauka m’dziko lathu lino,
kukhalenso kulira kwa munthu wina aliyense ndipo pamodzi tonse tithetse zonse
zomwe zimatichititsa kuti tikhale odzikonda ndi achiphamaso (Misericordiae Vultus,
15).
2.6 Mulingo Wosalondola Pa Za Chuma
Ndifenso okhudzidwa poona kuti momwe Boma limafotokozera m’mene chuma
chikuyendera m’dziko lino sizigwirizana ndi m’mene zinthu ziliri pa moyo wa tsiku ndi
tsiku wa Amalawi ambiri. Pamene Boma likupitiriza kunena kuti chuma cha dziko lino
chagwira mseu, zooneka tsiku ndi tsiku zikusonyeza kuti nzika zambiri m’Malawi muno
zili m’mavuto aakulu zedi. Ife tikuganiza kuti tingathe kunena kuti chuma m’dziko
chikuyenda bwino pokhapokha ngati moyo wa anthu ambiri ndi ku midzi komwe uli
wotukuka ndi wotha kupeza mosavuta zosowa zao. Chuma cha dziko chithandize
anthu onse osati owerengeka okha. Mulingo wosonyeza kuti chuma m’dziko chikupita
patsogolo ukuyenera kukhala m’mene miyoyo ya anthu yatukukira ndi kupitira
patsogolo. M’mene moyo wa anthu uliri ndiye mulingo woona wa m’mene chuma
chikuyendera m’dziko. Pachifukwa ichi, tikupempha Boma lathu kuti lizinena zoona
pokamba za m’mene chuma chikuyendera m’dziko lino kuti tonse pamodzi
tithandizane kupeza njira zothetsera vutoli. Ndondomeko za chuma cha dziko
zikuyenera kuteteza moyo ndi maufulu a munthu aliyense ndi kuonetsetsa kuti moyo
wa anthu onse ukutukuka.
2.7 Kukana Kusankhana Pa Chuma Cha Dziko
Poona kusiyana kwakukulu komwe kulipo pakati pa anthu osauka ndi olemera m’dziko
lino, tikukumbukira za nkhnai ya Chiweruzo Chomaliza (Mateo 25:31-46) yomwe
imatiphunzitsa kuti tiziika patsogolo ndi kuganizira poyamba zosowa za anthu osauka
ndi ovutika. Masiku ano, anthu ambiri m’dziko lino ndi amphawi amene moyo wao
susonyeza konse ulemelero umene anthu amayenera kukhala nawo ngati ana a
Mulungu. Moyo wao nthawi zonse ndi wovutikira ndipo amayenera kuchita matatalazi
kuti apitirizebe kukhala ndi moyo. Ndi zoziziritsa thupi kuzindikira kuti ngakhale
m’dziko muno muli vuto la za chuma, alipo anthu ena momwe muno amene
akusangalalira zipatso za chitukuko chifukwa ali ndi zonse ngakhalenso zosefukira pa
zosowekera za moyo wao (Kukhala Moyo Mchikhulupiriro Chathu, p. 2).
Chodabwitsanso china ndi chakuti, anthu ochepawa amene ali ndi zonse zowasowa
pa moyo wao, ndi omwewonso amene amakonza ndondomeko zoyendetsera chuma
cha dziko zomwe zingathe kutukula moyo wa anthu osauka kapena kupitiriza
kuwapondereza.
Pozindikira kusowa kwa chilungamo kotereku, tili ndi udindo waukulu kwa anthu
osauka amene sangapeze zosowa pa moyo wao. M’buku lake lotchedwa Evangelii
12
Gaudium, Papa Francis akutipempha tonse kuti tikane ndi kunenetsa kuti ai pa nkhani
ya chuma chopatulana kapena chokhalira anthu ochepa okha (53-54). Tikane kukhala
akapolo opembedza chuma (55-56), tikane kulamulidwa ndi chuma m’malo moti
chumacho chititumikire (57-58) ndipo tikane kusankhulana pa chuma kumene
kumabweretsa nthawi zambiri zipolowe (50-60). Pofuna kukonzanso ndondomeko
zoyendetsera chuma cha dziko, lamulo lofunikira kuligwiritsa ntchito ndi lakuti, ikhale
ndondomeko yothandiza anthu osauka ndi ovutika imene idzachititsa kuti anthu
olemera athandize anthu osauka osati osauka kupitiriza kulemeretsa olemera kale (cf.
Gaudium Evangelii, 58). Kuchepa kwa kusiyana pakati pa anthu olemera ndi osauka
ndiye mulingo woyenera wosonyeza kuti chuma chikuyenda bwino m’dziko.
Tidaanenanso m’mbuyomu kuti “kukhulupirika, ubwino, kudzilemekeza, mwai
woperekedwa kwa onse: ndi ngodya zomwe zingathe kuunikira fuko lathu pamene
likutukuka ndi kupita patsogolo” (Kukhala Moyo Mchikhulupiriro Chathu, p. 3).
Tikufuna kubwerezanso kuti poona anthu olemera kwambiri komanso osaukitsitsa
pakati pathu funso loyenera kumadzifunsa ndi lakuti: kodi anthu osaukitsitsawa,
amatha bwanji kukhala moyo?
2.8 Kudzitsutsa
Masiku apitawa, tadabwa kumva kangapo zimene zikuchitika zoti lero Boma litha
kunena mfundo mkulengezedwa pa wailesi, TV ndi m’manyuzi koma posapita nthawi
wina wa m’Boma lomwelo nkulengeza zina zotsutsana. Izi zitha kuchititsa kuti anthu
ayambe kukayika ndi kusiya kukhulupirira Boma lao. Pamene zinthu zikuoneka ngati
kuti Boma lilibe mfundo yeniyeni pa nkhani ina yokhudza dziko, anthu amayamba
kudzifunsa kuti kodi Boma limeneli likudziwa zomwe likufuna kuchita! Pali zitsanzo
zambiri zomwe tingapereke pa nkhaniyi koma chifukwa cha nthawi tingotchulapo ziwiri
zokha: anthu akudabwa pa kusintha kwa maganizo kwa Boma pa nkhani yolemba
ntchito adokotala ndi anesi komanso pa nkhani ya billo yokhudza Mwai Wodziwa
Zimene Zikuchitika (Access to Information Bill). Tikupempha Boma kuti lisonyeze kuti
ndi ilo limene likutsogolera dziko lino ndipo litsimikizire anthu kuti likudziwa komwe
tikupita.
