BANJA: MALO APADERA OPEZERAMO MPHATSO YA CHIKONDI

One of the presenter on live transmissionBANJA: MALO APADERA OPEZERAMO MPHATSO YA CHIKONDI
______________________________________________
La Mulungu la 49 La Kufalitsa Uthenga ku Malawi
LAMULUNGU, 26 JULAYI, 2015

Okondedwa Abale ndi Alongo mwa Ambuye,

Pa Lamulungu la 49 lokumbukira za kufalitsa uthenga padziko lonse la m’chaka cha 2015, ndikukumbukira ndi kukupemphani kuti, mogwirizana ndi mutu wa chaka chino womwe uli pamwambapo, tisinkhesinkhe mozama poyang’anitsitsa banja motsogozedwa ndi mawu a Apapa Francis otsindika kufunika kwa kulumikizana ndi kukambirana m’banja, komwe ndi maziko a chikondi chenicheni. Ichi ndi chinthu chofunikira kwambiri kuno kwathu ku Malawi chifukwa, monga mukudziwa, Mpingo uli kalikiliki kukonzekera kuchita Sinodi ya Moyo wa Banja.

Kuwonjezera apo, pa 31 Januwale, 2015, Maekiskopi athu kudzera m’Bungwe la Maepiskopi a Katolika kuno ku Malawi la Episcopal Conference of Malawi (ECM), mounikiridwa ndi mfundo zomwe nthumwi zidakambirana pa msonkhano wa AMECEA womwe udachitikira kuno ku Malawi mwezi wa Julayi, 2014,adaatipempha kuti, ngati alaliki, tichitepo kanthu pa momwe moyo ndi chikhalidwe cha anthu zikusinthira. Pa msonkhanowu Banja ndi kukambirana kapena kulumikizana inali iwiri mwa mitu imene nthumwi zidakambirana mozama pa nkhani yokhudza kufalitsa Uthenga Wabwino.

Chaka chino, Tsiku Lofalitsa Mauthenga Padziko Lonse likutipatsanso mwawi woona mgwirizano womwe ulipo pakati pa moyo wa m’banja ndi udindo wa kufalitsa Uthenga Wabwino pogwiritsa ntchito njira zamakono. Nchodziwikiratu kuti zipangizo zamakono zofalitsira mauthenga nzofunika kwa ife tonse m’njira zosiyanasiyana. Koma ngakhale zili choncho, tikuzindikiranso kuti zipangizo zamakono zimenezi zili ndi ubwino ndi kuipa kwake komwe kumakhudza miyoyo ya anthu ambiri malinga ndi momwe anthu akuzigwiritsira ntchito.

Kulumikizana kwa anthu m’Banja

Mpingo wa Katolika umakhulupirira kuti banja ndi chinthu chofunikira kwambiri pakati pa anthu ndiponso pa utumiki wa Mpingo. Apapa Fransisko chaka chino adanena kuti m’Banja Lachikhristu ndi malo omwe anthu amaphunziramo kulumikizana kwenikweni ndi kulimbitsa mtima wa ubale. Mu Uthenga wawo wa Lamulungu la 49 la Kufalitsa Uthenga Padziko Lonse, Apapa Fransisko akutithandiza kusinkhasinkha pa nkhani yopezeka pa Luka 1: 39-56 ya Maria woyendera msuweni wake Elizabeti, pomwe amayi awiriwa adagawana kuchokera pansi pa mtima za chikhulupiriro chawo.

Kuchokera pa uthenga wa Apapa, titha kutolapo zinthu zingapo:

1. M’banja Lachikhristu, kukambirana kuyenera kulumikizitsa thupi (monga m’mene mwana amachitira polumphalumpha m’mimba mwa mayi wake) ndi mzimu ( monga amayi awiri, anagawana za chimwemwe chawo).

2. Kukambirana m’banja kuyenera kulumikizitsa mwamuna, mkazi ndi ana komanso kuwalumikizitsa ndi Mulungu kudzera m’mapemphero.

3. M’banja Lachikhristu, bamboo, mayi ndi ana ayenera kuphunzira momwe anthu ayenera kuonetseranana chikondi ndi kuthandizirana wina ndi mnzake.

4. Banja Lachikhristu ndi malo momwe eni ake amaphunziriramo kumvetsetsana ndiponso kuvomera zofooka za wina ndi mnzake nkumakhululukirana.

Mwachidule, kulumikizana ndi chinthu chofunikira kwambiri m’moyo wa Mpingo chifukwa, ngati banja la Mulungu, akhristu ayenera kukhala olumikizana. Ichi nchifukwa chake Mkhristu aliyense ayenera kukhala ndi chidwi chofalitsa Mthenga Wabwino pogwiritsa ntchito zida zamakono zomwe iye angakhale nazo.

