KULIMBITSA MASOMPHENYA A KUMENE TILIKUPITA
KUKONZEKERA CHISANKHO CHAPATATU CHA 2014
M’NYENGO YA LENTI NDI PASAKA
Episcopal Conference of Malawi
Bungwe la Chilungamo ndi Mtendere (CCJP)
NYENGO YA LENTI YA MASIKU MAKUMI ANAYI (40)
Mpingo udasankha masiku 40 chifukwa masiku 40 m’Baibulo ndi nyengo yokozekera:
(a) Chigumula cha m’nthawi ya Nowa chinachitika masiku 40:
Mulungu ankakonzekera kulenganso kachiwiri dziko lapansi ndi mtundu wa anthu watsopano.
(b) Aisraeli adaali mchipululu zaka 40:
Mulungu ankawakonzekera kuti alowe m’dziko lachilonjezo.
(c) Mose adaakhala pa phiri la Sinai masiku 40:
Mulungu ankamukonzekera kuti akapereke malamulo khumi a Mulungu.
(d) Ulendo wa Eliya wopita ku phiri la Sinai udatenga masiku 40:
Anali kukonzekera kuti akumane ndi Mulungu.
(e) Anthu aku Ninive anasala ndi kuzilanga kwa masiku 40:
Adaali kukonzekera kuti Mulungu awakhululukire machimo awo.
(f) Yesu adakhala m’chipululu masiku 40:
Ankakonzekera kuti alalike Mthenga Wabwino wachipulumutso.
Momwemonso Lenti ndi ya masiku 40:
Timakonzekera kulandira misteri ya Pasaka yachipulumutso.
KUFUNIKA KWAKE KWA PASAKA
(a) Kwa Aisraeli, Pasaka chidali chizindikiro chakumasulidwa kuchokera ku ukapolo ndi kusanduka mfulu.
(b) Kwa Yesu, Pasaka ndikusintha kuchokera ku uchimo wadziko lapansi ndi kupita ku Ufumu wa Atate ake.
(c) Kwa Akhristu, Pasaka ndi chiyambi cha kusinthika kwathu kuchoka ku uchimo ndi imfa kupita ku moyo wosatha.
Mau Otsogolera
Chisankho chapatatu chikubwerachi chidzachitika pamene dziko la Malawi lizidzakondwerera zaka 50 (Golden Jubilee) za ufulu wakudzilamulira ndi zaka 20 za ulamuliro wa zipani zambiri womwe udayamba m’chaka cha 1993. Padakali pano tili mu nyengo yopambana kwambiri ya chakachi ngati Akatolika komanso ngati nzika za dziko lino lokoma ndi lokongola la Malawi. Ngati Akatolika, kuyambira tsiku la Phulusa (5 March, 2014), tikuyamba nthawi yopambana ya masiku makumi anayi (quadragesima) yowirikiza kaya titi kuchulukitsa mapemphero, kusala, ndi kuchita ntchito zachifundo. Nyengo imeneyi idzatifikitsa ku Mlungu Woyera – nthawi yapadera yokumbukira Masautso, Imfa ndi Kuuka kwa Ambuye athu Yesu Khristu. Nyengo ya Lenti idzatitsogolera ku nyengo ya Pasaka pamene timakondwerera kuti Ambuye athu Yesu Khristu adagonjetsa tchimo ndi imfa. Ngati nzika za dziko lathu lokongola lino – Malawi – posachedwapa tidzachita chisankho pa 20 May, 2014 pamene tidzasankhe atsogoleri athu kwa zaka zisanu zikubwerazi. Tili pa mphambano yofunikira kwambiri pamene mwai waukulu wotenga nawo mbali posankha tsogolo la dziko lathu wagwanso m’manja mwathu.
M’kalata yawo yaposachedwapa yotchedwa “Kulimbikitsa Masomphenya a Kumene Tilikupita”, Aepiskopi adapempha Akatolika onse ndi anthu onse akufuna kwabwino kuti agwiritse ntchito bwino ndiponso moyenera mwai wa chisankho chapatatu chomwe chikubwerachi pozindikira kuti mwai wotere umapeleka mpata wamtengo wapatali kuti tilibikitse masomphenya a kumene tili kupita ngati dziko. Monga Yoswa ndi atsogoleri anzake, Aepiskopi athu akuona kuti Malawi wafika pa mphambano: “ngati simutumikira Ambuye, sankhani lero yemwe mufuna kudzamtumikira…Ine ndekha ndi banja langa, tidzatumikira Ambuye” (Yoswa 24:15). Tikupemphedwa kuti tilimbikitse masomphenya a kumene tilikupita ngati dziko ndipo kuti tidzipereke kugwira ntchitoyi potsata mapazi a makolo athu omwe adachita zazikulu kuti tifike pamene tilipa komanso kuti tisasankhule mchitidwe odziononga tokha. Tikupemphedwa kulimbikitsa ndi kumanga Malawi yemwe makolo athu adali naye masomphenya ndipo kuti tisiyiretu mchitidwe wosandutsa Malawi kukhala wotsutsana ndi amene makolo athu adamenyera nkhondo ndi kumfela.
Chisankho chapatatu chomwe chikubwerachi, chikutipatsa ife mwai wolimbikitsa masomphenya a kumene tilikupita. Zonzezi zitanthauza kuchita chisankho cha ufulu, chokomera ndi kuvomerezeka ndi anthu onse komanso kusankha atsogoleri omwe ali ndi khumbo, kudzipereka ndipo omwe angakwanitse kusintha zinthu m’dziko mwathu muno. Chikutanthauzanso kuti anthu ovota atha kutuluka mu umphawi wadzaoneni womwe ali nawo podzisankhira atsogoleri omwe angawathandize kutero. Kulephera kukhala ndi chisankho chotere, kusavota komanso kulephera kusankha atsogoleri abwino, kwa ife ndi chimodzimodzi kusankha imfa mmalo mosankha moyo. Uwu ndiye uthega wakalata yathu yomwe tikupereka kwa Akatolika anzathu ndi kwa anthu onse akufuna kwabwino. Ili ndiye pempho lathu kwa onse okhudzidwa ndi chisankho chikubwerachi.
Ndi mwai wa mzama kwaife kuti nyengo yotifikitsa ku chisankho cha patatuchi ikuyendera limodzi ndi nyengo ya Lenti ndiponso Pasaka, nthawi yomwe timakumbukira zazikulu za chipulumutso chathu zomwe ndi Masautso, Imfa ndi Kuuka kwa Ambuye athu Yesu Khristu. Kodi tinganene kuti zimenezi zangochitika mwangozi? Zochitika zilizonse m’moyo wa anthu sitingazimvetse popanda kuzitanthauzira mwauzimu; popeza kuti kudzera m’zochitika zimenezi, ndithudi ndi m’mene Mulungu amadzionetsera kwa ife. Iyi ndi nyengo ya chaulere cha Mulungu!
Kabuku kano ndi njira imodzi yowonetsetsa kuti tsogolo la dziko lathu lino liyendetsedwe ndi dzanja la Mulungu makamaka panthawi yofunikirayi. Kabukuka kakuika pamodzi Mau a Mulungu ndi maphunzitso a Aepiskopi athu kuti poteropo tithandizane kupemphera, kusinkhasinkha ndi kutenga nawo mbali pa nthawi ino pamene chisankho chayandikira. Bukuli likutithandiza kupemphera ndinso kusinkhasinkha pogwiritsa ntchito makalata a Aepiskopi ndi Mau owerengedwa pa tsiku Lamulungu. Izi zili molingana ndi chikhulupiriro cha Mpingo choti “chimwemwe ndi chiyembekezo, madandaulo ndi mazunzo a anthu anthawi yathu ino,…ndizo chimwemwe ndi chiyembekezo, madandaulo ndi mazunzo a anthu otsatira Yesu Khristu” (Gaudium et spes 1).
Ngakhale kuti iyi sikalata ya Aepiskopi athu monga timaidziwira nthawi zonse, komabe mfundo ziri mkatimu zachokera m’kalata za Aepiskopi ndipo njira yogwiritsa ntchito kalatazi m’nyengo ino yokonzekera chisankho motere yavomerezedwa ndi Aepiskopi athu onse. Maganizo amenewa akugwirizananso ndi zomwe anavomerezana Aepiskopi athu ku msonkhano wao wa AMECEA zoti ndi bwino kuti Mpingo wa Katolika kuno ku Malawi ukhale woona kutsogolo, watcheru ndinso wachangu pankhani zobweletsa Chiyanjano, Chilungamo ndi Mtendere.
M’ntchitoyi tasonkhanitsa pamodzi mfundo zikuluzikulu zam’kalata ya Aepiskopi ya December, 1st, 2013, yotchedwa “Kulimbikitsa Masomphenya a Kumene Tilikupita” ndi mfundo zina za kalata zam’mbuyomu za Aepiskopi zokhudza chisankho. Bungwe la Katolika la Chilungamo ndi Mtendere kudzera mu kabukuka likufuna kuthandiza Mpingo ndi anthu ena akufuna kwabwino kukonzekera bwino Pasaka ndi chisankho chapapatu chikubwerachi.
Kwenikweni zolinga za kabukuka ndi zitatu. Mfundo yoyamba, bukuli lithandiza ansembe kukonzekera bwino kugawa mau m’nyengo ya Lenti ndi m’chikondwerero cha Pasaka. Kachiwiri, bukuli liri ndi mfundo zikuluzikulu zoti anthu aziganizira ndi mafunso oti anthu adzikambirana mozama m’magulu monga m’miphakati/m’malimana, m’magulu a Chilungamo ndi Mtendere, m’magulu a achinyamata, Akhristu eni ake ndi m’zokambirana zina zokhudza chisankho. Cholinga chotsiriza ndi chofunika kwambiri ndi chakuti, kubukuka kapereke chikhumbokhumbo kwa anthu kuti asinkhesinkhe, apemphere, ndi kusintha moyo wao m’nyengo ino ya Lenti ndi ya Pasaka. Kabuku aka kalembedwa kuti kathandize Akhristu panyengo ino ya Lenti ndi ya Pasaka kuganiza bwino za udindo wao pothandiza kukonza tsogolo la dziko lino.
Ntchito iyi ikadakhala nkhambankamwa chabe ngati sipakadapezeka anthu, magulu komanso mabungwe oti maganizo a Aepiskopiwa awatsatire ndikuyesetsa kuchitapo kanthu kuti izi zitheke. Tiwathokoze pano onsewa chifukwa cha chithandizo, luntha ndi kudzipereka kwao. Taonani tsono, ntchito yawo ndi imene iri m’manja mwathuyi. Chaka chino mwai uli m’manja mwathu pamene nyengo ya Lenti ndi Pasaka ndi nyengonso imene tikukonzekera chisankho chapatatu. Kuyandikana kwa nyengozi singozitu ayi. Ino ndi nthawi imene tikupemphedwa kuti tiyikirepo umboni pa mphamvu ya Mulungu pa zochitika za m’dziko popeza kuti zonse zochitika padziko pano zilitu m’manja mwa Chauta.
Rev. Fr. George Buleya
Secretary General – Episcopal Conference of Malawi
MAU OYAMBIRIRA
2014 ndi chaka cha masankho pachifukwa ichi ndi chofunikira kwa ife a Malawi. Nyengo ya Lenti ndi Pasaka tayambayi, kuyambira Tsiku la Phulusa, pa 5 March 2014, ndi nthawi ya mwai wa padera woti tipempherere ndikusinkhasinkha za atsogoleri omwe tingafune kusankha kuti ayendetse dziko lathu.
Lenti
Lenti ndi nyego yoti tiunikiridwe ndi kudziyeretsa. Ndi nyengo yakuwala yomwe timapemphedwa kusinkhasinkha mfundo zitatu zofunikira izi:
1. Kukhazikika m’moyo wamapemphero
Lenti ndi nthawi yopempha Mulungu mtima wofuna kusintha machitidwe athu ndikukhulupirira Mthenga Wabwino. M’nyengo ya Lentiyi, aliyense mwa ife akupemphedwa kuyamba ndi kutsiriza tsiku lirilonse ndi pemphero. Kuwonjezera apo, tikupemphedwa kuti tizipemphera poyamba ndi potsiriza ntchito iliyonse. Yesu Khristu adatiphunzitsa kuti tizipemphera nthawi zonse mosalekeza. Kupemphera ndi kukweza mitima ndi maganizo athu kwa Mulungu, ndipo pemphero limaposa zinthu zonse. Komabe, tikuchenjezedwa kuti tipewe kugwa m’chinyengo chodzionetsera pochita mapemphero athu. Tizipemphera pokhulupirira kuti Mulungu ndiye Atate athu amene amatikonda nthawi zonse ndipo ndi wokonzeka kutithandiza. Pamene tikupemphera, timasonyeza mtima wofuna kuchita kufuna kwake m’malo momuumiriza kuti achite kufuna kwathu.
M’mapemphero athu a m’nyengo ino ya Lenti chaka chino, tikupemphedwa kupempherera chisankho chapatatu chikubwerachi kuti Mulungu atiunikire kuti tidzavotere atsogoleri abwino, amasomphenya, ndi otha kusintha zinthu omwe adzatsogolere Malawi kukhala otukuka ndi wochita bwino pachuma.
2. Kudzilanga
Nyengo ya Lenti ikutipempha aliyense mwa ife kusala zosangalatsa za thupi, monga zakudya ndi zakumwa, kuugwira mtima pa zilakolako, ndikupewa khalidwe lodzikonda. Malembo Woyera akutiuza kuti Yesu yemwe adasala zakudya masiku 40. Cholinga cha chizolowezi chimenechi ndi kutithandiza kuugwira mtima ndi kulora kuti mitima ndi maganizo athu zigwirizane ndi Mulungu. Izi zimatithandiza pa nkhondo yolimbana ndi zoipa ndi satana.