2.9 Kulowa Pansi Kwa Maphunziro
Tidaafotokozanso kambirimbiri m’mbuyomu kuti maphunziro akunka napitilira kulowa
pansi m’sukulu zathu za primary, sekondale ngakhalenso ku makoleji. Kusowa kwa
zipinda zophunziriramo ndinso kuchuluka kwa ana m’kalasi imodzi kuphatikizapo
mavuto ena monga, kusowa kwa zida zophunzitsira, kuchepa kwa aphunzitsi, sukulu
zowonongeka, nyumba zosungira mabuku zotsala pang’ono kugwa ndi laboratore
zosowa zida, etc. ndi zizindikiro zina zosonyeza kuti maphunziro alowadi pansi.
Tikufuna kutsindika kuti palibe dziko limene lingatukuke popanda kuikira mtima ndi
chuma pa nkhani ya maphunziro.
13
Poyang’anira tanena pamwambazi, ife ndife okhudzidwa ndi zotsatira zomwe
zingadze chifukwa chothetsa mayeso a Standade 8 ndi a Formu 2. Tikadakonda anthu
ambiri akadafunsidwa maganizo awo pa nkhani imeneyi chigamulo
chisanaperekedwe. Izi zikadathandiza kuchotsa nkhawa zimene ena ali nazo zoti
mwina Boma lidathetsa mayeso a Standade 8 ndi Formu 2 pongofuna kuchepetsa
ndalama zimene zimasoweka ku Unduna wa Maphunziro mosaganizira kuti potero,
maphunziro atha kulowa pansi. Pamene tikuthokoza chifukwa cha thandizo lomwe
sukulu za Mipingo zimalandira (pulaimale ndi sekondale), tikupempha Boma kuti
lisonyeze chidwi choposa apa pothandiza kukonzanso ndi kukulitsa sukulu za
sekondale ngati tikufuna kuti dziko lathu lidzakhale ndi achinyamata amene “adzathe
kukwaniritsa zomwe amafuna kukhala mosavuta” (CSDC, 164).
2.10 Njala Yosatha
M’zaka zotsatana zapitazi, m’dziko lathu lino mwakhala muli njala chifukwa cha
kusefukira kwa madzi komanso chifukwa cha ng’amba yomwe idaononga mbeu
m’madera ena. Boma lidachita chotheka pa vutoli polengeza kuti anthu okhudzidwa
ndi madzi osefukirawa athandizidwe. Tikuyamika mabungwe ndi magulu ena amene
adagwirana manja ndi Boma kuonetsetsa kuti munthu wina aliyense asafe ndi njala
m’nyengo imeneyi. Takondwanso kumva kuti Boma lakhazikitsa pulani ya ishuransi
yothandiza pa ngozi zochitika chifukwa cha madzi osefukira. Komabe ndife
okhudzidwa ndi kusowa kwa chimanga m’dziko muno masiku ano. Kusowa kwa
chimangaku kwachititsa kuti anthu opitilira 2.8 million avutike ndi njala chaka chino
ndipo zotsatira zake ndi kunzunzika ndi imfa popanda chiyembekezo china
chilichonse. Anthu akukhala nthawi yayitali pa mizere akudikilira kuti mwina nkugula
chimanga ku misika ya ADMARC zomwe zikuchititsa kuti alephere kugwira ntchito
mokwanira yosamalira minda yao. Izi ndi zachidziwikireni kuti polephera kusamala
minda yao nthawi yolima ino, anthu amenewa sadzakololanso chakudya chokwanira
m’chaka chimenechi.
Tikudandaulanso chifukwa cha zomwe tamva kuti azimai pamodzi ndi ana ao akugona
ku misika ya ADMARC ndi chiyembekezo chakuti mwina nkugulako chimanga pa tsiku
lotsatira. Tikuona zimenezi ngati zinthu zochotsa ulemelero wa umunthu wa amai
ndipo ndi zinthu zosavomerezeka. Kupatula kusowa kwa chimanga, kuli malipoti
onena kuti pali madilu akatangale amene akuchitika pakati pa ena ogwira ntchito ku
ADMARC ndi anthu ena amabizinezi omwe akugulitsana chimanga chambiri kenaka
nkumakachigulitsa pa mtengo wokwera kwambiri. Siumunthu kuti wina adzilemeretse
potengera tsoka la Amalawi osauka. Kuposera apa, chokhumudwitsa china ndi chakuti
timamva ena akunena kuti chimanga chilipo m’dziko muno chikhalireni mukapita ku
misika yambiri ya ADMARC chimapezeka mwa apo ndi apo. Poona m’mene zinthu
zilirimu, tikupempha Mabungwe a Boma monga ADMARC kuti afikitse chimanga
chimene chilipo ku misika yimene anthu angathe kufikako. Ufulu wokhala ndi
chakudya umakhalira aliyense. Pa nthawi ngati ino, mwina titha kugwa m’chinyengo
14
kuti titseke maso athu osafuna kuona ndi kuzindikira udindo wathu kwa anthu ovutika.