Kugwiritsa ntchito Zida Zamakono zofalitsira Mauthenga m’Banja

Malinga ndi kafukufuku wina amene adachitika, dziko la Malawi ndi limodzi mwa maiko amene apita patsogolo kwambiri pa nkhani yogwiritsa ntchito zida zamakono zofalitsira mauthenga makamaka makomputa ndi lamya za m’manja. Izi zasandukadi gawo lofunikira kwambiri pa moyo wandale ndi chitukuko cha kwa Amalawi ambiri okhala m’matauni ndi m’madera a kumidzi. Komabe, potsata maganizo a Apapa Francis ndiponso poyang’anira udindo wa Mpingo pa nkhani yofalitsa uthenga wabwino, ine ndili ndi mafunso awiri ofunika kuti tisinkhesinkepo:

a. Kodi ifeyo tikugwiritsa ntchito bwanji zida zamakono zofalitsira mauthenga pofuna kugawana nkhani za chikondi ndi kulumikizana wina ndi wina ndi mnzake?

a. Kodi makolo ndi aphunzitsi, mukuwathandiza bwanji ana anu ndi achinyamata kuti azitha kugwiritsa ntchito zida zamakono zofalitsira mauthenga m’njira yowapindulira m’masiku amakono ano pamene kufalitsa nkhani ndi mauthenga zapita patsogolo – zalowa dijito?

Tikamvetsera akhristu ambiri za zimene akuziona zokhudza kagwiritsidwe ntchito ka zida zamakono zofalitsira mauthenga, kukuwoneka kuti ambiri sakukondwera ndi momwe ena akugwiritsidwira ntchito zidazi, makamaka poganizira izi:

a. Mwamuna ndi Mkazi
• Amuna ndi akazi ena a pabanja akumatumiza kapena kulandira mauthenga onyansa kuchokera kwa anthu ena kudzera mm’zida monga ma lamya am’manja zomwe pamapeto pake, zikumadzetsa mikangano ndi kusamvetsana m’banja.

• Amuna ndi akazi ena a pabanja salola kuti mnzawo wa pabanja aone kapena kugwiritsa ntchito lamya yawo ya m’manja kapena komputa yawo – chomwe chimadzetsa kukayikirana ndi kusakhulupirirana pakati pawo.

• Amuna ndi akazi ena a pabanja amalandira mauthenga kapena lamya pakati pa usiku zomwe zimangokulitsa kusakhulupilirana pakati pa mkazi ndi mwamuna.

• M’malo mocheza kapena kukambirana ndi mnzawo wabanja zinthu zokomera banja lawo, amuna ndi akazi ena amakhalira kuyankha mauthenga ochokera kwa anzawo pa lamya zawo za m’manja.

• Amuna ndi akazi ena a pabanja amatenga zida zamakono zofalitsira mauthenga ngati abwenzi ocheza nawo kotero kuti salabadiranso za mnzawo wa banja.

• Makolo ena akuthera ndalama zawo pa kugula zida zamakono zofula zotumizira ndi kulandirira mauthenga m’malo mosamalira ana awo.

b. Ana

• Achinyamata ena omwe ndi ophunzira m’sukulu kapena makoleji amaononga ndalama zambiri zomwe makolo awo amawapatsa pa kugwiritsa ntchito lamya za m’manja, m’malo mogula zinthu zofunika pa maphunziro awo.

• Achinyama ena akutaya nthawi pomafufuza zithunzi ndi makanema olaula ndi mauthenga ena oipa pa lamya zawo za m’manja.

b. Ansembe ndi amuna ndi akazi amZipani
Zina kambu zina leku, zikuonekanso kuti kugwiritsa ntchito molakwika zida zolandirira ndi kutumizira mauthengazi sikukukhudza amuna kapena akazi a pabanja ndi ana okha ayi. Ngakhale ena mwa ansembe, abulazala ndi asisiteri a m’zipani zosiyanasiyana za mu Mpingo agwa m’mbuna yomweyi. Mwachitsanzo, pakati pathu mchitidwe wotanganidwa ndi kuyankha lamya zathu nthawi ya Nsembe ya Misa, tikakhala pa misonkhano, kubanikira lamya zathu za m’manja pamene m’malo mwa kudya limodzi kapena kucheza ndi ansembe kapena anzathu a m’chipani omwe tikukhala nawo pamodzi, ukukulirakulira. Tsono kodi ngati iwo amene adasankha kudzimana zambiri kuti atsatire ndi kutumikira Khristu akukomedwa ndi kutengeka ndi zinthu zimenezi, angathandize bwanji am’mabanja ndi achinyamata kuti azigwiritsa ntchito moyenera zida zamakono zotumizira ndi kulandilira mauthengazi?

Tiyeni titembenuke mtima
Monga momwe taoneramu, pafunika ndithu kuti akhristu achitepo kanthu pankhani ya kugwiritsa ntchito moyenera njira ndi zida zamakono zofalitsira mauthenga. Tikuyenera kumanga mfundo imodzi yoti m’mabanja achikhristu ndi malo apadera momwe tiyenera kupezamo chikondi cha Mulungu pokhala olumikizana mwachikhristu ppamene tikugwiritsa ntchito zida zomwe tili nazo. Zipangizo zimenezi zikhale zida zotithandiza ife kuti tizikhala moyo wosagalala wapabanja ndi kutisendeza kufupi ndi Mulungu. Tisalole kuti zitidyere nthawi yocheza ndi mabanja athu ndi Mulungu. Tisalole kuti zida zimenezi zitilepheretse kukwaniritsa udindo wathu, ungakhale udindo pa maphunziro kapena njira zopezera ndalama. Amayi athu Maria Virgo Wodala, amene anapereka nthawi yawo kwa Mulungu ndi kwa banja lake, atipempherere tonsefe.

Ndine wanu mwa Khristu,

Bishopu Martin Mtumbuka

Wapampando wa Zofalitsa Mauthenga
Bungwe la Maepisikopi ku Malawi
26 Julayi, 2015

Leave a Comment

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Scroll to Top
× How can we help you?