3. Ntchito zachifundo
Potsiriza, ndalama ndi zinthu zina zonse zomwe taika padera pokhala wodzilanga mu nyengo ya Lenti zikuyenera kugwiritsidwa ntchito pothandiza amphawi ndi osowa omwe m’gulu mwawo mulinso ana ndi amai amasiye. Izi zimatiphunzitsa kukhala odzimana. Amalawi, chaka chino pa chisankho cha patatu chikubwerachi, akupemphedwa kuvotera pa maudindo osiyanasiyana atsogoleri omwe angakwanitse kubweretsa umodzi, chilungamo, mtendere ndi chitukuko m’dziko. Tiyeni tisapereke dziko lino m’manja mwa atsogoleri oipa, osaganizira amphawi makamaka anthu akumudzi omwe ndi ochuluka, komanso atsogoleri odzikonda omwe akungotanganidwa ndi kudzilemeretsa ndi kudzikundikira chuma. Tiyeni tikhale maso ndipo tisalole kupusitsidwa ndi atsogoleri omwe akulojeza zabodza zoti abweretsa chuma kudziko lino popanda kuchigwirira ntchito.
PASAKA
Chikondwerero chachikhristu cha Pasaka gwelo lake ndi chikondwerero cha Pasaka cha Ayuda chomwe chidali chikumbutso komanso chifaniziro cha ulendo wokutuluka (exodus) omwe unawamasula Ayuda muukapolo waku Ejipito. Aisraele amachita chikondwerero ichi usiku wa pa 14 mwezi omwe iwo ankautcha Abib (omwe pambuyo pake anayamba kuutcha Nisan). Poyamba kwenikweni ankatsira nsembe ya mwana wankhosa kapena mwana wambuzi wobadwa chaka chomwecho ndi wopanda chilema (Eks. 12:3-6) komanso kosathyoka fupa (Num. 9:12) pofuna kupempha madalitso pa msambi wawo. Magazi a mwana wa nkhosa uja amawapaka pa mphuthu za zitseko ngati chizindikiro chakuti iwo ndi wopatulidwa. Nyama ya mwanawonkhosa ija inkadyedwa limodzi ndi buledi wopanda chotupitsira pa mwambo wa chakudya omwe unkachitika mwachangu.
Pa Phwando la Pasaka, Aisreale amakumbukira ndikusandutsanso chatsopano mwambo osaiwalika pamene mnjelo wa Mulungu anapitilira nyumba zawo ndi kupha mwana woyamba aliyense wa Muegipito. Amachita chikodwerero ichi osati ndi cholinga chongolengeza za ntchito zazikulu za Mulungu ayi, komanso kukumbukira chipulumutso chawo ndi kuti iwowo ndi Fuko loima palokha ngati dziko.
Mu Chipangano Chatsopano, Yesu anachita phwando la Pasaka asadalowe m’masautso ndi imfa yake. Mkati mwa phwandolo Iye adatenga buledi namusandutsa kukhala thupi lake. Adatenganso chikho cha vinyo nasandutsa vinyoyo kukhala magazi ake omwe adayenera kudzakhetsedwa kuti anthu ambiri apulumuke. Kudzera m’mwambo umenewu, Yesu adasanduka Kankhosa katsopano ka Pasaka amene imfa yake idasanduka chiyambi cha kutuluka (exodus) kwatsopano kuchoka mu ukapolo wa utchimo wa dziko lino kupita ku Ufumu wa Atate ake (Yoh 13:1).
Pasaka yachikhristu imakondwerera Pasaka ya Yesu wochoka ku imfa kupita ku moyo wosatha. Popeza kuti Yesu Khristu adauka pa tsiku loyamba la Sabata, Akhristu amakumbukira nasandutsanso Pasaka ya Yesu kukhala yochitika chatsopano pa tsiku lotsatira Sabata ya Ayuda. Aroma adalitchula tsikuli, “TSIKU LA DZUWA”. Akhristu adalisandutsa kukhala “TSIKU LA AMBUYE” (TSIKU LA MULUNGU) (Chiv. 1:10).
Pasaka ndi chikondwerero choposa zikondwerero zina zonse pakati pa Aisraele komanso Akhristu. Imawapempha kukhala ndi moyo woyenerana ndi zazikulu zomwe amakondwerera nazisandutsa kukhalanso ngati zochitika chatsopano. Pokhala amodzi ndi Khristu mu Ukaristia, Pasaka imayatsa mwa Akhristu moto wachikhulupiriro chakudzakomana naye Khristu mkubwera kwake kwachiwiri (Parousia) (I Ako. 11:26). Loweruka lisadafike tsiku la Pasaka, Akhristu amachita mapemphero wochezera usiku wonse pamene amawerenga Malembo Woyera osimba za mbiri yonse ya chipulumutso; amabatiza akatekumeni kukhala ana a Mulungu; amachita mwambo wa chizindikiro cha kufa kwao ku moyo wa uchimo ndi kuuka kwao ku moyo watsopano; ndipo amatsira Nsembe ya Ukaristia. Mu njira iyi, Pasaka yachikhristu imautsa chiyembekezo mwa mkhristu aliyense choti wakwanitsa kufikapo pa Misteri ya Pasaka kudzera m’kukomana kwake ndi Ambuye m’masautso, imfa and kuuka kwao. Pa chifukwa ichi, Pasaka ya Akhristu ndiye chiyambi cha ulendo wopita ku phwando lakumwamba.
Chisankho Chapatatu Chomwe Chikubwerachi
Pa chisankho chapatatu chomwe chikubwerachi, woyenera kuvota adzakhala ndi mwai wovotera Khansala, Phungu wa Nyumba ya Malamulo ndi Pulezidenti wa dziko. Chifukwa cha ichi, ndi kofunika kufotokozera bwino chomwe wovota ayenera kuganizira asanaponye komanso mkati mwakuponya voti yake.
Kusankha Wotiimirira
Zotsatirazi ndi mfundo zofunika kuziganizira pofufuza munthu woyenera kukhala wotiimirira ku Ward, (monga khansala), constituency (monga phungu wa nyumba ya malamulo) komanso dziko (monga Pulezidenti).
• Makhansala ayenera kukhala odziwika m’dela lanu, aphungu ayenera kukhala odziwika mu constituency yao.
• Makhansala ayeneranso kukhala odziwa bwino zosoweka za dela lanu.
• Makhansala ayenera kukhala nzika za ward yanu, pamene phungu akhale nzika wa constituency yanu ndipo pulezidenti akhale nzika ya dziko lanu.
• Onse akhale ndi mtima woganizira anthu wosauka ndi oponderezedwa.
• Asalonjeze zinthu zomwe sizikhudza mphamvu zao kapenanso kulonjeza zinthu zosatheka, koma alonjeze zinthu zomwe zingatheke kuzikwaniritsa komanso zomwe zikukhudza mphamvu ndi udindo wawo ngati khansala, phungu kapena pulezidenti.
• Aonetse poyera kuti ndi anthu oyeneradi kuti ena awadalire ndipo kuti ali wokonzeka kutumikira anthu onse.
• Aonetse poyera mfundo zawo zoyendetsera ntchito pa udindo wawo ndiponso pamene akulengeza manifesto zawo, asonyeze kuti ali ndi masomphenya othandiza kusintha zinthu m’dela lanu ndi m’dziko lonse.
Kufotokozera za Maudindo a Khansala, Phungu ndi Pulezidenti
Khansala ndi munthu yemwe wasankhidwa kuti ayimirire anthu mu khonsolo ya pa boma kapena tawuni kapenaso mzinda. Khansala amakhala limodzi ndi anthu ake ndipo amaonetsa chidwi pa madandaulo ndi zopempha za anthu makamaka zokhudza chisamaliro cha anthu mu dela kapena ward yake.
Ntchito ndi udindo wa Khansala
• Kuimirira anthu a m’dela / ward ku Khonsolo ndi kumapititsa ku khonsoloko madandaulo omwe anthu akufuna kuti khonsolo iwathandize;
• Kukonza mapulani achitukuko ndi kukawapereka ku khonsolo kuti khonsoloyo ichitepo kanthu;
• Kukamba ndi aphungu akunyumba ya Malamulo ndi cholinga chofuna kuonetsetsa kuti anthu a mu ward akulandira chisamaliro chokwanira komanso choyenerera monga pa nkhani za magetsi, chitetezo komanso chithandizo pa mavuto ogwa mwadzidzidzi;
• Kutenga nawo mbali pa ntchito yoounika bwino kagwiritsidwe ntchito ka ndalama za khonsolo ndi mmene khonsolo ikugwirira ntchito zake zotumikira anthu potengera ward yokhudzidwayo. Chinanso kuonetsetsa kuti ntchito zonse za khonsolo zikugwiridwa mosabisa kanthu komanso mosamala chuma. Kufotokozera anthu zonse zomwe khonsolo yamanga ngati ndondomeko yoyendetsera ntchito za khonsolo.
Phungu wa Nyumba ya Malamulo ndi munthu wosankhidwa kuti ayimirire anthu mu constituency (dela lokulirapo lopangidwa ndi ma ward awiri kukakhala kumidzi, kupitilira awiri kukakhala m’tawuni). M’Malawi muno tili ndi ma constituency 193 zomwe zikutanthauza kuti tiyenera kukhala ndi aphungu aku nyumba ya Malamulo okwana 193.
Udindo wa Phungu wa Kunyumba ya Malamulo:
• Kuiimirira anthu mu constituency popititsa ku Nyumba ya Malamulo madandaulo a anthu omwe akusowa kuti boma lichitepo kanthu komanso kufotokozera anthu zonse zomwe Nyumba ya Malamulo yamanga ngati mfundo zoyendetsera dziko.
• Kuiimirira zokonda za anthu a mdela lake pa zokambirana za dziko lonse.
• Kuyang’anira ntchito zonse za boma kudzera m’makomiti a ku Nyumba ya Malamulo.
• Kukambirana ndi kupanga malamulo a dziko mu Nyumba ya Malamulo.
Pulezidenti wa Dziko ndi mtsogoleri wa zonse yemwe wapatsidwa mphamvu zotsogolera ntchito zonse za boma. Udindo uwu ndi waukulu koposa maudindo ena onse m’dziko lathu lino ndipo ndi okhudza kutsogolera komanso kuyendetsa dziko.
Zina mwa Ntchito za Pulezidenti:
• Kuimirira anthu onse pa nkhani zokhudza dziko lonse;
• Kuvomereza ma bill omwe aunikidwa ndi kuvomerezedwa Kunyumba ya Malamulo.
• Kupereka utsogoleri ku dziko.
• Kutsogolera nthambi zitatu za boma zomwe ndi; Nduna za boma, a ku khothi ndi Aphungu a ku Nyumba ya Malamulo;
• Kutsogolera dziko ndi boma.
Mfundo zofunika zothandiza anthu kutenga mbali moyenera mu chisankho chapatatu
Kaponyedwe ka Voti
• Padzakhala mapepala ovotera atatu, lovotera; pulezidenti, phungu wa Kunyumba ya Malamulo ndi khansala.
• Chongani pa mapepala onsewo koma pa pepala lirilonse chongani munthu m’modzi wakumtima kwanu.
• Kuchonga anthu awiri kapena oposa apo pa pepala lovotera kudzapangitsa kuti pepala la voti lanulo lisavomerezedwe.
Zofunika zina zotiunikira pa chisankho
(a) Poponya voti ya Khansala pafunika kuti ovota adziwe bwino malire a ward yawo kuti apewe kuvotera khansala wa ward yina komwe khansala wawo sakupezeka pa pepala lovotera.
(b) Mu constituency iliyonse ya kumidzi muli ma ward awiri kupatulo ma constituency amene ali m’tauni.
(c) Anthu onse omwe analembetsa pa kalembera wa voti ayenera kukhala ndi chidwi chopita ku misonkhano ya kampeni yonse.
(d) Mudziwe udindo ndi ntchito zenizeni za khansala, phungu ndi pulezidenti kuti musasokoneze izi ndi malonjezo abodza.
(e) Nkofunika kuti tipewe kugwiritsa ntchito chipembedzo, mtundu ndi chikhalidwe cha anthu pofufuza khansala, phungu kapena pulezidenti woyenera kuti timuvotere.
(f) Sizili choncho nthawi zonse kuti wopikisana yemwe ali wa mtundu wathu, chipembedzo chathu, kapena wochokera ku chigawo chakwathu ndiye amene angakhale wabwino koposa ena onse kapena kuti ndi yemwe angakhale oganizira zokonda za anthu koposa onse ayi.
(g) Tikukumbutsidwa kusankha atsogoleri omwe angasinthe miyoyo yathu, chuma chathu, ndale zathu komanso ife tonse ngati Amalawi.
(h) Tipemphere ndi kudalira Mulungu kuti ationgolere pamene tikusankha atsogoleri.
(i) Tisankhe atsogoleri omwe akufuna kufikitsa dziko lathu la Malawi ndi madela athu onse pa mulingo watsopano wachitukuko komanso njira yatsopano yoyendetsera ntchito za ndale.
9 March, 2014: LA MULUNGU LA 1 MU LENTI
1. CHOLINGA: KUGWIRITSA NTCHITO BWINO UFULU WATHU WOPATSIDWA NDI
MULUNGU
MAU OYAMBIRIRA: Mwachikondi chake chachikulu Mulungu adatilenga natipatsa nzeru ndi ufulu. M’mau oyamba, tikumva kuti makolo athu akale aja adaononga ufulu umene Mulungu adawapatsa. Iwo sadamvere Mulungu ndipo adachimwa pakudya chipatso choletsedwa m’munda uja wa Edeni. Pamene makolo athu adalephera, Yesu adakonza pakugonjetsa tchimo ndi manyengero a satana chifukwa chakudya cha Yesu chinali kuchita kufuna kwa Atate ake. Ndi kofunikira kuti tidzipereke kwathunthu pakuchita kufuna kwa Mulungu. Chifukwatu chimwemwe ndi mtendere weniweni zimadza pakumva ndi pakuchita zomwe Mau a Mulungu anena. Kusamvera kumadzetsa zomwe Malembo Oyera amatcha “umaliseche”, kutanthauza kudzitsitsa pa ulemerero wa umunthu ndi kufika pa mlingo wa nyama. Kudzidalira mwa iye yekha ngati munthu kumatsutsana ndi ndondomeko yachipulumutso cha Mulungu.
2. KUMVETSA MAU A LERO
MAU OYAMBA: Genesis 2:7-9; 3:1-7
(a) Pamene Mulungu adalenga munthu mchifanizo chake, adafuna kuonetsa ulemerero omwe munthu ali nawo kusiyana ndi zolengedwa zina.