Tikupempha Akatolika ndi anthu onse akufuna kwabwino kuti aonetse umodzi wao ndi
anthu onse amene akuvutika ndi njala. Tonsefe tikupemphedwa kuti tikhale ndi mtima
wosamalira abale athu (Genesis 4:9). Monga Yohane Paulo II Woyera adaanenera,
tikachita zimenezi tisonyeza “chitsimikizo cholimba ndi chopilira pa kudzipereka
kwathu ku ubwino wa munthu aliyense; kutanthauza ubwino wa onse ndi munthu
aliyense chifukwa tonsefe ndife oyenera kusamalira abale athu onse” (Solicitudo Rei
Socialis, 38).
Zonse tanena pamwambazi ndi zongothandiza pakanthawi chabe, basi. Tikusowa
tipeze njira zokhalitsa zosinthira Malawi kukhala dziko lodzidalira pa nkhani ya
chakudya. Ife tikuganiza kuti Malawi ndi dziko lomwe lidadalitsika ndi zinthu zambiri
zomwe titazigwiritsa bwino ntchito, njala itha kudzakhala mbiri yakale. Madzi abwino
ndi nthaka ya chonde zomwe zikungokhala ndi chuma chomwe mwina
sitikuchigwiritsa bwino ntchito mopindula. Sitisowa kukumbutsa Atsogoleri athu ndi
nzika zonse za m’dziko muno kuti Malawi ndi dziko limene limadalira ulimi. Tiyeni
titsatire malangizo a Paulo Mpostoli onena kuti: “Munthu wosafuna kugwira ntchito,
kudyanso asadye” (2 Atesalonika 3:10).
Pa nkhani ya feteleza wa makuponi, tikupempha Boma kuti likonzenso ndi kukometsa
ndondomekoyi kapena lipeze njira m’mene lingasiyire kugawa makuponiwa.
Choyenera kudziwa ndi chakuti, kaya Boma lipeza njira yotani pa nkhaniyi, liyenera
kuganizira ubwino wa anthu osauka m’mapulani ake. Kuti dziko lino lizikhala ndi
chakudya chokwanira nthawi zonse, tikuganiza kuti yakwana nthawi yoti Boma liyike
chuma chambiri ndi kukhazikitsa ulimi wothilira ngati bizinezi. Izi zidzathandiza
Amalawi ambiri kuti azidzalima ndi kukolola kawiri pa chaka. Iyi ndi njira yokhayo
yomwe tikuganiza kuti ingathandize dziko la Malawi kukhala lodzidalira pa nkhani ya
chakudya.
Tikadalankhulabe nkhani ya ulimiyi, ife ndife okhudzidwa ndi malipoti otsutsana
okhudza kusowa kwa matrakitala ndi makina otonolera chimanga zomwe Boma
lidaagula pofuna kupititsa patsogolo ntchito za ulimi m’dziko lino. Tikupempha Boma
kuti lifufuze bwino za nkhaniyi. Tikukhulupirira kuti nkulakwa komanso sichilungamo
kuti Amalawi osauka ndiye adzalipire ngongole ya katundu ameneyu chikhalirenicho
palibe chimene adapindulapo ndi matrakitala ndi makina otonolera chimangawo.
Potsiriza, tikupempha akatswiri athu pa nkhani ya malimidwe ndi ulimi wothilira kuti
akonze mfundo ndi ndondomeko zomwe zingathandize dziko lino kukhala lodzidalira
pa chakudya. Tafuna kubwerezanso kunena kuti, ndondomeko ndi zochita zonse za
Boma, mulingo wake uyenera kukhala ulemelero wa munthu, makamaka anthu
osauka ndi oponderezedwa. Izi zidzakhala chitsimikizo cha kudzipereka kwa Boma
poganizira anthu osauka ndi oponderezedwa (Mateo 25:31-46).
15
2.11 Chilungamo ndi Chifundo Chosasankha Kwa Onse
Zotsatira za kuba kwa ndalama za Boma kodziwika ndi dzina loti Kashigeti zakhudza
moyo wa Amalawi ambiri mpaka tsopano lino. Zofunikira za anthu monga sukulu ndi
zipatala zikuvutika kwambiri chifukwa cha Kashigeti. Amalawi tonse tikuyembekezera
kuti Boma lifufuza bwino pa nkhaniyi ndipo okhudzidwa ndi nkhaniyi azengedwe
mulandu ngati pali umboni wokwanira. Anthu m’Malawi muno akuyembekezera kuti
Boma litenga nkhaniyi ngati yayikulu yosoweka kuyitsata bwino poganizira zotsatira za
kubaku komwe kwachititsa Amalawi ambiri osauka kuti azikhala ndi moyo wovutika.
Apa tinene kuti ndi chinthu cholimbitsa mtima kuona kuti anthu ena okhudzidwa ndi
nkhani ya Kashigetiyi akuzengedwa mulandu m’makhothi ndipo chiweruzo
chikuperekedwanso poyang’anira malamulo a dziko lino. Komabe, ndi bwino kunena
pano kuti anthu ambiri akusonyeza kukhumudwa pakumva za chilango chimene
chikuperekedwa kwa olakwawo. Ambiri akukhulupirira kuti malamulo okhudza nkhani
za mtundu umenewu ngwofunika kuwaunikanso poyang’anira kukula kwa nkhaniyi ndi
zotsatira zake ku dziko ndi nzika zonse.
Tafuna kudziwitsa Boma kuti Amalawi akuyembekeza zambiri kuposa zimene
zachitika pa nkhani imeneyi. Tikuda nkhawa ndi mchitidwe wina wa Boma womazenga
mulandu wa munthu kudzera m’njira zofalitsira nkhani. Tikupempha Boma kudzera
m’mabungwe ake ozenga milandu (Bungwe Lothetsa Katangale ndi Ziphuphu – ACB,
Ofesi ya Woona Za Milandu – DPP) kuti lifufuze ndi kuzenga milandu onse amene
akuganiridwa ngati pali umboni wokwanira. Tikupemphanso Boma kuti lionetsetse kuti
magulu ozenga milanduwa akuchita zimenezi momasuka ndi mwaufulu mopanda wina
kulowerera m’ntchito yao. Tikupemphanso mabungwe onse ofufuza ndi kuzenga
milandu kuti afulumire kufufuza nkhanizi mwaukadaulo ndi mopanda tsankho.
Tikufuna kukumbutsa Boma kuti pa nkhani yolamulira, chithunzi cha Boma chimene
anthu ali nacho m’maganizo ao ndi chofunikira kuchilabadira ngati zoona zenizeni.
Pachifukwa ichi, Boma lifufuze ndi kutsiriza nkhani ya K92 billion ndi ya K577 billion
imene owerengera ndalama adalephera kufotokozera bwino. Tikhulupirira kuti ubwino
wa dziko lonse ukuyenera kukhala patsogolo pa ubwino wa wina aliyense angakhale
wandale. Onse okhudzidwa ndi nkhaniyi amangidwe ndi kuzengedwa mulandu
chifukwa “Chifundo sichitsutsana ndi chilungamo koma m’malo mwake chimathandiza
munthu kuti azindikire Mulungu amene amafuna kufikira wochimwayo ndi kumpatsa
mwai woti adziunike, atembenuke mtima ndi kukhulupirira” (Misericordiae Vultus, 21).
2.12 Akatswiri Osagwiritsidwa Ntchito: Adokotala, Anesi ndi Aphunzitsi
Posunga ndi kutsata kuti malamulo a chilungamo ndi opereka mwai kwa wina aliyense
akutsatidwa, “Boma likuyenera kuonetsetsa kuti mwai woti munthu atha kupeza
ntchito yomuyenerera malingana ndi kuthekera kwake ulipo m’dziko” (Pacem in Terris,
64). Ngakhale ndizomveka kuti Boma silingathe kulemba ntchito anthu onse m’dziko,
komabe tikuona kuti nkuwononga ndalama kulipirira maphunziro a adokotala, anesi
16
ndi aphunzitsi amene Boma silingathe kuwalemba ntchito chikhalireni m’dziko muno
muli vuto lilikulu lakusowa kwa anthu ngati amenewa. Izi tikuziona ngati kuti Boma
likungolipirira anthu kuti akhale ndi luntha lomwe akukagwiritsa ntchito ku maiko ena
osati m’dziko lao lomwe lino. Pachifukwa ichi, Amalawi ambiri osauka akulephera
kukhala ndi mwai wolandira thandizo kuchokera kwa akatswiri omwe Boma
lidawaphunzitsa.
2.13 Chitetezo M’dziko
Kuperewera kwa chitetezo ndi vuto lomvetsa chisoni limene ladzetsa chiopsezo
m’dziko lathu lino masiku ano. Miyoyo ya anthu komanso amabizinezi ndi anthu
akumidzi omwe ali pa chiopsezo chosowa chitetezo tsiku ndi tsiku. Chodetsa nkhawa
kwambiri ndi chakuti, nthawi zina amene amaopseza anthu ndi apolisi ena amene
amagwirizana ndi mbava nkumavutitsa anthu m’malo mosungitsa malamulo, bata ndi
mtendere.
Tikufuna kudzudzulanso mchitidwe wolanga anthu olakwa m’madera ndi ku midzi
kwathu pakuwanzunza ndi kuwapha m’malo moti atsate zimene malamulo amanena.
Tikuda nkhawa kuti mkhalidwe woterewu utha kupereka mantha kwa anthu
makamaka akunja amene akadakonda kudzagwira ntchito za chitukuko m’dziko muno.
Mchitidwe wotere utha kubwezera m’mbuyo zimene Boma lakhala likuchita potsekula
makomo a dziko lathu kwa anthu akunja aphindu ngati njira yabwino yobweretsa
chitukuko.
Takhudzidwa mwachisoni kwambiri ndi malipoti amene tikumva kuti anthu achi albino
akuphedwa m’dziko lathu lino. Tikufuna kubwerezanso kunena mwamphamvu kuti,
anthu achi albino ndi anthu monga wina aliyense ndipo ngwoyenera kulemekezedwa
ndi kutetezedwa ndi ife tonse m’madera athu.
Papa Leo XIII adanena kuti, “ndi ubwino wa anthu onse komanso wa munthu wina
aliyense kuti mtendere ndi bata zikhalepo pakati pathu” (Rerum Novarum, 36).
Pachifukwa ichi, tikupempha nzika zonse m’dziko lino ndi anthu onse akufuna
kwabwino kuti tigwire ntchito pamodzi ndi Boma pofuna kuti dziko lathuli likhale la
mtendere ndi bata.
2.14 Kusankhana Mitundu ndi Zigawo
Ngakhale kuti takwanitsa kuchita zambiri pofuna kuti m’dziko muno mukhale
demokalase, ife tikuda nkhawa chifukwa pakuoneka kuti anthufe titha kugawikana.
Mkhalidwe wosankhana mitundu kapena zigao zimene wina akuchokera ukukhala
ngati wayamba kuzika mizu pakati pathu. Izi zimaonekera poyera mwanjira
zosiyanasiyana monga kusankhana pa nkhani ya ndale, chuma ndipo kusapezeka
kwa mwai wofanana kwa anthu a mitundu ndi zigawo zosiyanasiyana. Ganizo
lobweretsanso Fedeleshoni ndi limodzi mwa chizindikiro cha kugawikanaku.
Tikukumbutsa nzika zonse kuti makolo athu amene adakhazikitsa Fuko la Malawi,
17
adachita chotheka kuthandiza Amalawi onse kuti azionana ngati abale. “Umodzi” ndi
ngodya imene ili maziko a dziko lino. Izi ndi zogwirizana ndi kufuna kwa Mulungu
Mlengi wathu amen amafuna kuti tizikhalira pamodzi ndi molemekezana.