(b) Mulungu adafuna kuti munthu aliyense akhale ndi ufulu ndi wokondwa, koma ngati cholengedwa ndi Mulungu, ufulu wake uli ndi malire. Mulungu yekha ndiye mtengo wopatsa moyo ndi nzeru zodziwira zabwino ndi zoipa. Kudziwa zabwino ndi zoipa kutanthauza kukhala ngati Mulungu amene amadziwa zonse.
(c) Zinyengo zimadza pofuna kuyesa mphamvu zathu osati kufooka kwathu. Kodi tinene kuti njoka ija inapeza mkazi uja poti anali ndi nzeru zambiri ndiponso kuti akanatha kuphunzira nsanga?
(d) Njoka imatengedwa kuti ndi yochenjera chifukwa:
i. Kufundula kumasonyeza kuti ili ndi njala yofuna kukhala wamuyaya
ii. Imayenda popanda phokoso ndipo imaluma mosayembekezera
iii. Imaikira mazira ambiri.
(e) Kuchimwa kumatanthauza kusokoneza zoona za Mulungu kuti zikhale ngati zabodza. Mkati mwakuchimwa paakudya chipatso choletsedwa chija, Adamu ndi Eva azindikira tchimo ndipo ndi ogwidwa ndi manyazi.
SALIMO: 50:3-6, 12-14,17
Tonse ndife ochimwa ndipo tisowa chikhululukiro cha Mulungu. Ngati tilapa machimo athu, Mulungu ndi wokonzeka kutikhululukira chifukwa chifundo chake ndi chopanda malire.
MAU ACHIWIRI: Aroma 5:12-19
Paulo akufotokozera kusiyana pakati pa Adamu ndi Yesu. Pakumvera Atate ake, Ambuye athu Yesu Khristu adagonjetsa tchimo ndi imfa zomwe zinabwera chifukwa cha kusamvera kwa Adamu. Koma kudzera mwa Yesu, imfa idatipatsa moyo.
MTHENGA WABWINO: Mateo 4:1-11
(a) Yesu ndiye Mose watsopano amene adakhadzikitsa Israele watsopano:
(i) Monga adachitira Aisreale polowa m’chipululu pambuyo pooloka Nyanja yofiira, Yesu akupita ku chipululu pambuyo polandira ubatizo mumtsinje wa Yordane;
(ii) Monga adachitira Aisraele pokhala m’chipululu zaka 40 asadalowe m’dziko lachilonjezo, Yesu adakhala masiku 40 m’chipululu asadayambe ntchito yake yopulumutsa anthu;
(iii) Monga adayesedwera Aisraele m’chipululu muja, Yesu nayenso adayesedwa m’chipululu muja;
(b) CHINYENGO CHOYAMBA: Dyera. Satana adafuna kuyesa Yesu kuti asandutse miyala kukhala chakudya ngati chida chofuna kutchukira. Yesu sadagonjere mayeserowo ndipo adagwiritsa ntchito Mau opezeka pa Deuteronomo 8:3 omwe akuti, “munthu sakhala ndi moyo ndi chakudya chokha ayi koma ndi mau onse otuluka mkamwa mwa Mulungu”.
(c) CHINYENGO CHACHIWIRI: Milakuli. Satana adayesa Yesu kuti aonetse ulemerero wake. Adamuuza Yesu kuti adzigwetse pansi kuchokera pa denga la tempile chifukwa choti Salimo 91:11 imatsimikizira za chitetezo cha Mulungu kwa anthu osankhidwa ngati Iyeyo. Ngati savulala anthu adzamtamanda kuti ndiye mpulumutsi. Koma Yesu adagwiritsa ntchito mau apa Deuteronomo 6:16 akuti, “usayese Ambuye Mulungu wako”.
(d) CHINYENGO CHACHITATU: Kupembedza mafano. Podzitchula kuti ndiye Mbuye wadziko lonse lapansi, satana akuuza Yesu kuti amugwadire ndi kumpembedza ndi cholinga choti satanayo ampatse Yesu ulamuliro wadziko lonse lapansi. Yesu adakana ponena mau apa Deuteronomy 6:13, akuti, “muziopa Chauta Mulungu wanu, muzipembedza Iye yekha.”
3. MAPHUNZIRO:
(a) Taphunzira kuti kumvera ndiye gwero la chimwemwe ndi bata la mumtima. Ndipo kumvera koona kumatanthauza kumva mau ndi kuchita kufuna kwa Mulungu.
(b) Anthu onse amagwa m’chinyengo cha kudzikhulupirira iwo wokha, cha kunyada ndi cha kufuna kukhala ndi mphamvu zolamulira. Tiyeni tisankhe njira yachikondi ndi yakutumikira chifukwa Yesu ndiye njira imeneyi.
(c) Kudziwa mau a Mulungu ndi kuchita zomwe mauwo akunena kuti tigonjetse zinyengo. Tiyeni tikhale mtundu woopa Mulungu pakuika mitima yathu pa njira ya kumva ndi kuchita zomwe mau a Mulungu amanena.
4. MAPHUNZIRO OCHOKERA M’KALATA ZA AEPISKOPI ATHU
(a) Chimwemwe chenicheni chimapezeka pamene tivomereza kuti ndife olengedwa m’chifanizo cha Mulungu ndi pakuchita zinthu ngati ana a Mulungu (Momwe tingamangire fuko lachimwemwe, 20th march 1961);
(b) Masomphenya a Malawi watsopano amene akutchulidwa m’nyimbo yafuko lathu akutsamira pa chikhulupiriro mwa Mulungu ndi chithandizo chake. Makolo athu akale aja adatsindika mfundo yoti ndife mtundu woopa Mulungu. Pa chifukwa ichi, zolakalaka zathu, maloto ndi masomphenya atsogolo lathu ndiponso mtima ofuna kukhala Fuko, tsinde lake lenileni ndi chikhulupiriro mwa Mulungu ndiponso kutsata zimene Mulunguyo amatiunikira kuti tikhale Fuko lachilungamo. (Kulimbikitsa Masomphenya a Komwe Tilikupita, 1st December, 2013, p.3);
(c) Pali makhalidwe ambiri oipa pakati pathu amene amachititsa kuti anthu asamalabadire za Mulungu ndi kuti azidalira nzeru zawo zokha ndiponso kuti adzisankhire okha chabwino ndi choipa (Kulimbikitsa Masomphenya a Komwe Tilikupita, 1st December, 2013, p.7)
(d) Zinayenera kutero kuti pamene takwaniritsa zaka 50, Mmalawi aliyense anayenera kusangalala pokhala ndi zomuyenereza zomwe zimatheka ngati tiganizira zaubwino wa aliyense. Nkhani yomwe ili pano ndiyakuti tione ngati tidagwirizana ndi Mulungu pa masomphenya athu m’zaka 50 zapitazi. Tidayamba ndi kulakalaka kukhala ndi Malawi wotukuka pa ndale ndi pa chuma mothandizidwa ndi Mulungu. Pachifukwa ichi, tisaganize kuti lero tingakwanitse masomphenya athuwa popanda Mulunguyo (Kulimbikitsa Masomphenya a Komwe Tilikupita, 1st December, 2013, p.22).
5. ZOYENERA KULINGALIRA
(a) Kodi ife anthu timasiyana bwanji ndi zolengedwa zina?
(b) Taphunzirapo chaini pa za kulumikizana kwa pakati pa ufulu ndi kumvera Mulungu potengera zomwe zili mu nkhani ya Adamu ndi Eva m’munda wa Edeni uja?
(c) Kodi masomphenya amakolo athu akale aja anali otani mokhudzana ndi dziko lathu komanso chikhulupiriro chathu mwa Mulungu?
(d) Perekani zitsanzo za malamulo, mfundo ndi machitidwe omwe akuonetsa kuti amalawi adataya masomphenya akale aja moyang’anira chikhulupiriro chathu mwa Mulungu.
(e) Ndi zinthu ziti zomwe tingatchule zimene tinganene kuti Malawi adapindula mu zaka 50 zaufulu wodzilamulira?
(f) Ndi zizindikiro ziti zosonyeza kuti Amalawi akufunitsitsa kuti akhale ndi ufulu wotaya pakati, wogwiritsa ntchito njira zakulera, wokwatirana amuna kapena akazi okhaokha, kukana kuti Mulungu alipo zomwe monga adachitira Adamu, zikusonyeza kuti anthu akufuna ufulu opanda malire?
(g) Poyang’anira masomphenya amakolo athu akale aja, ndi atsogoleri otani amene tiyenera kusankha pachisankho chapatatu chikubwerachi?
(h) Ngati mzika tili ndi udindo otani pofuna kuonetsetsa kuti tikusunga masomphenya ofuna kuika Mulungu patsogolo?
16 March, 2014: LA MUMULUNGU LA 2 MU LENTI
1. CHOLINGA: ULENDO WOPITA MTSOGOLO
MAU OYAMBIRIRA: Kuti tikwaniritse zolinga zathu tiyenera kucheza ndi anzathu. Ulendo wa Abram wopita ku Kanani udaali ulendo umene udadzapindulira ena. Kudzera mwa Abram anthu amitundu yonse padziko lapansi adzalandira madalitso. Momwenso ulendo wa Yesu wopita ku Yerusalemu omwe unali nkhani yayikulu pomwe Yesu anasintha maonekedwe ake pa phiri paja udzadzetsa chipulumutso ku dziko lonse.
2. KUMVETSA MAU ALERO
MAU OYAMBA: Genesis 12:1-4
(a) Mulungu adauza Abram kuti achoke kudziko lakwawo, komwe adakuzolowera, anali wotetezedwa, ndiponso komwe ankakhala mokondwa;
(b) Chikhulupiriro ndi kudzipereka kwake kwa Abram kunadzetsa madalitso ochuluka ku mitundu yonse ya dziko lapansi;
(c) Ngakhale chinali chinthu chovuta kuti asiye dziko lake, iye adakhulupirira ndipo adamvera Mulungu.
SALIMO: 32:4-5, 18-20, 22
Salimoyi ndi yotamanda Mulungu chifukwa cha kukhulupirika kwake komwe kumatipatsa chiyembekezo m’malonjezo ake ndiponso chikhulupiriro m’chikondi chake.
MAU ACHIWIRI: 2 Timoteo 1:8-10
(a) Paulo akulangiza Timoteo kuti avomere zinthu zonse zosasangalatsa zobwera chifukwa chotsata Mthenga Wabwino;
(b) Kuitanidwa ndi Mulungu ndi mphatso yopambana imene imaulura cholinga cha muyaya chimene chimayenera kuchititsa ochilandira kuti athandize anthu ena.
MTHENGA WABWINO: Mateyo 17:7-19
Ali ku Yerusalemu, Yesu adzakwanilitsa zosowa za dziko lapansi kudzera m’masautso ndi mu imfa yake yapamtanda. Koma imfa yake idzapherezera m’chigonjetso ndi ulemerero wake.
(a) Maonekedwe a Yesu asinthika pamaso pa Petro, Yakobe ndi Yohane ndipo iwowa adzamuonanso akuzunzika m’munda wa Getsemani;
(b) Phiri ndi malo okomanilanako ndi Mulungu;
(i) Kuitanidwa kwa Mose ndiponso kulandira malamulo khumi a Mulungu kudachitika pa phiri la Sinai;
(ii) Eliya, pambuyo pothawa chiwembu cha Jezebel chofuna kumupha adapita ku phiri la Sinai kumene adakakumana ndi Mulungu;
(iii) Chinyengo chotsiriza cha Yesu chinachitikira ku phiri;
(iv) Maphunziro akulu a Yesu adachitikira pa phiri;
(v) Yesu adadyetsa anthu zikwizikwi pa phiri;
(vi) Asanakwere Kumwamba, Yesu adatsazika ophunzira ake pa phiri;
(c) Mose akuimira Malamulo ndipo Eliya akuimira aneneri. Malamulo ndi aneneri akuimira Chipangano Chakale. Polankhula ndi Yesu, Mose ndi Eliya akusonyeza kuti Yesu akupherezetsa Chipangono Chakale;
(d) Mau omveka kuchokera kumwamba akusonyeza kuti Yesu ndi Mwana wokondeka wa Mulungu. Tiyeni timumvere. Zakale zapita. Tiyeni tiyambe zatsopano.
3. MAPHUNZIRO:
(a) Monga adachitira Abram, tiyeni tidzichita zinthu ndichikhulupiriro mwa Mulungu; siyani kaganizidwe ndi makhalidwe akale zomwe ndi monga; kugawira anthu zinthu zaulere, kuchulukitsa zipani zandale zopanda mfundo zenizeni, kufuna kukhala atsogoleri opanda masomphenya, adyera, akuba, otukwana, abodza ndi zina zotero.
(b) Yambani mwatsopano, khulupirirani Mulungu ndikumanga Malawi watsopano. Funiranani zabwino pakukhala ndi mtima umodzi. Yambani zinthu zatsopano, musachoke pakati pa anzanu, limbikitsani ndikupititsa patsogolo ubwino wa anthu onse.
(c) Monga adachitira Timoteo, tiyeni tilalike ndi kuchitira umboni Mthenga Wabwino mopanda mantha ndi manyazi. Cholinga chathu chikhale kusintha kaganizidwe ka anthu. Tiunikire anthu kuti asiye kuona anzawo ngati olephera pamene akupita patsogolo ndi luso losiyanasiyana ndiponso pandale.
(d) Monga Ambuye yesu adasinthika pa phiri paja, nafenso tisinthe mitima yathu, nzeru zathu ndi maganizo athu ndiponso pakayendetsedwe ka dziko lathu. Tiyeni tichotse atsogoleri opanda masomphenya. Moyo siulendo wawekha. Lolani kuti anthu onse apeze madalitso kudzera mwa inu. Pilirani mazunzo ndizokhumudwitsa kuti mupindulire anthu ena. Musangoganizira za ufulu wanu wokha komanso za udindo wanu.
(e) Mpingo ndiye mwana wokondeka wa Mulungu m’masiku athu ano. Tiyeni titsate zimene Aepiskopi athu akhala akutiphunzitsa mokhudzana ndi ufulu wa demokalase mu zaka zapitazi. Chipembedzo chathu chizitiunikira m’miyoyo yathu. Timalandira mau a Mulungu ndi Ukaristia osati pofuna kukometsa miyoyo yathu yokha komanso ya anzathu.