Tonse tikuitanidwa kuti tinyadire mtundu wathu ndi kukondana wina ndi mzake ngati
ana a Mulungu. Palibe mtundu umene ndi wa mtengo wapatali kuposa unzake.
Kusankhana mitundu kaya zigao zimene anthu amachokera ndiponso kugawikana
kwina kuli konse chifukwa cha chuma kaya ndale ndi zotsutsana ndi kuitanidwa
kwathu ku choonadi (cf. Kukhala Moyo M’chikhulupiriro, p. 2-3). Tonse ndife banja
limodzi la anthu, posayang’anira chigao, mtundu, ndale, chipembedzo ngakhale
kusiyana kwa maganizo. Ngati nzika za dziko lino, tili ndi udindo wonena ndi wochita
zinthu zoluzanitsa ndi kuyanjanitsa anthu komanso zinthu zopititsa patsogolo kukhalira
pamodzi mwamtendere (cf. Kulimbikitsa Masomphenya a Dziko Lathu, p. 14).
Ngati Abusa anu, tikupempha nzika zonse za dziko lino kuti tiziika Malawi dziko lathu
patsogolo osati zokomera mtundu kapena chigao chathu. Tikupemphanso Akatolika
ndi anthu ena onse akufuna kwabwino kuti tizikondwerera pozindikira kuti tonse
chiyambi chathu komanso komwe tikupita ndi kumodzi. Pa chifukwa ichi, nkofunika
kuti tizilemekezana, kukhalira pamodzi mwa chilungamo ndi mwa chikondi ndi onse
amene sitili nao m’chipembedzo chimodzi kapenanso amene zokonda zao ndi
zosiyana ndi zathu. Tiyeni titsate malangizo a Paulo Woyera Mpostoli amene amati:
“Muziyesetsa kusunga umodzi mwa Mzimu Woyera pa kulunzana mu mtendere ngati
thupi limodzi ndi Mzimu Woyera mmodzi monganso pali chiyembekezo chimodzi,
Mbuye mmodzi, chikhulupiriro chimodzi, ubatizo umodzi ndi Mulungu mmodzi amene
ali Atate a anthu onse. Iye ali pamwamba pa onse, amagwira ntchito kudzera mwa
onse ndipo ali mwa onse” (Aefeso 4: 3-6).
Potsiriza, tikupempha Boma kuti likonze mfundo ndi ndondomeko zothandiza kuti
pasakhale magulu ena pakati pathu amene akuiwalidwa. Tikupemphanso Zipani
zonse Zandale, Ogwira Ntchito m’Mabungwe, Mafumu ndi Atolankhani kuti apewe
kulemba kaya kufalitsa nkhani zodzetsa udani pakati pa Amalawi amene ndi anthu
okonda mtendere. Ofalitsa nkhani asamale poonetsetsa kuti nkhani kapena
mauthenga ao ndi oona osati odzetsa kugawikana. Amalawi ambiri amadalira ofalitsa
kuti apeze msangulutso ndi kudziwa zochitika za chitukuko m’dziko. Pa chifukwa ichi,
kugwiritsa ntchito mau otha kugawa ndi kunyoza anthu komanso mauthenga otha
kuyambitsa zipolowe ndi chinthu chosavomerezeka m’dziko la demokalase momwe
mumayenera kukhala maganizo osiyanasiyana. Tiyeni tilole kuti Mau a Mulungu,
Maphunzitso a Mpingo komanso Makhalidwe Ovomerezeka a Atolankhani aunikire
ntchito zonse zofalitsa nkhani ndi mauthenga pofuna kudziwitsa Amalawi kuti adziwe
zoona zenizeni nthawi zonse (cf. Kulimbikitsa Masomphenya a Dziko Lathu, p. 16).
18
2.15 Mkangano Pakati pa Aphungu ndi Makhansala
Ndife okondwa kuti pa 20 May 2014, tidachita chisankho cha makhansala kuti
athandize kuyendetsa chitukuko cha m’dziko lino. Koma tazindikira mwachisoni kuti
pali mkangano, kukayikirana komanso kukokanakokana pakati pa atsogoleri athu
oyendetsa Maboma Ang’ono. Tikukhulupirira kuti ngati vuto limeneli silithetsedwa,
kufunika kwa ulamuliro wa maboma ang’ono kukhala kopanda tanthauzo. Izi zitha
kuchititsa kuti ntchito za chitukuko cha dziko ndi nzika zonse zisapindulepo pa
ndondomeko yoyendetsera Boma imeneyi. Motero, tikupempha Makhansala, Aphungu
aku Nyumba ya Malamulo, Ogwira ntchito ku Khonsolo ndi Mafumu kuti aphunzire
kugwira ntchito limodzi molemekeza udindo wa wina aliyense komanso mozindikira
kuti onse ndi oyenera kukhala odalirana.
Tikupempha mbali zonse zokhudzidwa ndi nkhaniyi kuti ziunikiridwe ndi mfundo ya
kupereka mwai kwa aliyense kuti akwaniritse zomwe angathe poyang’anira udindo
wake. “Monga tikudziwa kuti nkulakwa kwambiri kuwachitira zinthu anthu ena zimene
iwo eni angathe kuchita ndi kukwanitsa mwa iwo okha, chonchonso nkulakwa
kwambiri komanso kusokoneza ufulu wa ena kuti mabungwe kapena magulu ena
amphamvu alande ndi kuchitira ntchito magulu kapena mabungwe amene kuthekera
kwao ndi kochepera” (CSDC, 186). Choncho, ndi bwino kuti magulu kaya mabungwe
atenge udindo pa zinthu zothandiza ubwino wa moyo wao womwe ndipo magulu
kapena mabungwe amene ali ndi kuthekera koposa ngati Boma, asalowerere
m’zintchito ngati zimenezi.