(f) Mosiyana ndi Petro yemwe sankamvetsa zomwe zinkachitika panthawiyo koma nkumafuna kuti zipitilire, ife, amene tsopano lino tikumvetsa zomwe zidaachitika pa phiri paja, tiyeni tipite patsogolo.
4. MAPHUNZIRO OCHOKERA M’MKALATA ZA AEPISKOPI ATHU
(a) Monga zidachitikira ndi Abraham kuti adauzidwa kuti asiye dziko la kwao, ndi monga adachitira Yesu pakusinthika m’maonekedwe, Aepikopi akuona kuti chisankho chikubwerachi chizatha kusintha zinthu. Malinga ndi momwe tingaitengere nkhaniyi, mwina titha kudzakwaniritsa kusintha zinthu mokomera Amalawi onse, komanso ngati sitisamala titha kutaya mwai wokonzanso dziko lathu (Kulimbikitsa Masomphenya a Komwe Tilikupita, 1st December, 2013, p.16).
(b) Chisankho chapatatu chomwe chikudzachi, chidzatipatsa mwai wolimbikitsa masomphenya akomwe tilikupita. Izi zitanthauza kuchita chisankho mwabata, mwaufulu, mwachilungamo ndiponso kuti tidzasankhe atsogoleri monga Abram ndi Yesu, okhala ndi mtima otumikira anthu modzipereka ndiponso otha kusintha zinthu (Kulimbikitsa Masomphenya a Komwe Tilikupita, 1st December, 2013, p.1).
(c) Sikokwanira kukhala ndi utsogoleri wabwino ngati utsogoleriwo ulibe maziko ake pa mfundo zabwino zokhudza chitukuko cha dziko lonse. Ntchito zina zachitukuko zimatha kuoneka kuti ndi zabwino ndithu ndipo ndi zotha kusintha zinthu m’dziko. Pachifukwa ichi, sikwabino kuti ulamuliro uliwonse uzilowetsa ndale pa ntchito zachitukuko (Kulimbikitsa Masomphenya a Komwe Tilikupita, 1st December, 2013, p.12).
5. ZOYENERA KULINGALIRA
(a) Kodi chikhulupirio chathu chingatithandize bwanji kusintha zinthu m’dziko lathu?
(b) Monga ulendo wa Abram kuchokera ku Haran kupita ku Kenani, monganso ulendo wa Yesu kuchokera ku Galilea kupita ku Yerusalemu unadzetsa madalitso ochuluka ku mitundu yonse, tingatani kuti tisankhe atsogoleri oti mkudzetsa madalitso ochuluka ku dziko la Malawi?
(c) Monga zinachitikira ntchito za Mose ndi Eliya popherezera mwa Yesu, tingatani kuti machitidwe ndi makhalidwe abwino, mfundo ndi ntchito za chitukuko cha dziko la Malawi zisafere m’njira?
(d) Monga zinaliri ndi Abram amene anauzidwa kuti achoke kwao, tingatani kuti tisankhe atsogoleri amene angathe kutumikira dziko lathu modzipereka ndi modziiwala?
23 March, 2014: LAMULUNGU LA 3 MU LENTI
1. CHOLINGA: MOYO WABWINO POZINDIKIRANSO MASOMPHENYA OYAMBA A FUKO LA MALAWI
Mau Oyambirira: Madzi oyenderera amatanthauza moyo. Monga momwe Yesu adaunikira, kuthandiza kuzindikiranso ndi kusandulitsa munthu wa mai uja, amene adali wochimwa ndiponso wosalidwa, pamene adabwera kudzatunga madzi pachitsime, kuti akhale mboni ndi kuthandiza anzake kuti nawonso alandire chipulumutso, tiyeni ifenso tikokere anthu ena kwa Yesu pomudziwa, pomukonda, pomutsatira ndi pomtsanzira Iye.
2. KUMVETSA MAU A LERO
MAU OYAMBA: Eksodo 17: 3 – 7
Pamene Aisraele adavutika ndi ludzu losowa madzi m’chipululu muja, adapemphera kwa Mulungu ndipo Iye adawapatsa madzi ofumila mu m’thanthwe.
SALIMO: 94: 1 – 2, 6 – 9
Tiyeni tisaumitse mitima yathu; tiyeni tikhale anthu omvera. Ngodala amene amamva ndi kuchita zomwe Mau a Mulungu anena.
MAU ACHIWIRI: Aroma 5: 1, 5 – 8
Mtendere ndi chiyembekezo zimathetsa ludzu la mzimu wathu. Mulungu amatipatsa madzi a moyo kudzera mwa Yesu Khristu amene timam’dziwa kudzera mwa Mzimu Woyera.
GOSPEL: Yohane 4: 5 – 42
(a) Pamene Yesu adaapempha madzi akumwa kuchokera kwa munthu wamayi wa Chisamaria, mayiyo adadabwa chifukwa
(i) Ayuda ndi Asamariya ankadana kwambiri
(ii) Mphunzitsi wachiyuda sankaloledwa kulankhula ndi mkazi pagulu la anthu.
(b) Ataunikirikdwa kuti Yesu ndi amene amapatsa madzi amoyo, munthu wamayi uja adapempha madzi amoyowo. Adathandizidwa kuti adzizindikirenso pamene Yesu adamuuza kuti akatenge mwamuna wake. Munthu wamayiyo adayenera kuvomera moyo wake wochimwa womwe adaali nao m’mbuyo ndipo adazindikira kuti Yesu adaali mprofeti. Mosataya nthawi, adayamba kukamba za malo a chipembedzo. Pamene Yesu adamfotokozera kuti chipembedzo choona chimachitika mu mzimu ndi mu m’choona, munthu wamayiyo adadziteteza ponena kuti ndi Messiah amene adzaulule zonsezo.
(c) Pamene Yesu adaulula kuti Iye ndi Mpulumutsi wolonjezedwa uja, munthu wamayi uja adasiya mtsuko wake nafulumira kukaitana anzake a m’mudzi mwake kuti adzakumane ndi Yesu. Yesu atakhala nao kwa masiku angapo, anthu a m’mudzi umenewo adakhulupirira kuti Iye analidi Mpulumutsi wa dziko lapansi.
3. MAPHUNZIRO:
(a) Yesu adabwera kudzayanjanitsa mtundu wa anthu ndi Mulungu, anthu onse pa dziko lapansi ndiponso kudzakometsa ubale pakati pa amuna ndi akazi.
(b) Monga munthu wamayi uja, ifenso timadziwa Yesu pang’onopang’ono ngati:
(i) Munthu womva ludzu wopempha madzi akumwa
(ii) Munthu wolemekezeka
(iii) Mprofeti
(iv) Mpulumutsi wolonjezedwa uja
(v) Mpulumusti wa dziko lonse lapansi.
(c) Yesu adatsata ndondomeko yake yochitira zinthu:
(i) Akuwatenga anthu monga mmene aliri
(ii) Akuwazindikiritsa ulemelero wao
(iii) Akuwasandutsa anthu atsopano
(iv) Akuwakweza kuti akhale ana a Mulungu.
(d) Yesu amatithandiza kuti tidzizindikirenso ndi kupeza masomphenya atsopano
(e) Tikuyenera kukhala anthu atsopano. Kuti izi zitheke, tikuyenera kuchita zotsatirazi:
(i) Kusiya kaganizidwe kathu kakale
(ii) Kusiya mchitidwe wongokhala nkumadalira ena
(iii) Kugawana zisinsi, chimwemwe ndi masomphenya
(iv) Kuthandiza anthu kuti akhale ndi moyo woona, chitukuko cha moyo wonse wa munthu, chimwemwe, mtendere ndi moyo wosefukila.
4. MAPHUNZIRO OCHOKERA M’KALATA ZA AEPISKOPI ATHU
(a) Pamene tidayamba ulendo wathu wofuna kudzilamulira, tinkalakalaka, mwa zina, utsogoleri wolemekeza maufulu a anthu, ndale ndiponso malamulo othandiza kutukula chuma ndi anthu. (Kulimbikitsa Masomphenya a Kumene Tilikupita, 1 December 2013, p. 3)
(b) Amalawi ankafuna dziko lomasuka pa ndale ndi pa chuma. Awatu ndiye masomphenya omwe akupezekanso m’nyimbo ya Fuko lathu. (Kulimbikitsa Masomphenya a Kumene Tilikupita, 1 December 2013, p. 3)
(c) M’kalata yomwe adalemba Aepiskopi pa 29 October 1960, adati: Ndi udindo wathu ndithu kuzindikiritsa anthu onse za malamulo a Mulungu omwe mtundu uliwonse wa anthu uyenera kutsamirapo. Ndi udindo wathunso kuteteza maufulu achibadwidwe a anthu amene adaperekedwa ndi ndi Mulungu ndipo palibe mtsogoleri wina aliyense amene angawalande. (Kulimbikitsa Masomphenya a Kumene Tilikupita, 1 December 2013, p. 3)
(d) Pamene ankathira ndemanga pa masomphenya ndi zofuna za anthu komanso kulimbikitsa Akatolika kuti azitenga nawo mbali pa nkhani ya ndale, Aepiskopi anzathu a m’mbuyomu, sanalowerere m’ndale za chipani, koma adalimbikitsa kayendetsedwe kabwino ka dziko potsamira pa chikondi ndi chilungamo. (Kulimbikitsa Masomphenya a Kumene Tilikupita, 1 December 2013, p. 4)
(e) Zimene ankafuna Aepiskopiwo pano titha kunena kuti zasanduka nsanamira za Malawi watsopano ndipo mfundo zimenezi zidzapitirira kutiwunikira pa udindo umene aliyense ali nawo womanga Fuko la Malawi. (Kulimbikitsa Masomphenya a Kumene Tilikupita, 1 December 2013, p. 5)
5. ZOYENERA KULINGALIRA
Pa 20 May, 2014, Amalawi adzakhala ndi mwai wosankha atsogoleri amene angathe kukonzanso masomphenya a dziko lino.
(a) Tingaphunzirepo zotani pa za m’mene mayi wa chisamaria uja adazindikilira za moyo wake?
(b) Monga Yesu adamuthandizira munthu wa mayi uja kuzindikira kuti kupembedza kwenikweni kumachitika mu mzimu ndi m’choona, ife tichite zotani kuti tizamitse kukhulupirika kwathu?
(c) Kodi ndi masomphenya otani omwe tikufuna kuzindikiranso poyang’anira zomwe makolo athu ankafuna?
(d) Kodi Amalawi onse amawadziwa masomphenya a dziko lino?
(e) Tichite zotani kuti tidzasankhe atsogoleri amene amadziwa ndi kukhulupirira masomphenya a dziko lino?
(f) Nanga tichite chiani kuti Amalawi onse adziwe ndi kuyendera masomphenya a dziko lino?
(g) M’chisankho chikubwerachi, tidzavote bwanji mu mzimu ndi mu choona?
30 March, 2014: LAMULUNGU LA 4 MU LENTI
(AMECEA COLLECTION SUNDAY)
1. CHOLINGA: KUSANKHA ATSOGOLERI A MASOMPHENYA
Mau Oyambirira: Kawirikawiri, timasankha atsogoleri pongoyang’anira maonekedwe ao okha basi. Mau a Mulungu a lero akutiphunzitsa kuti posankha, tiziyang’anira mtima wake wa munthu. Chinthu chachikulu chimene chimachititsa kuti m’Malawi muno mukhale umphawi si kusazindikira kokha ai, koma dyera ndi kudzikonda kwa atsogoleri. Tiyeni tisankhe atsogoleri a masomphenya, ochita zinthu poyera, amene sangodzilemeretsa iwo eni kapena abale awo.
2. KUMVETSA MAU A LERO
MAU OYAMBA: 1 Samuele 16: 1, 6, 10 – 13
Jesse, bambo ake a Davide, adasankhula Eliab ndi abale ake ena kuti akhale atsogoleri a Israele chifukwa cha maonekedwe ao amphamvu, okongola, anzeru ndi otha kuchita zinthu mwa luso. Koma Mulungu adasankhula Davide ngakhale adaali wamng’ono ndi ooneka wonyozeka.
SALIMO: 22
Abusa abwino amatengera nkhosa zao kumene kuli msipu wobiriwira ndipo amazipatsa madzi kuti zithetse ludzu. Poyang’anira zimenezi ndi mmene zinthu ziliri pakati pathu, tikuyenera kuyang’ana ndi kusankha atsogoleri a masomphenya.
MAU ACHIWIRI: Aefeso 5: 8 – 14
Paulo akutilangiza kuti tiyenera kusankha kuwala osati mdima. Kuwala kumaonekera kudzera m’moyo wodzilemekeza, wabwino ndi woona. Ntchito za mumdima ndi monga chinyengo, kuba, mkhalidwe woipa ndi katangale.
GOSPEL: Yohane 9: 1 – 41
(a) Ophunzira adafunsa ngati munthu amatha kuvutika chifukwa cha tchimo lake kapena tchimo la makolo ake? Yesu sakugwirizana ndi kaganizidwe kotere.
(b) Yesu adachiritsa munthu wa khungu pa tsiku la Sabata. Izi zidapatsa mwai a Farisi kuti alowetsemo ndale ndi cholinga chofuna kumpezera chifukwa Yesu. Potsiriza, adangomugwetsa mu mpingo munthu wochizidwa uja chifukwa ankachitira umboni kuti Yesu adali (i) munthu wabwino (ii) mprofeti (iii) munthu wa Mulungu (iv) ndiponso Ambuye.
(c) Abale ndi makolo ake a munthu wochizidwa uja akuchita mantha kuchitira umboni kuti Yesu ndi amene wachiza mwana wao chifukwa nawonso akuopa kuchotsedwa m’chipembedzo cha Chiyuda.
(d) Nkhaniyi ikutha motembenuzika: wakhungu akuona ndipo owona akuchita khungu.
3. MAPHUNZIRO
(a) Monga m’mene adasankhidwira Davide, posankha atsogoleri, tiyeni tiyang’anire mitima yao. Mtima ndi nkhokwe ya (i) zisinsi (ii) kabati ya choonadi (iii) ndiponso Tempile la Mulungu.
(b) Tiyeni tisankhe anthu a makhalidwe odzilemekeza, abwino ndi oyendera choonadi. Mtima wodzaza ndi mdima umabweretsa dyera, zolankhula zoipa, katangale, kuba ndi kuwononga katundu wa dziko ndipo umaika patsogolo zinthu zoipa monga kutaya pakati ndi maukwati a pakati pa amuna kapena akazi okhaokha.
(c) Timulole Yesu kuti atichize ndi kuchotsa khungu lathu kuti tithe kuona ndi kuzindikira atsogoleri amene ali ndi masomphenya ndi amene alibe.
(d) Choona chimatipatsa ufulu. Tiyeni tizinena zoona. Tiyeni tiwulule maganizo athu okhudza anthu amene ali m’maudindo mopanda mantha kapena kuopa.
(e) Tiyeni titsekule maso a anthu kuti athe kuzindikira atsogoleri opanda masomphenya.
4. MAPHUNZIRO OCHOKERA M’KALATA ZA AEPISKOPI ATHU
(a) Sankhani anthu a masomphenya, amene pamodzi ndi anthu amene akuwatsogolera, angathe kukonza zoyenera kukwaniritsidwa zomwe ziyenera kukhala zooneka ndi zotheka zosonyeza zofuna, chiyembekezo ndi maloto a anthu. (Kulimbikitsa Masomphenya a Kumene Tilikupita, 1 December 2013, p. 16)
(b) Mtsogoleri wabwino amadzetsa kusintha ndi kukometsa zochitika pakati pathu. (Kusankha Atsogoleri Athu, 28 December 2003, p. 3)
(c) Chimene Boma labwino lingachite ndi kuonetsetsa kuti nzika zonse za m’dziko ndi magulu osiyanasiyana pakati pathu akuchitapo kathu kuthetsa umphawi pogwira ntchito molimbika. (Tsogolo Lathu Liri M’manja Mwathu, December 2008, p. 3)
5. ZOYENERA KULINGALIRA
(a) Kodi Mau a Mulungu a lero atiphunzitsa zotani pa nkhani yosankha atsogoleri?
(b) Kodi mtsogoleri wa masomphenya amadziwika bwanji?
(c) Tichite chiani kuti tidzasankhe atsogoleri odzilemekeza, a masomphenya ndi okonzeka kuteteza Malamulo a dziko lathu, amene sadzalola zinthu zoipa ngati kutaya pakati, kukwatirana amuna kapena akazi okhaokha, kuvomereza mchitidwe wokana kuti Mulungu alipo, wosawononga chuma cha dziko, wokhala wokonzeka kuwulula katundu amene ali naye?
(d) Tingazindikire bwanji atsogoleri amene angakwaniritse zomwe ife Amalawi timalakalaka?
6th April, 2014: LA MULUNGU LA 5 MU LENTI
1. CHOLINGA: KUSINTHA KUCHOKERA KU IMFA KUPITA KU MOYO
MAU OYAMBIRIRA: Chikhulupiriro chathu chimatitsimikizira kuti ngakhale matupi athu afe tidzakhala moyo mpaka muyaya. Mu Mthenga Wabwino wa lero, poukitsa Lazaro kwa akufa atakhala m’manda kwa masiku anayi, Yesu akuonetsa poyera kuti Atate am’patsa mphamvu zotha kubwezeretsa ndi kusintha ululu wa imfa ndi kubwezeretsanso moyo.
2. KUMVETSA MAU ALERO
MAU OYAMBA: Ezekiele 37:12-14
Mprofeti Ezekiele akupereka chiyembekezo kwa Aisraele omwe ali ku ukapolo ku Babeloni powauza kuti adzabwerera kwawo. Tsopano akuoneka ngati akufa, koma ayembekezere kuti adzaukanso. Mulungu adzawapatsa moyo ndi kuwabwezeretsanso kwawo.
SALIMO: 129
Tiyeni tikhulupirire Mulungu mosayang’anira kukula kwa mavuto athu. Monga momwe Mulungu amatipulumutsira ku msampha wa imfa, adzatipulumutsanso ku moyo wa umphawi ndi mavuto ena.
MAU ACHIWIRI: Aroma 8:8-11
Ngati tadzazidwa ndi Mzimu wa Yesu, Mulungu adzatiukitsa kwa akufa monga adachitira ndi Yesu.
MTHENGA WABWINO: Yohane 11:1-45
(a) Lazaro, Marita ndi Maria anali abwenzi a Yesu, koma Yesu atamva za matenda a Lazaro, sadakamuone nthawi yomweyo. Yesu anafika ku Betania Lazaro atamwalira kale ndipo atakhala m’manda masiku anayi.
(b) Pamene amalandira Yesu, Marita anali ndi maganizo awiri otsutsana:
i) Kufuna kumdzudzula Yesu chifukwa cholephera kubwera kudzamuona nzake akudwala.
ii) Chikhulupiriro kuti Mulungu achita chilichonse chomwe Yesu angamupemphe.
(c) Pamene Yesu adamutsimikizira Marita kuti Lazaro adzauka kwa akufa, Marita adaonetsa chikhulupiriro chozama povomereza kuti Lazaro adzaukadi ndi moyo patsiku lomaliza.
(d) Yesu adaulura kuti Iye anali woukitsa kwa akufa ndi opereka moyo. Izi zitanthauza kuti Yesu ndi Mulungu.
(e) Marita adamuzindikira kuti Yesu ndi Mpulumutsi olonjezedwa uja. Chikhulupiriro ichi ndi chomwe chinapangitsa kuti Yesu aukitse Lazaro kwa akufa.
(f) Nsanje inapangitsa akulu aayuda kuti ayambe ku kukonza zakupha Yesu.
3. MAPHUNZIRO:
(a) Monga mmene Mulungu adalonjozera Aisraele kuti adzawapatsa moyo watsopano, akulonjezanso kuti adzasandutsa Malawi kukhala watsopano.
(b) Tikalora Mzimu Woyera wa Mulungu kukhala mwa ife, ife limodzi ndi atsogoleri athu titha kukhala zida zakusinthika kwa Malawi. Mulungu ndiye mwini moyo poti Iyeyo ndiye moyowo.
(c) Mdima ungakule bwanji, m’bandakucha umabwera basi. Panthawi iyi yamwai, nthawi yachisankho chapatatu, tiyeni tiike moyo m’dziko lathu.
(d) Posalowa m’mudzi muja komanso pomulora Marita kuti anene zakumtima kwake, Yesu anaonetsa poyera makhalidwe a mtsogoleri wabwino. Mtsogoleri woona amathandiza anthu kukhala odzidalira pa moyo wao pogwiritsa ntchito zinthu zomwe ali nazo mwaphindu.
(e) Tiyeni tidzitukule tokha kuchoka mu umphawi kupita m’moyo wosasowa kanthu pokhala anthu ogwira ntchito molimbika.
4. MAPHUNZIRO OCHOKERA M’KALATA ZA AEPISKOPI ATHU
(a) Tikuyenera kusankha “atsogoleri omwe ali wokonzeka, odzipereka ndipo omwe angathe kusintha zinthu m’dziko lathu lino” (Kulimbikitsa Masomphenya a Komwe Tilikupita, 1st December, 2013, p.1)
(b) Tileke khalidwe lofuna “kusintha popanda kukhala osinthika…”(Kulimbikitsa Masomphenya a Komwe Tilikupita, 1st December, 2013, p.7)
(c) Tikusowa atsogoleri omwe amalemekeza “malamulo a dziko”; opanda khalidwe “losakasaka anzawo pofuna kuwapezera milandu ndi kuwamanga popanda zifukwa zokwanira”; opanda khalidwe “loika kumbali ndi kuthaniratu ndi opikisana nawo pa ndale”; opanda khalidwe “logwiritsa ntchito mphamvu zawo mokomera iwo eni pamene alowa m’boma; koma akhalidwe lotekeseka ndi zosowa za anthu komanso osamala bwino chuma cha dziko” ndi oyendetsa bwino ntchito zakagawidwe ka chumacho; opanda khalidwe “logwiritsa ntchito ndi kuba chuma cha dziko ndi cholinga cholemeretsa zipani zawo ngakhalenso iwo eni” (Kulimbikitsa Masomphenya a Komwe Tilikupita,1st December, 2013, p.7-8)
(d) Tisankhe atsogoleri omwe alibe khalidwe “longodalira thandizo la maiko akunja” (Kulimbikitsa Masomphenya a Komwe Tilikupita,1st December, 2013, p.9)
(e) Dziko lathu lino likusowa “utsogoleri wapamwamba ndi wamasomphenya” (Kulimbikitsa Masomphenya a Komwe Tilikupita, 1st December, 2013, p.10)
(f) Tikuyenera kusankha atsogoleri omwe amalimbikitsa “mapulani achitukuko cha dziko lonse” (Kulimbikitsa Masomphenya a Komwe Tilikupita,1st December, 2013, p.10)
(g) Pachifukwa ichi, Mulungu akulimbikitsa utsogoleri wamasomphenya, wothandiza kusintha zinthu, othandiza ena kutha kupanga zinthu modzidalira, wosamalira, otumikira, woteteza, woganizira anthu ndi omvera Iye. (Kulimbikitsa Masomphenya a Komwe Tilikupita,1st December, 2013, p.10-11)
(h) Zotere zikutipempha kukhala ndi atsogoleri apamwamba ndithu omatha kuiwala zokonda zawo pofuna kulimbikitsa ubwino wa anthu onse (Kulimbikitsa Masomphenya a Komwe Tilikupita, 1st December, 2013, p.11)
(i) Mtsogoleri wabwino akhale ndi makhalidwe awa: masomphenya, kapitawo wabwino, wopereka zitsanzo zabwino, olemekeza malamulo a dziko ndi mphamvu za malamulo, wosamala bwino chuma cha dziko, wotsatira mfundo za demokalase, ndipo akhale oopa Mulungu (Kulimbikitsa Masomphenya a Komwe Tilikupita, 1st December, 2013, p.14-15)
(j) Mtsogoleri akhale okonzeka kusandutsa Malawi kukhala watsopano, kusintha zinthu pofuna kusintha miyoyo ya anthu osangosintha mopanda cholinga (Kulimbikitsa Masomphenya a Komwe Tilikupita, 1st December, 2013, p.15).
5. ZOYENERA KULINGALIRA
(a) Monga momwe Aisraele adapezera moyo watsopano pomasulidwa kuchoka muukapolo, tingabweretse bwanji chiyembekezo kwa Amalawi ambiri amene agwidwa mu umphawi, kusadziwa kulemba ndi kuwerenga, kutaya mtima, kudalira chithandizo cha maiko akunja, kungodalira zogawagawa ndi kumangoombera mmanja zilizonse?
(b) Kodi chikhulupiriro chathu mwa Yesu ngati wodzodzedwa wa Mulungu, Mwana weniweni wa Mulungu wa moyo, chingatithandize bwanji kuti tisinthe miyoyo yathu?
(c) Ndi maphunziro ati amene tingapeze kuchokera mzimene akutiphunzitsa Aepiskopi athu pa nkhani ya utsogoleri wotha kusintha zinthu?
13 April, 2014: LA MUMULUNGU LA KANJEDZA
1. MUTU: KUPAMBANA KOBWERA KUDZERA M’MASAUTSO NDI KUONA YESU MWA ANTHU OSAUKA
MAU OYAMBIRIRA: Mzeru zathu za umunthu sizingakwanitse kumvetsa kwathunthu chisinsi cha chipulumutso chathu: kupeza moyo kudzera mu imfa; ulemerero kudzera mkunyozedwa kotheratu; kukwezedwa kudzera mkutsitsidwa; kupambana kudzera mkugonja; Chiyanjano kudzera mkukanidwa. Yesu sadabwere kudzathetsa masautso ndi imfa koma kudzationetsa njira yoyenera kutsata pamene takomana ndi masautso ndi imfa.
2. KUMVETSA MAU ALERO
MAU OYAMBA: Yesaya 50: 4-7
Iyi ndi nyimbo yachitatu ya Mtumiki wa Mulungu. Ngakhale akukomana ndi mavuto ambiri, mtumikiyo sakutaya chikhulupiriro chake mwa Mulungu.
SALIMO: 21:8-9, 17-20, 23-24
Tikakomana ndi mavuto timaganiza kuti Mulungu watiiwala. Komabe, tidziwe kuti vuto liri lonse pamoyo wathu ndi laphindu. Mulungu amatiyesa kuti atilimbitse m’chikhulupiriro.
MAU ACHIWIRI: Afilipi 2:6-11
Monga momwe Yesu adadzichepetsa nadzipanga kukhala kapolo wotifera ife pamtanda, nafenso tikhale nalo khalidwe lakudzichepetsa pokhala atumiki a anthu onse.
MTHENGA WABWINO: Mateyo 26:14-27, 66
(a) Anthu ngodabwitsa: lero akuimba “Hosanna”, pa Lachisanu Loyera adzakuwa, “mpachikeni pa mtanda”!
(b) Yudasi sakumutchula Yesu kuti “Ambuye” akumutchula “Aphunzitsi”kungoonetsa kuti alibe chikhulupiriro ndipo choncho ndi amene adzapereke Yesu kwa adani ake.
(c) Ngakhale kuti mkulu wa ansembe, Kaifa anali ndi mphamvu zotha kupulumutsa Yesu m’manja mwa adani ake, akuopa Ayuda anzake, Aroma komanso akuopa kuchotsedwa ntchito. Kumbukirani kuti ndi Kaifa yemweyu amene anayambitsa malonda anyama zoperekera nsembe ndi ndi mchitidwe wosintha ndalama mu Tempile.
(d) Yesu akuoneka munthu wosowa chitetezo komanso munthu oponderezedwa.
(e) Ku bwalo la Pilato, bwalo lalikulu loweruza milandu pakati pa Ayuda lidasintha mlandu wa Yesu kukhala woukira boma pamene poyamba amamuimba mulandu wonyoza Mulungu:
(i) Kumemeza anthu kuti aukire boma
(ii) Kulimbikitsa anthu kuti asamakhome msonkho
(iii) Amadzitchila yekha “mfumu”
(f) Pilato anali katswiri kwambiri pa nkhani za ndale:
(i) Anazindikira kuti mulandu wa Yesu unali Msampha
(ii) Adafuna kuti apulumutse Yesu pomufunsa ngati analidi mfumu ya Ayuda
(iii) Anayesanso kupulumutsa Yesu pomupereka kuti amutulutse mmalo mwa Barabba
(iv) Anasamba m’manja mwake nalamula kuti Yesu akwapulidwe
(g) Pogonjera maganizo a atsogoleri awo, nzika za dziko zinasankha kupulumutsa Barabba osati Messiah. Tsiku ili, tchimo lidapambana.