2.16 Utsogoleri Wotha Kusintha Zinthu
Kwa nthawi yaitali Amalawi akhala akulakalaka dziko lathu titakhala ndi atsogoleri
osinthika komanso otha kusintha zinthu m’magawo onse a Boma. Chiyembekezo cha
anthu ndi chakuti, dziko la Malawi likusowa atsogoleri oterewa kuti lithe kusintha ndi
kutukuka pa nkhani ya za chuma, moyo wa ndale ndi poonetsetsa kuti zomuyenerera
munthu aliyense kuti akhale ndi moyo wabwino zikupezeka. Mulungu amafuna
utsogoleri wa masomphenya, wotha kusintha zinthu, wopereka mphamvu ku anthu,
wodziwa kusamalira, kuteteza ndi kutumikira nzika zonse, woganizira ubwino wa
anthu ndi wolemekeza ndi kumvera Iye ngati Mlengi wa zonse (cf. Kulimbikitsa
Masomphenya a Dziko Lathu, p. 10-11). Kuti mtsogoleri athe kusintha zinthu “ayenera
kukhala wokonzeka kuthandiza kuti zinthu zikhale zatsopano ndipo kusintha kwake
kukhale kwakuti zinthu zikusanduka zabwino koposa kale osangosintha chifukwa
chongofuna kusintha, ai (cf. Kulimbikitsa Masomphenya a Dziko Lathu, p. 15).
Mtsogoleri wotere ayenera kukhala ndi zomuyenereza ngati zotsatirazi: munthu wa
masomphenya, wodziwa kusamala zinthu za m’dziko, wa zitsanzo zabwino, wodziwa
ndi kulemekeza Malamulo a dziko, wochita zinthu mwapoyera, wolimbikitsa
demokalase ndiponso woopa Mulungu (cf. Kulimbikitsa Masomphenya a Dziko Lathu,
p. 14-15).
19
Ife tikuganiza kuti ndi utsogoleri wokhawo wotha kusintha zinthu umene ungathe
kuthandiza ogwira ntchito m’Boma ndi ntchito zina zotumikira anthu kuti akwaniritse
udindo wao mwaukadaulo. Chifukwa cha ubwino wa anthu ao, atsogoleri otere
amasiya njira zakale ndi zosathandiza zoyendetsera dziko ndi ndale ndi kubweretsa
zatsopano. Awa ndi atsogoleri amene mau ao amagwirizana ndi zochita zao.
Atsogoleri abwino ayenera kuyamba ndi iwo kupereka zitsanzo zabwino – “makamaka
podziwa ndi kukhazikitsa mwachimvekere zimene akufuna kukwaniritsa zomwe
ziyenera kukhala zotheka komanso zogwirizana ndi zimene nzika za m’dziko
zimafuna, kuyembekeza ndi kulakalaka m’moyo wao” (cf. Kulimbikitsa Masomphenya
a Dziko Lathu, p. 14).
Choncho, tikupempha Boma, Zipani za Ndale, Mabungwe a Ogwira Ntchito, Mipingo
yosiyanasiyana ndi Mafumu kuti onse achite chotheka kukhala atsogoleri otha
kusintha zinthu m’maudindo awo otumikira anthu (cf. Kusankha Atsogoleri athu, p. 3-
6; Tsogolo Lathu Liri M’manja Mwathu: Ulendo wa Kuchisankho cha 2009, p. 7-8;
Kulimbikitsa Masomphenya a Dziko Lathu, p. 15). Atsogoleri onse ndi ku malo konse
kumene ali akuyenera kukhala achilungamo, okhulupirika, osakondera ndiponso
onena zoona komanso a mbiri yabwino ndi yolemekezeka.
Ife, Apiskopi Akatolika, tikukhulupirira kuti tafotokozazi ndi mtundu wa atsogoleri
amene angathe kuthandiza nzika zonse kuti zitenge nao mbali m’zochitika ndi
kukonda dziko lao. Ndi maganizo amenewa, ife tikulimbikitsa zimene Utsogoleri wa
masiku ano ukutipempha tonse kuti tikhale anthu okonda kugwira ntchito
modzipereka, odzilemekeza komanso okonda dziko lathu. Maiko amene adaali
osachita bwino adatha kusintha zinthu chifukwa chotsata mfundo tanena
pamwambazi. Choncho, ife tidzapitiriza kulalikira Amalawi onse monga takhala
tikuchitira m’mbuyomu kuti; “kutenga nao mbali pomanga Fuko lathu ndi udindo wa
nzika iliyonse m’Malawi muno” (cf. Kulimbikitsa Masomphenya a Dziko Lathu, p. 11).
Ngati Amalawi, tikusowa kuzindikiranso kufunika kwake kokonda dziko lathu ndi
kotenga nao mbali pa ntchito ya chitukuko. Palibe wina angatukule dziko la Malawi
koposera ife eni ake amene tili nzika za dziko lino. Izi zikusowa kuti tikhale anthu
odzilemekeza, okonda kugwira ntchito komanso okonda dziko lathu. Nkhani zosakaza
ndi kuba chuma cha Boma – Cashgate – komanso kukula kwa mkhalidwe wokonda
katangale pakati pathu ndi zizindikiro zoipa zosonyeza kuti sitilikonda mokwanira dziko
lathu.
M’Chaka ichi cha Jubile ya Chifundo, tikupempha mwapadera onse amene amachita
nawo za katangale kuti asinthe ndi kutembenuka mtima. Monga Papa Francis
akunenera; “Katangale amatilepheretsa kuti tione tsogolo lathu ndi chiyembekezo
chifukwa umbombo ndi kudzikonda udyo kotereku kumasokoneza zofuna ndi
zolakalaka za anthu ofooka ndipo kumapondereza anthu osaukitsitsa” (Misericordiae
Vultus, 19). Chaka Choyera cha Chifundochi ndi mwai wapadera kwa tonsefe kuti
tisinthe ndi kuyambanso moyo watsopano. Pamene tikuvutika m’dziko lathu lino
20
chifukwa cha zotsatira za katangale ndi zina za umbanda pakati pathu, ndi nthawi
yabwino kuti timvetsere kudandaula ndi kulira kwa anthu ambirimbiri osalakwa amene
alibe nkanthu komwe, salemekezedwa ndipo palibe uyo amamvetsera zofuna zao
kapena kusamala moyo wao. Zomwe aliyense mwa ife ayenera kuchita ndi kuvomera
kuti ndife osowa kutembenuka mtima ndi kudzipereka tokha mwa chilungamo
m’nyengo iyi ya chifundo imene Mpingo ukutipatsa (cf. Misericordiae Vultus, 19).