(h) Mau oti INRI akutanthauza, “Yesu waku Nazarete mfumu wa Ayuda” ngakhale anachitiridwa chipongwe choopsa: Kuperekedwa kwa adani ake, kukanidwa, kuimbidwa mlandu ku bwalo la kukhothi, nsanje, kaduka, kukwapulidwa, kuzunguzidwa ponseponse, kusenza mtanda, kuvulidwa zovala, kupachikidwa pa mtanda, kukuwizidwa, imfa yamanyazi yapamtanda.
(i) Yesu adamva ululu ndipo mzimu wake unawawidwa kwambiri:
i. Bwenzi lake Yudasi ndiye adamupereka kwa adani ake.
ii. Bwenzi lake lina Petro anamukana
iii. Ophunzira ake ena onse anamuthawa
iv. Akulu achipembedzo sadangolephera kumumvetsa komanso anapangana zakuti amuphe.
v. Anthu amene sadaali Ayuda adamupachika ngati munthu woukira.
vi. Amanva ngati Atate ake a kumwamba amutaya.
vii. Anthu odutsa panjira yapafupi ndi pomwe Yesu adapachikidwa anali kum’nyoza.
(j) “Mulungu wanga, Mulungu wanga…” Salimo imeneyi imayamba ndi dandaulo koma imatha ndi mau wotamanda ndi kuthokoza Mulungu. Popemphera salimo imeneyi, Yesu akutsimikiza kuti Iyeyo ndiye Mtumiki wa Ambuye amene akudzipereka yekha ngati nsembe kwa Mulungu ndi cholinga chopulumutsa abale ndi alongo ake.
3. MAPHUNZIRO:
(a) Nkhani ya Masautso a Yesu ikutiphunzitsa kuti masautso ndiyo njira yofikira ku ulemerero. Popanda thukuta palibe zokoma.
(b) Pakuti Iye mwini adasaukapo, Yesu amakhala mbali ya anthu omwe akuzunzika namayenda nawo m’masautso awo.
(c) Tichenjere, kampeni itha kupotoza mzika za dziko kusankha munthu oipa/wamilandu ndikukana mtsogoleri wabwino yemwe angathe kuthandiza kuti zinthu zisinthe.
(d) Yemwe angathedi kukhala mtsogoleri wabwino ndi amene ali wokonzeka kupeza masautso chifukwa cha ubwino wa anthu ena.
(e) Tiyeni tisagulitse maziko a moyo wathu pofuna kukondweretsa ena. Tiyeni tikane maukwati a amuna kapena akazi okhaokha, kutaya mimba, njira zamakono zakulera komanso chiphunzitso chakuti Mulungu kulibe.
4. MAPHUNZIRO OCHOKERA M’KALATA ZA AEPISKOPI ATHU
(a) Ngakhale masiku ano, anthu amene ali pa chiopsezo ndi amenenso ali osauka, asowa kuyang’aniridwa mwapadera. Chifukwatu kunena zoona, ife tikudabwa kuti zikutheka bwanji kuti mpaka masiku ano anthu akufabe ndi njala, akupitilira kukhalabe osaphunzira sukulu, akusowabe thandizo la makhwala, ndipo alibe nyumba zabwino zogonamo? (Kulimbikitsa Masomphenya a Komwe Tilikupita,1st December, 2013, p.13).
(b) Mfundo zoyendetsera dziko zizikhala zoganizira anthu osauka ndipo zionetsetse kuti chuma sichikukhala m’manja mwa anthu ochepa okha (Kulimbikitsa Masomphenya a Komwe Tilikupita, 1st December, 2013, p.13).
5. ZOYENERA KULINGALIRA
(a) Mau a Mulungu a lero akutipatsa maphunziro otani pa nkhani zoganizira amphawi ndi oponderezedwa?
(b) Mu nkhani ya masautso a Yesu, ndi maphunziro ati omwe tikupeza pa mutu wa:
(i) Kumpereka munthu kwa adani ake
(ii) Mphamvu za satana zomwe zimayesetsa kuti chilungamo chisaoneke
(iii) Mphanvu, udindo komanso kukhala ndi chuma
(iv) Mantha pankhani yoimira amphawi ndi anthu opanda chitetezo
(v) Kugwiritsa ntchito mphamvu za ndale molakwikwa pofuna kudzipezera zokonda za iwe mwini
(vi) Kumvera kopanda nako udindo pakati pa asilikali ankhondo
(vii) Anthu ambiri kupotozedwa kuti asankhe zinthu zoipa.
(c) Kodi ndondomeko zathu, malamulo athu ndi mapulani omwe timakonza oyendetsera dziko lino ndi zoimiriradi amphawi?
(d) Tingachite chiani kuti tithandizepo pantchito zotukula miyoyo ya anthu osauka m’Malawi?
(e) Ndi mfundo ziti zomwe Malawi monga dziko angatsate kuti zikweze miyo ya anthu osauka?
20th April, 2014: LA MULUNGU LA PASAKA
1. CHOLINGA: KUUKA KWA YESU KWA AKUFA
MAU OYAMBIRIRA: Kuuka kwa Yesu kwa akufa ndiye chithimethime chachikhristu. Kudzera mu kuuka kwake, Yesu akusandutsa manyozo onse ofera pa mtanda kukhala kupambana kwa moyo. Popeza kuti Yesu adauka kwa akufa, timakhulupirira kuti ifenso tidzauka kwa akufa. Yesu ouka kwa akufa amabwera kwa ife mu njira zosiyanasiyana ndipo amatiitana kuti titenge nawo mbali m’moyo wake. Chikondi ndiye chinthu chofunika koposa pamene ifeyo tikutenga nawo mbali m’moyo wa Yesu.
2. KUMVETSA MAU ALERO
MAU OYAMBA: Ntchito 10:34; 37-43
Petro akupereka chidule cha kumvera kwathu motere:
(a) Yesu adali munthu ndithu ndipo adayendayenda uku ndi uku kuchita zabwino
(b) Mphamvu za Mulungu zimasintha dziko lapansi kudzera mwa Yesuyo
(c) Ayuda adamupha Yesu pomupachika pamtanda
(d) Mulungu adamuukitsa kwa akufa
(e) Apostoli ndiye mboni ya zimenezi
(f) Tikupemphedwa kuleka kuyenda m’njira zathu zoipa ndi kuyamba kukhala moyo wosonyezadi kuti ndife anthu wooukitsidwa kwa akufa.
SALIMO: 117:1-2, 16-17, 22-23
Popeza kuti kuuka kwa Yesu kwa akufa ndiye tsinde lachikhristu, Lamulungu la Pasaka ndi tsiku lopambana masiku ena onse mu kalendala yachikhristu. Pa tsiku ili, Yesu, mwala omwe amisiri omanga nyumba adaukana, udasanduka wapangodya.
MAU ACHIWIRI: Akolose 3:1-4
Ubatizo udatiyambitsa moyo watsopano womwe udzafike pake penipeni osati m’moyo uno koma kumwamba. Kuti tiyeneredi kulandira moyo umenewu, chikhulupiriro chathu chiyenera kuyenda limodzi ndi ntchito zathu zabwino.
MTHENGA WABWINO: Yohane 20:1-9
(a) Chikondi komanso kulimba mtima ndizo zidapangitsa Maria Magadala kulawilira kwambiri mmawamawa kupita ku manda a Yesu. Ataona kuti mwala otsekera pa khomo la manda wachotsedwapo, maganizo awiri adamufikira:
(b) Akuba aba thupi la Yesu ndi kuthawa nalo
(c) Akulu a Ayuda alitengera thupi la Yesu ku malo ena kuti akaliononge ndi kulinyoza koposa
(d) Izi zinali zovuta kuti azimvetse nchifukwa chake adathamangira kwa Petro ndi Yohane. Petro anali mtsogoleribe pakati pa okhulupirira ngakhale anali atamukana Yesu katatu. Yohane anali wophunzira yemwe Yesu ankamunkonda kwambiri.
(e) Zodabwitsa kwambiri pakati pa Ayuda omwe samakhulupirira umboni wa azimai, ophunzira awiri aja adathamanga kupita kumanda a Yesu kuja modalira umboni wa munthu wamayi. Yohane ndiye adafika pa mandapo msanga komabe adapereka mwai kwa Petro kuti atsogolere mwambo olowa m’mandamo;
(f) Ngakhale Petro ndi Yohane adaona umboni wofanana wakuuka kwa Yesu, Yohane ndi amene anaona nakhulupirira kuti moyo wagonjetsadi imfa.
3. MAPHUNZIRO:
(a) Yesu wouka kwa akufa adakweza ulemerero wa amai pakati pa Ayuda pamene adamupanga Maria Magadala kukhala mboni yakuuka kwake pamaso pa Apostoli;
(b) Maria adakhudzidwa ndi mmene Yesu adafela; adaonetsa kumvera ndi kukhulupirika pothamanga kupita kumanda ndipo kenaka kuthamanga kupita kwa ophunzira a Yesu. Nawonso Ophunzira a Yesu adakhudzidwa ndithu nathamanga kupita ku manda a Yesu.
(c) Timapembedza Lamulungu osati Loweruka chifukwa ndilo tsiku limene Ambuye Mulungu adaukitsa Yesu kwa akufa ndipo potsatira izi, Iye amaonekera kwa ophunzira ake pambuyo pakuuka kwa akufa ndipo izi zimachitika Lamulungu lokhalokha (Yohane 20:19, 26; 21:1). Mzimu Woyeranso anatsikira pa ophunzira ake (Pentetcost) patsiku Lamulungu (Ntchito 2:1).
(d) Chikhulupiriro ndi chikondi ziyenera kuyenda limodzi. Pogwiritsa ntchito maso achikhulupiriro tiyenera kuona nkhope ya Yesu mwa anthu omwe ali njala, ludzu, m’ndende, osauka, ana amasiye, odwala, osowelatu pogwira komanso anthu osalidwa pazifukwa zosiyanasiyana. Chikondi chiyenera kutipangitsa ife kuchita ntchito zathu mwachifundo ndi mwachilungamo.
(e) Tiyeni tonse tidzifanizire ndi anthu atatuwa:
i) Maria Magadala anali ochimwa koma anasintha atakumana ndi Yesu. Zotsatira zake zidasonyeza kuti chikondi chake pa Yesu chidakula kuposa cha onse
ii) Petro anali munthu waphuma kwambiri pochita zinthu koma anadzipereka kwathunthu kwa Yesu; ngakhale anamukana Yesu katatu Yesu sadamulande udindo wokhala mtsogoleri wa Apostoli.
iii) Yohane anali wophunzira amene Yesu ankamkonda kwambiri. Chikondi ndi chimene chinatsekula mtima wake kuti akhulupirire kuti yesu adaukadi kwa akufa.
(f) Utsogoleri umathandiza ena kuti agwire ntchito molimbika mwinanso moposa mphamvu zawo. Atsogoleri okonda dziko lawo amathandiza anthu kukhala otukuka pa mbali zonse zokhudza moyo wao. Atsogoleri osakonda dziko lawo amamanga ulamuliro wawo pa bodza, umbava, ziphuphu, ulesi, malonjezo onama, komanso kuvomereza zoipa komanso malamulo oipa.
(g) Tikupemphedwa kuti tifufuze atsogoleri okonda dziko lawo, ndipo amene ali okonzeka kufera dziko lawo osati kuliononga.
4. MAPHUNZIRO OCHOKERA M’KALATA ZA AEPISKOPI ATHU
(a) Monga akhristu, tikuyenera kudziwa kuti dziko lathu lino ndi gawo limodzi la dziko lonse lapansi lomwe timakhalamo. Ili dziko lomwe latithandiza kulandira zaulere zosawerengeka za thupi komanso zauzimu. Nzika iliyonse ikuyenera kukonda dziko lake monga momwe mwana amakondera mayi wake (Tingamange bwanji dziko lachimwemwe, 1961).
(b) Ndi mtima womwewu wokonda dziko lathu, tikukupemphani ngati akhristu kuti mutenge nawo mbali modzipereka ndi modziwa zomwe mukuchita pa ntchito yomanga dziko lino. Voterani anthu ambiri yabwino posayang’anira chigawo chomwe akuchokera, mtundu wao, chilankhulo, chipani chawo cha ndale kapena mpingo wawo. Malawi akusowa atsogoleri okonda dziko lawo, anthu amene amaika patsogolo ubwino wa dziko asanayambe kuona ubwino wa iwo eni (Tingamange bwanji fuko lachimwemwe, 1961).
(c) Mkhalidwe wowononga chuma cha dziko ndiponso katangale zomwe zakula pakati pathu masiku ano, zikusonyezeratu poyera kuti tilibe mtima wokonda dziko lathu. Kukonda dziko lathu masiku ano, kumatanthauza: kukhala ndi ufulu wolembetsa mkaundula wa voti ndiponso kuvotera atsogoleri abwino. Kumatanthauzanso kutengapo gawo pa ntchito zachitukuko cha dziko lathu ndi kuonetsetsa kuti atsogoleri amene tawasankha akugwiradi ntchito yao motumikira anthu mwachikondi ndi mwachilungamo (Kulimbikitsa Masomphenya a Komwe Tilikupita, 1st December, 2013, p.13).
(d) Kukonda dziko lathu moona ndi molondola kutanthauza kupewa izi:
i) Mkhalidwe wofuna kupeza zolakwa mwa ena ndi kuwamanga popanda kufufuza bwino kapena tisanafufuze chilungamo chake cha nkhani pofuna kulepheretsa ena kupikisana nawo pachisankho;
ii) Mkhalidwe wosafuna kuchitapo kanthu, kuchita zinthu mobisa ndi kusagwiritsa ntchito bwino katundu waboma;
iii) Kugwiritsa ntchito mphamvu molakwikwa ndi kuononga katundu waboma pofuna kulemeretsa zipani kapena iwo eni mosakomera dziko;
iv) Kulowetsa ndale pa nkhani yaumphawi ndi kugwiritsa ntchito anthu osauka molakwika powagawira zinthu m’malo mowalimbikitsa kuti akhale odziimira paokha.