2.17 Kutsutsa Mozindikira ndi Mothandiza
Pambuyo pa zaka zoposa makumi awiri za ndale za demokalase, tikadaonabe kuti
udindo wa Zipani Zotsutsa umangoonekera poyera pamene Aphungu aku Nyumba ya
Malamulo akukumana. Kudzera m’mitsutso yokhudza nkhani za ku Nyumba ya
Malamulo, Komiti za Nyumbayi, Zipani za Ndale komanso Aphungu aku Nyumba ya
Malamulo amasonyeza kuti akufuna ndithu kuthandiza Boma ndi Maunduna ake onse
kuti akwaniritse bwino udindo wao. Komabe, tikuona kuti Zipani Zotsutsa zitha kuchita
bwino koposa m’mene zikuchitira pakali pano.
Poyamba, tikuyembekeza kuti Azipani Zotsutsa azigwira ntchito limodzi ndi Boma
polithandiza kupeza ndi kufotokoza njira zothetsera mavuto amene dziko lathu
likukumana nawo makamaka vuto la njala. Tikupempha Otsutsa, ngati Boma
loyembekezera, kuti azipereka fundo ndi njira zina zothetsera mavuto amene dziko
lathu likukumana nawo. Ndi pochita zimenezi pamene anthu angaone kuti Zipani
Zotsutsa zikusonyeza kuti zimakhudzidwa ndi mavuto amene nzika za dziko lino
zikukumana nawo. M’nyengo yovuta ngati imeneyi, kupereka njira zina zothandiza
Boma kuti zinthu zisinthe ndi njira yokhayonso imene ingalimbikitse chikhulupiriro cha
anthu mwa Zipani Zotsutsa.
Kachiwiri, tikuyembekeza Zipani Zotsutsa kuti zizichita kalondolondo wa m’mene
zinthu zikuyendera ndi kumabweretsa poyera maganizo a ndondomeko zina
zatsopano zosiyana ndi zongolankhula za ndale zimene zimangokhala zokoma
kuzimvera koma palibe china chilichonse chosintha chomwe chimaoneka pambuyo
polankhulaku. Kuti dziko lathu litukuke, tikusowa kuti Azipani Zotsutsa azifufuza bwino
ndi mozama ndondomeko ndi mapulani a Boma makamaka okhudza chitukuko cha
dziko lonse. Amalawi amayembekezera kuti atsogoleri amene adasankhidwa ngati
Aphungu ku Nyumba ya Malamulo, azikambirana zinthu zokhudza dziko lino
mwachikulu m’malo momangoteteza zipani zao.
Kachitatu, tikuyembekeza kuti demokalase izichitika ndi kuoneka poyera m’katinso
mwa Zipani Zotsutsa. Ndi udindo wathu kukumbutsa atsogoleri onse kuti “atsogoleri a
demokalase yeniyeni amayenera kufunsa ndi kumvetsera maganizo a ena ndipo
amayenera kupewa kudziwunjikira mphamvu ndi kulola ena kuti achite ntchito zina
m’malo mwa iwo eni komanso amayamika pamene wina wachita bwino” (cf.
Kulimbikitsa Masomphenya a Dziko Lathu, p. 15). Tikukhulupirira kuti demokalase
imayenera kuyambika mkatikati mwa zipani chifukwa ndi m’zipani momwemo m’mene
21
demokalase imatha kuyambanso kulephera kukwaniritsidwa. Demokalase ya m’zipani
itha kuthandiza kuti demokalase ya m’dziko lonse ikome ndi kukhwima koposa. Pa
chifukwa ichi, tikupempha Zipani zonse Zotsutsa zimene pakali pano pali
kukokanakokana mkati mwao kuti zisonyeze kwa Amalawi kuti zitha kuthetsa kusiyana
maganizo kwao mwa chichikulu. Kuyendetsa dziko ndi udindo wa tonse kuyambira
Chipani Cholamula, Zipani Zotsutsa komanso nzika zonse za m’dziko.
2.18 Kusamalira Chilengedwe
Ngati dziko lomwe likukumana ndi mavuto akudza chifukwa cha kuonongeka kwa
chilengedwe, tikufuna kupempha nzika zonse kuti tichitepo kanthu posamalira
chilengedwe chimene ndi mphatso yaulere yochokera kwa Mulungu. Madzi osefukira
komanso chilala chimene chatigwera zikhale zinthu zotikumbutsa kuti china chake
chidalakwika pa ubale wa ife anthu ndi chilengedwe. Maphunzitso a Mpingo wa
Katolika amatsindika kuti tiyenera kulemekeza Mulungu Mlengi wa zonse posamalira
bwino za chilengedwe. Chisamaliro cha chilengedwe sichiyenera kungochitika
panthawi yodzala mitengo monga Boma likatipempha, ai, koma kuzindikira kuti izi ndi
zimene chikhulupiriro chathu chimatipempha. Tikupemphedwa kuti titeteze anthu
komanso dziko lonse lapansi ndi kusonyeza chikhulupiriro chathu pokhala anthu
osamala chilengedwe cha Mulungu. Kuonongeka kwa chilengedwe ndi chinthu
chodetsa nkhawa chomwe sitingathe kungochisiya osachitapo kanthu.
Tikupempha Boma mwamphamvu ndithu kuti lionetsetse kuti tikugwiritsa bwino ntchito
nkhalango zathu m’dziko lino ndi kufufuza kuti kodi zomwe tapata kuchokera ku
nkhalango zimenezi zapindulira bwanji mtundu wa Amalawi?
Tikupempha magulu onse amu Mpingo wa Katolika ndi sukulu zonse za maphunziro
akuya kuti azikambirana ndi kumvetsetsa uthenga wa Papa Francis womwe adalemba
m’buku lake lotchedwa, Laudato si` momwe iye amatipempha kuti tizisamalira dziko
lapansi popeza dzikoli ndiye kwao kwa munthu aliyense. Uthenga wa Papawu ndi
wofunika kwambiri makamaka kwa ife amene takhudzidwa ndi mavuto omwe adza
chifukwa cha kuonongeka kwa chilengedwe.
Mau Otsiriza
Ife, Aepiskopi Akatolika, ngati Abusa, tikuzindikira mavuto amene anthu ambiri osauka
akukumana nao m’dziko lino. Tikupempha Boma kuti lisonyeze utsogoleri pothandiza
Fuko la Malawi kukhala lokonda kugwira ntchito, kudzidalira ndi kukhala ndi luso
lopanga zinthu zosiyanasiyana. Panthawi yovuta ngati yino, Boma liunikenso
m’chitidwe ndi mfundo zina kuti anthu tonse tisinthe makhalidwe ndi kaganizidwe
kathu kuti potero m’dziko muno mupezeke chakudya chokwanira aliyense, chitetezo
komanso chisamaliro cha chilengedwe kudzera m’maphunziro othandiza anthu
kugwiritsa ntchito njira zina zophikira ndi zinthu zina zofunikira kusintha m’dziko lathu
lino.
22
Tikupemphanso Amalawi onse akufuna kwabwino kuti tigwirizane m’cholinga cha
chitukuko cha dziko lathu chimene tikufuna kukwaniritsa pogwira ntchito limodzi ngati
Fuko. Kuti titukuke, Fuko la Amalawi likusowa anthu a umunthu, odzilemekeza amene
akudziwa zomwe akufuna komanso okonda dziko lao. Kuti izi zichitike, Boma
likuyenera kutsogolera pokhala oyamba kusonyeza zitsanzo zabwino. Boma
lionetsetsenso kuti nzika iliyonse ili ndi mwai wotha kuchita zimene ingathe malingana
ndi kuthekera kwake posayang’anira chipani cha ndale, potero tidzatha kukwaniritsa
zomwe tikufuna ngati dziko. Tikupempha Akatolika onse ndi anthu onse akufuna
kwabwino kuti aganizire mozama mfundo za makhalidwe abwino amene tafotokoza
mu Uthenga wathuwu. Mau a Mulungu amati, kumene kulibe mithenga yochokera kwa
Mulungu (masomphenya) anthu saweruzika” (Miyambo 29:18). Ngati Akatolika, tili ndi
masomphenya othandiza m’Maphunzitso athu a Mpingo okhudza moyo wathu. Ngati
dziko, limene likulakalaka kuti lidziwe chomwe tikufuna kukwaniritsa, Maphunzitso a
Mpingo pa za Moyo wa Anthu (Catholic Social Teaching) atha kukhala ngati mulingo
wotithandiza ndi kuchita zinthu zovomerezeka. Pa chifukwa ichi, mfundo zabwino za
Maphunzirowa tizitenge ngati gao lofunikira la moyo wathu chifukwa tidayitanidwa kuti
tikhale mchere ndi kuwala kounikira dziko lonse la pansi (Mateo 5: 13-16).
Monga Paulo Woyera akunena, “Ngakhale imfa kapena njala sizingatilekanitse ife ndi
chikondi cha Khristu” (Check quotation), tikukhulupirira kuti chikondi ndi chikhulupiriro
chathu mwa Mulungu ndi zimene zimatithandiza kuti tikhale ndi chikhulupiriro ndi
chiyembekezo cha Chikhristu chosagwedezeka. Ngakhale kuti moyo wathu wonse
wakutidwa ndi ziopsezo za njala, umphawi, kusowa kwa chilungamo, mliri, kusintha
kwa nyengo, etc. palibe chomwe chingatilekanitse ndi chikondi cha Khristu, amene,
m’chifundo chake, adadzipereka yekha chifukwa cha ife.
Tsopano tikutembenukira kwa Maria, Amai Achifundo. Tikupempha kuti ndi chikondi
chake chokoma atiyang’anire m’Chaka Choyera ichi, kuti tonse tithe kuzindikiranso
chimwemwe cha kukoma mtima kwa Mulungu! Asatope kutiyng’ana ife ndi maso ake
achifundo kuti ifenso tikhale oyenera kusinkhasinkha za nkhope ya Mwana wake Yesu
(cf. Misericordiae Vultus, 24).
Most Reverend Thomas L. Msusa Chairman and Archbishop of Blantyre
Right Reverend Martin Mtumbuka Vice Chairman and Bishop of Karonga
Most Reverend Tarsizio G. Ziyaye Archbishop of Lilongwe
Right Reverend Peter Musikuwa Bishop of Chikwawa
Right Reverend Emmanuel Kanyama Bishop of Dedza
Right Reverend Montfort Stima Bishop of Mangochi
Right Reverend George Tambala Bishop of Zomba
Monsignor Michael A. Muwowo Diocesan Administrator of Mzuzu
Tsiku: Lamulungu Lachisanu mu Nyengo ya Lenti, 13 March 2016
23
Episcopal Conference of Malawi
Its a well articulated pastral letter. Its balanced. This is what is need and we have to commend our bishops for this timely letter . Both the government & opposition need to reflect on this letter and change for the better. Malawians let us follow this noble advice and fully participate in paying taxes and other developmental activities. May God bless us all
Bravo ma Bishop athu ntchito mukuigwira.