(e) Kudalira udyo mabungwe ndi abwenzi opereka thandizo omwe amapereka chithandizo chaocho pofuna kukwaniritsa zofuna zawo zomwe zimatikakamiza ife kutaya chikhalidwe chathu (Kulimbikitsa Masomphenya a Komwe Tilikupita, 1st December, 2013, pp.9-10).
5. ZOYENERA KULINGALIRA
(a) Kodi kuuka kwa Yesu kwa akufa ndi tsinde la moyo wachikhristu bwanji?
(b) Monga Maria Magadelena uja, amayi angachitepo zotani pofuna kutenga nawo gawo mzinthu zofunikira pakati pathu?
(c) Tchulani mavuto amene dziko lathu likukumana nawo ndiponso zimene zalembedwa m’kalata ya Aespiskopi yapitayi zomwe zingalepheretse anthu kukonda dziko lawo.
(d) Ndani amene akukhudzidwa kwambiri ndi mavuto amene atchulidwa pamwambawa?
(e) Tchulani makhalidwe amene mudzayang’anire posankha atsogoleri amene ndi oona, okhululupirika ndi okonda dziko lawo.
(f) Poyang’anira chisankho chapatatu chikubwerachi, tingachite chiani kuti tilimbikitse mfundo zothandiza kusintha dziko lathu ndipo tingatani kuti tipewe mfundo zodzetsa mavuto ndi nkhawa pakati pathu?
27 April, 2014: LAMULUNGU LA 2 LA PASAKA
1. CHOLINGA: CHISANKHO CHA MTENDERE NDI BATA
Mau Oyambirira: Mphatso yoyamba yoperekedwa ndi Ambuye Yesu wouka kwa akufa kwa okhulupirira Iye ndiponso kwa mtundu wonse wa anthu ndi mtendere. ‘Mtendere ukhale nanu’ ndiye anali mau ake ngati malonje pamene anakumana koyamba ndi ophunzira ake atauka kwa akufa. Mau amenewa adasanduka malonje a mafuno abwino amene akhristu amafunirana pa nthawi ya Nsembe ya Misa yotikumbukira Misteri ya Pasaka yomwe – Chipulumutso chathu. Kuposa kale lonse, mtundu wa anthu masiku ano ukusowa mtendere womwe ndi mtendere wam’maganizo, mtendere wamumzimu, mtendere wamumtima ndinso makamaka mtendere wam’dziko umene tingathe kuupeza pokhapokhapo tilumikizana ndi Yesu Mfumu ya mtendere.
2. KUMVETSA MAU A LERO
MAU OYAMBA: Ntchito 2: 42 – 47
Ena mwa makhalidwe a Akhristu oyamba anali awa: (i) kukhulupirika, (ii) kugawana zomwe aliyense anali nazo ndi anthu osowa, (iii) kupemphera pamodzi (iv) ndi kusangalira pamodzi.
SALIMO: 117: 2 – 4, 13 – 15, 22 – 24
Tiyeni tithokoze Mulungu amene amatipulumutsa ku mavuto osiyanasiyana. Tikuyenera kukhala nzika zodalirika m’dziko ndi Akhristu abwino mu Mpingo.
MAU ACHIWIRI: 1 Petulo: 1: 3 – 9
Tikuyenera kukhala mboni zenizeni za Yesu. Monga Yesu adazunzika, ifenso tidzayesedwa ndi mayesero owawa ngati moto. Titabadwanso kachiwiri mu ubatizo, tiyeni tichite izi: (i) kukhala ndi chikhulupiriro (ii) kufunafuna chuma cha m’dziko lachilonjezo (iii) tizichita zinthu ngati anthu amene adapulumutsidwa. Yesu adafafaniza machimo, zowawa ndi kufooka kwathu. Ngakhale kuti sitinamuone, tiyeni tikule m’chikhulupiriro.
GOSPEL: Yohane 20: 19 – 31
(a) Yesu anaonekera Ophunzira pa tsiku lotsatira Sabata ya Ayuda. Adawalonjera ndi mafuno a mtendere nawauzira mpweya. Izi ndi zizindikiro zosonyeza kuti Yesu wouka kwa akufa akulenganso mwatsopano. Moyo watsopanowu udzaonekera pokhululukirana.
(b) Tomasi adakaniratu kwathunthu kukhulupirira kuti Yesu adauka kwa akufa mpaka atadzionera yekha. Pa Lamulungu lotsatira, Yesu adadzionetsa kwa Tomasi. Atangomuona Yesu, Tomasi adasonyeza chikhulupiriro chachikulu ngati m’mene adaonetseranso kusakhulupirira kwake masiku am’mbuyo.
(c) Yesu adati, ‘ngodala amene akhulupirira ngakhale sanaone’
3. MAPHUNZIRO
(a) Munthu aliyense amasowa anzake kuti akhale ndi moyo. Ife tonse tikupemphedwa kutsanzira chitsanzo cha moyo wa Akhristu oyamba aja.
(b) Mtendere, ngati mphatso yoyamba ya Khristu wouka kwa akufa ndi wofunikira pa chikhulupiriro chathu cha Chikhristu.
(c) Monga Yesu adapatsa ophunzira ake moyo watsopano powauzira mpweya, ntchito yathu ndi kuthandizana ndi Mulungu polenganso ndi kukometsa dziko la pansi.
(d) Monga Tomasi uja, tiyeni tisonyeze poyera ngati tili ndi chikaiko ndipo pamene taunikiridwa, tiyeni tilimbenso mtima posonyeza poyera chikhulupiriro chathu.
(e) Tiyeni tisankhe atsogoleri athu mozindikira ndi mwanzeru kuti tidzamange Malawi watsopano pa thanthwe la chikhulupiriro, chikondi, umodzi, choona ndi chilungamo.
4. MAPHUNZIRO OCHOKERA M’KALATA ZA AEPISKOPI ATHU
(a) ‘Pamene tidayamba ulendo wathu wofuna kudzilamulira, tinkalakalaka, mwa zina, utsogoleri wolemekeza maufulu a anthu, ndale ndiponso malamulo othandiza kutukula chuma ndi anthu.’ Mtendere ndi chinthu chimodzi chimene ife tinkalakalaka monga momwe Nyimbo ya Fuko lathu ikufotokozera: ‘Mulungu dalitsani Malawi, mumsunge mtendere.’ (Kulimbikitsa Masomphenya a Kumene Tilikupita, 1 December 2013, p. 3)
(b) Banja, boma ndiponso Mpingo ziyenera kugwirira ntchito limodzi mogwirizana kuti anthu apezedi chitukuko chenicheni komanso chimwemwe chodzaza. (Kumanga Tsogolo Lathu, 1994)
(c) Alipo ena pakati pathu amene amakana zofuna za demokalase zimene anthu ambiri amafuna. Mchitidwe wotere ndi woopsa ndipo tiyenera kuukaniratu kwathunthu pakati pathu. Demokalase ikalephera, zotsatira zake zimakhala chipwirikiti. (Kumanga Tsogolo Lathu, 1994, p. 12)
(d) Amene amapambana pa chisankho, olamulira ndi otsatira ao onse, atha kugwa m’chinyengo chomanyoza amene amaganiziridwa kuti alephera. Kukondwerera udyo kwa amene apambana chisankho kutha kuyambitsa udani ndi kugawikana pakati pathu. Pali zitsanzo zokwanira kuchokera m’maiko ena za momwe zinthu zinavutira molakwika. (Kumanga Tsogolo Lathu, 1994, p. 12)
(e) Mtendere utha kukhalapo pokhapokhapo ngati ife tonse tisonyeza mtima womvetsetsana ndi kupititsa patsogolo khalidwe la chilungamo pakati pathu. (Kumanga Tsogolo Lathu, 1994, p. 14)
(f) Kaganizidwe koti ‘opambana, zonse ndi zake’ kaliponso pakati pathu. Pachifukwa ichi, opambana amaganiziridwa pa zinthu zambiri pamene amene alephera amaponderezedwa. Izi zimatha kubzala mbeu ya udani ndipo potsiriza zitha kuwononga demokalase. (Kumanga Tsogolo Lathu, 1994, p. 14)
(g) Mtendere sungakhalepo ngati amene atenga udindo wolamulira sakufuna kuchitapo kanthu kuti anthu azikhala moyanjana ndinso polamulira mosakondera. (Kumanga Tsogolo Lathu, 1994, p. 14)
(h) Sitingayembekezere kuti boma lingakwaniritse zolinga zake pokhapokhapo ngati ifenso tili okonzeka kuchitapo kanthu…Ngati sitidzipereka pogwira ntchito zathu, sitingathe kumanga dziko la mtendere ndi chilungamo. (Kumanga Tsogolo Lathu, 1994, p. 14)
(i) Masomphenya a Malawi, monga ikufotokozera nyimbo ya Fuko lathu, ndi otsamira ndiponso odalira chithandizo cha Mulungu. Ndife Fuko lokhulupirira Mulungu; choncho zolakalaka zathu ndi maloto athu akutsogolo zikhale ndi maziko ake m’chikhulupiriro mwa Mulungu. (Kulimbikitsa Masomphenya a Kumene Tilikupita, 1 December 2013, p. 3)
(j) Tikuyenera kupemphera mwamphamvu: kuyambira nthawi yokonzekera, panthawi yovota ndiponso chitatha chisankhocho. Pamene tizipemphera, tikumbukirenso kusala ndi kudzilanga. Amayi Maria Wodala Mfumu ya Mtendere, atimpherere ife ndi Fuko lathu. (Kulimbikitsa Masomphenya a Kumene Tilikupita, 1 December 2013, p. 22)
5. ZOYENERA KULINGALIRA
(a) Pozindikira kuti mtendere ndi mphatso yofumira kwa Yesu Khristu wouka kwa akufa, ife tingakhale bwanji zida zodzetsa mtendere umunewu ngati ophunzira ake?
(b) Tingatsimikize bwanji chikhulupiriro chathu mwa Khristu wouka kwa akufa pamene pakati pathu pali ambiri ochita mantha ndi nkhani za umfiti ndi satanic?
(c) Ndi zinthu zotani pakati pathu zomwe zingadzapangitse kuti zipolowe zibuke (makamaka nthawi ya chisankho) ndi kusokoneza mtendere womwe tili nao m’Malawi muno?
(d) Tichite zotani ndi aneneri ongofuna kupezerapo mwai nthawi ya chisankhoyi?
(e) Monga Yesu wouka kwa akufa amapereka moyo watsopano kwa ife, nanga ifeyo tichite zotani kuti tisandutse Malawi kukhala watsopano?
(f) Kodi achinyamata angapewe bwanji kugwiritsidwa ntchito pa nkhani ya zipolowe ndipo tichite zotani kuti zimenezi zisadzachitike?
(g) Nanga ‘opambana’ ndi ‘oluza’ adzachite zotani pambuyo pa chisankho pofuna kupewa zipolowe?
4 May, 2014: LAMULUNGU LA 3 LA PASAKA
1. CHOLINGA: KUTSEKUKA POFUNA KUMANGA UFUMU WA MULUNGU
Mau Oyambirira: Monga ophunzira awiri aja amene anali pa ulendo wochoka ku Yerusalemu kupita ku Emmausi, ifenso tili pa ulendo wochokera pansi pano kupita ku Kumwamba. Ulendo wathu udzakhala watanthauzo ndi cholinga ngati tiyenda pamodzi ndi Yesu Khristu. Tiyeni timuuze Yesu nkhawa ndi madandaulo athu onse. Tiyeni timulolenso Yesu kuti atsekule maganizo ndi mitima yathu kudzera m’Mau a Mulungu ndiponso m’Buledi wamoyo.
2. KUMVETSA MAU A LERO
MAU OYAMBA: Ntchito 2: 14, 22 – 24
Pa tsiku la Pentekosite, Petulo adagwiritsa ntchito Salimo 16 polalika uthenga wa Chikhristu. Adafotokozera za kusauka, imfa ndi kuuka kwa Yesu. Ngati ife tikhulupirika kwa Ambuye, tidzayenda m’njira yopita kumwamba.
SALIMO: 15: 1 – 2, 5, 7 – 11
Tonse tikusowa kuwala. Tiyeni tilole Mulungu kuti atiwunikire posankha atsogoleri athu.
MAU ACHIWIRI: 1 Petulo: 1: 17 – 21
Tikuyenera kukhala ndi moyo ndi makhalidwe odzilemekeza. Kunyada ndi makhalidwe ena oipa zimaononga ndi kupangitsa Fuko lonse likhale ngati loola.
GOSPEL: Luka 24: 17 – 24
(a) Mthenga Wabwino walero ukutiphunzitsa kukhulupirira koyenera mwa njira izi: (i) tifotokoze nkhawa zathu ndi kuthandizana (ii) tizimvetsera Mau a Mulungu (iii) tizikonda kulandira Ukaristia
(b) Kleopasi ndi mzake uja adanyamuka kuchokera ku Yerusalemu kupita ku Emmausi atakhumudwa. Ankayendera pamodzi ndi mlendo wofuna kudziwa ndi kumvetsa zinthu. Atamufotokozera maganizo a chiyembekezo chao cholakwika chokhudza Messia, Yesu akudabwa chifukwa cha kusadziwa kwao ndipo adayamba kuwatambasulira Mau a Mulungu kuti amvetse bwino tanthauzo la masautso, imfa ndi kuuka kwa Yesu.
(c) Mau a Yesu sadangotsekula maganizo a ophunzira aja chabe komanso mitima yao idatsekuka. Adamuitana Yesu kuti akagone ku nyumba kwao ndipo Yesu adatsekulanso maso awo ponyema buledi.
(d) Pamene ophunzira awiri aja adabwerera ku Yerusalemu kuti akagawane ndi anzao za Uthenga Wabwinowu, adakapeza kuti otsala ajanso akudziwa kale kuti Yesu adauka chifukwa adaonekera Petulo.
3. MAPHUNZIRO
(a) Ngati anthu amene timasowa anzathu pa moyo wathu, kuchitira limodzi ndi anzathu ndiye gwelo la mphamvu zathu.
(b) Timange moyo wathu pa Ambuye Yesu amene adaali mwala umene amisiri adaukana koma udasanduka mwala wapangodya.
(c) Tiyenera kulemekeza ulemelero wa moyo wa munthu pakupemphera modzipereka ndi pokhala ndi makhalidwe a umunthu.
(d) Tizipemphera m’choona ndi mu mzimu pomufotokozera Mulungu zimene tili kumva monga chimwemwe, nkhawa, chisoni, ndi zina zotero.
(e) Timange moyo wathu pa Mau a Mulungu ndi pa masakalamenti makamaka Sakalamenti la Ukaristia.
(f) Tiyeni tikhale nawo mtima wofuna kugawana ndianzathu Mthenga Wabwino.
(g) Monga Petulo adaali woyamba kuwukitsidwa kwa akufa ndi Khristu wouka kwa akufa pamene adasintha kukana kwake kuti kusanduke chikondi, machismo athu asatilepheretse kukhala mboni za Yesu.
4. MAPHUNZIRO OCHOKERA M’KALATA ZA AEPISKOPI ATHU
(a) Kutengapo gawo pomanga mtndu wathu ndi udindo wa nzika iliyonse. (Kulimbikitsa Masomphenya a Kumene Tilikupita, 1 December 2013, p. 12)
(b) Ngati Akhristu, tiri ndi udindo woonetsetsa kuti tikutenga nao gawo mwanzeru povotera atsogoleri amene ali ndi zowayenerera ndiponso otha kukwaniritsa udindo wao umene tawasankhira. (Kusankha Atsogoleri, 28 December 2003, pp. 2 – 3)
(c) ‘Tivomere udindo wodziunika ife eni moonadi’; chifukwa pakutero, tikukhulupirira kuti dziko la Malawi lidzakhala latsopano momwe anthu ake azidzalemekezana pofufuza zoyenera kuchita kuti chitukuko chenicheni chikwaniritsidwe pakati pathu. (Kuwerenga ndi Kutanthauzira Zizindikiro za Nthawi ndi Nyengo, 31 October 2010, p. 8)
(d) ‘Ndi Amalawi amene angathandize kutukula dziko la Malawi.’ (Tsogolo Lathu Liri Mmanja Mwathu: Ulendo Wathu ku Chisankho cha 2009, 11 May 2008, p. 14)
(e) ‘Khalidwe la ulesi lilipo pakati pathu m’Malawi muno…tikunenetsa kuti ulesi ndi tchimo lokhudza waulesiyo komanso Fuko lonse. (Kusankha Tsogolo Lathu, 1993, p. 9)
(f) Tili kuyembekeza kuti nzika zonse zizitenga nao gawo mwachikulu m’zochitika m’dziko lathu lino. (Kusankha Tsogolo Lathu, 1993, p. 9)
5. ZOYENERA KULINGALIRA
(a) Kodi nkhani ya ku Emmausi yomwe tikuphunzirapo za kufunika kwa kumvetsera Mau a Mulungu komanso kuchita nao Nsembe ya Misa ingatithandize bwanji kukhala mboni ndi kulalika chikhulupiriro chathu?
(b) Pamene ophunzira awiri aja ankayenda pamodzi ndi Yesu ndipo potero adamvetsa dongoolo lomwe Mulungu anali nalo pofuna kupulumutsa mtundu wa anthu, tichite zotani kuti nzika zaku Malawi nazonso zikhale zoopa Mulungu kuti Fuko lathu likhale lokondana?
(c) Tingaphunzirepo zotani kuchokera ku zimene ophunzira aku Emmausi adaziona zotha kutithandiza kulimbana ndi kutaya mtima, kukhumudwa ndi zina zotero?
(d) Tichite zotani kuti nzika zonse muno m’Malawi zitenge nao mbali pokambirana ndi kusefa zinthu zimene zingathe kukometsa dziko lathu?
11 May, 2014: LA MUMULUNGU LA 4 LA PASAKA
1. CHOLINGA: MBUSA WABWINO
MAU OYAMBIRIRA: Chikhristu chidabwezeretsa ndi kukweza ulemerero wa munthu. Anthu onse adalengedwa m’chifanizo ndiponso ndi ana a Mulungu. Mulungu ngati Tate wathu, adatikonda kwambiri kotero kuti adatipatsa mwana wake wokondeka Yesu. Yesu adatikonda potifera pamtanda pofuna kutipulimutsa. Apa ndi pomwe pali kufanana mu ulemerero wa munthu aliyense. Choona chenicheni, ndiye maziko a Demokalase; Boma liyenera kukhala la anthu, loyendetsedwa ndi anthu ndiponso lokomera anthu omweo. Motero, mkhalidwe wonyada, wodzikonda ndi wongofuna zabwino za anthu ochepa ulibe malo m’dziko loopa Mulungu.
2. KUMVETSA MAU ALERO
MAU OYAMBA: Ntchito 2:14, 36-41
Anthu ndi amene adapachika Yesu pamtanda koma Mulungu Atate ndi amene adamuukitsa kwa akufa. Nanga ife tichitepo chiani? Tiyenera kutembenika mtima pakuchita izi:
i) Kulapa ndi kubatizidwa
ii) Kulandira mtima watsopano
iii) Kuyamba moyo watsopano
iv) Kupewa machimo amene timawabwerezabwereza
SALIMO: 22: 1-6
Mulungu ndi amene amatipatsa chakudya ndi madzi ambiri. Tiyeni tisankhe atsogoleri amene adzatithandiza kuti tidzikhala ndi chakudya chokwanira m’dziko lathu.
MAU ACHIWIRI: 1 Petro 2: 20-25
Aroma ambiri ankadziganizira ndi kudziona ngati anthu apamwamba pakati pa anzawo, motero sankafuna kugwira ntchito zamanja ndipo anali ndi akapolo owagwirira ntchito m’nyumba ndi m’minda mwawo. Akapolo sankaloledwa kukwatira kapena kukwatiwa kotero kuti ena mwa iwo ankangolowana ndipo ana oberekedwa ndi makolo otere, ankasanduka ana mbuye wawo.
MTHENGA WABWINO: Yohane 10:1-10
(a) Yesu akudziyerekeza ngati Mbusa wabwino wosamalira nkhosa zake.
(b) Panali ubale waukulu pakati pa mbusa ndi nkhosa zake. Ankadziwa nkhosa iliyonse ndipo nkhosazo zinkadziwa mau ake. Mbusa ankakhala patsogolo pa nkhosa zake ndipo nkhosazo zikamutsatira pambuyo. Zina mwa ntchito za mbusa zinali kutengera nkhosa zake kunsipu obirirwira, kuzipatsa madzi ndi kuziteteza ku zilombo zolusa.
(c) Khomo ndi chizindikiro chamalire pakati pakunja ndi mkati.
(d) Iye amene amalowera pa zenera mmalo molowera pakhomo ndi wakuba ndiponso wolanda. Anthu otere ndi omwe amaganizira zobera mavoti. Iwo safuna kutumikira anthu koma amangofuna ulemerero, kudzikundikira chuma ndi kudzilemeretsa okha.
3. MAPHUNZIRO:
(a) Monga adachitira Ayuda, ife timapachika Yesu pamtanda nthawi zonse pamene tipondereza amphawi, pamene sitikonda dziko lathu ndiponso pamene titsatira makhalidwe achikunja monga kuchotsa mimba.
(b) Ngati anthu tonse ndife ofanana, pachikhristu, sibwino kuti ena akhale mabwana ndi kuti ena akhale akapolo. Ngati olengedwa mchifanizo cha Mulungu, munthu aliyense ali ndi ulemerero wake osasunthika. Ndipo choti tidziwe ndi chakuti Yesu adafera anthu onse.
(c) Ufulu wa Demokalase utanthauza kuti nzika iliyonse ipatsidwe mwai wotengapo mbali pa zochitika m’dziko, osati panthawi ya masankho yokha koma nthawi zonse. Anthu ayenera kupeza zosowa zawo ndipo atsogoleri akhale woyamba kupereka zitsanzo zabwino pakati pa anthu kudzera m’mau ndi m’makhalidwe awo.
4. MAPHUNZIRO OCHOKERA M’MKALATA ZA AEPISKOPI ATHU
(a) Munthu ofuna kuima nawo pachisankho ayenera kukhala okhulupirika, olimba mtima, wanzeru zabwino ndiponso wophunzira ndi wanzeru zambiri. Ayenera kulemekeza maufulu amabanja, zipembedzo za anthu ena ndi ozindikira ntchito ndi udindo wake pakati pa anthu (Tingamange bwanji fuko lachimwemwe, 1961).
(b) Momwemonso ife tikupempha Akatolika aluso losiyanasiyana kuti akhale ndi chidwi cholowa nawo ndale pofuna kuti agwiritse ntchito luso lawo pufuna kuti amange demokalase pangodya zachikhristu; Pajatu ndale ndi njira yoyendetsera boma osati kukolana ndi kugwetsana monga tidziwira nthawi zonse. Tingamange bwanji fuko lachimwemwe, 1961).
(c) Munthu wofuna kupikisana nawo pachisankho, ayenera kukhala ndi zomuyenereza; akhale otha kuchita zinthu ndiponso mtima odzipereka ku ntchito yotumikira anthu. Palibe chimene chingachitike ngati atsogoleri komanso anthu ena m’dziko alibe mtima wofuna kugwira ntchito molimbika (Tingamange bwanji fuko lachimwemwe, 1961).
(d) Mtsogoleri wabwino ndi amene ali ndi mtima wofuna kutumikira anthu. Aphungu a Kunyumba ya Malamulo ndi otumikira anthu monga antchito ena onse aboma ngati aphunzitsi, madokotala, anamwino, etc amene amatumikira aliyense, olemera kapena osauka, achinyamata kapena okalamba, okhala m’tawuni kapena okhala kumidzi. Iwo amatumikira anthu pokhala limodzi ndi anthuwo, pakumvetsera zosowa zawo ndi pakuwalankhulira m’malo mwawo. Zizindikiro zilizonse zosonyeza kuti wofuna kupikisana nawo pachisankho ali ndi maganizo ongofuna kudzilemeretsa mosalabadira zosowa za anthu, ndi chifukwa chokwanira kuti tisamuvotere (Tingamange bwanji fuko lachimwemwe, 1961).
(e) Kuchita zinthu mwapoyera ndi chinthu chofunikira kwambiri ndipo ichi chikuphatikizapo kukhala omasuka kuti anthu athe kuona ndi kuunika zimene yemwe akufuna kupikisana nawo akuchita ndiponso kukhala wokonzeka kufotokozera mfundo za boma ndi momwe ndalama zagwiritsidwira ntchito (Tingamange bwanji fuko lachimwemwe, 1961).
(f) Anthu okhawo amene ali okhulupirika, odalilika ndi odzichepetsa ndi amene ayenera kusankhidwa (Tingamange bwanji fuko lachimwemwe, 1961).
(g) Anthu oyenera kusankhidwa ndi amene angathe kuunikira, kuongolera ndi kulimbikitsa anthu. Anthu otere ndi amene angalimbikitse anthu m’madera mwawo kuti azindikire ulemerero wao, ndi kuti anthuwo adzimasule mu ukapolo ongodalira thandizo la ena ndi kukhala odziimira paokha. Ayenera kulimbikitsa anthu awo kuti atukule miyoyo ndi mabanja awo ndi kupititsa patsogolo chitukuko cha dziko (Tingamange bwanji fuko lachimwemwe, 1961).
(h) Nthawi ya chisankho imapatsa nzika mwai ounika momwe nkhani za chuma, maphunziro, umoyo, utsogoleri wabwino, chitukuko ndi zina zotero zikuyendera. Iyi ndi nthawi yosankha ndi kutsimikiza atsogoloreri amene achita bwino ndi kuchotsa amene alephera (Kusankha Atsogoleri athu, 2003).
5 ZOYENERA KULINGALIRA
(a) Mogwirizana ndi Khristu Mbusa Wabwino, kodi mumamvetsa chiani pa zautsogoleri ngati utumiki?
(b) Tingazindikire bwanji atsogoleri osazindikira chimene akuchita, opanda masomphenya, opanda mfundo zachitukuko ndiponso omwe sangathe kupeza njira zothanirana ndi mavuto amene Malawi akukumana nawo?
(c) Kodi tingaunike bwanji m’mene tikuchitira pa ntchito za ulimi, maphunziro, umoyo, zomangamanga ndi zina zambiri pa nthawi ino pamene Malawi akukwanitsa zaka 50 za ufulu wodzilamulira?
(d) Kodi timamvetsa bwino za zosowa zathu ndiponso m’mene tingazipezere? Kodi takambirana motani za zosowa zathu ndi anthu amene akufuna kukaima nawo pachisankho chapatatu chikubwerachi?
(e) Tichite chiyani ndi atsogoleri olephera omwe safuna kupitiliza zabwino zomwe mautsogoleri am’mbuyomu adaziyamba?
(f) Tingachite chiyani pofuna kuti tidzasankhe atsogoleri amene adzalemekeze chikhululupiriro chathu?
MAU OTSIRIZA
Yesu adati, “Nthawi Yakwana, Ufumu wa Mulungu wayandikira. Tembenukani mtima ndi kukhulupirira Mthenga Wabwinowu” (Mk 1: 15). Aliyense ali ndi udindo woti akwaniritse kuti Ufumu wa Mulungu ukhazikitsidwe m’dziko lapansi. Tiyeni tionetsetse kuti Mulungu yekha ndiye amene akulandira ulemu ngati mwini zonse ndipo tikatero, mtendere udzatsikira dziko lapansi. Popeza Mulungu adapereka dziko lapansi kwa anthu ake, tili ndi udindo wotenga nawo mbali m’chisankho chili kubwerachi posankha:
Atsogoleri amene ndi oopa ndi okhulupirira Mulungu ndipo ali ndi mtima wofuna kuchita kwake. Tikuyenera kuvomera kuti Mulungu ndi Mlengi ndi Kasupe wa zinthu zonse. Kusankha atsogoleri amene sakhala tcheru kuti adziwe kufuna kwa Mulungu kuli ngati kudzitemberera ife tomwe ndi Fuko lathu lonse.