Uthenga wa ECM wokhudza Bambo Thomas Muhosha

UTHENGA WOCHOKERA KU BUNGWE LA AEPISKOPI ACHIKATOLIKA M’MALAWI (ECM) WOKHUDZA BAMBO THOMAS MUHOSHA

Titamva kuti Bambo Thomas Muhosha akuganiziridwa kuti akukhudzidwa pa nkhani ya kuphedwa kwa McDonald Masambuka yemwe anali wachialubino, ife Aepiskopi Achikatolika tinali ndi msonkhano wadzidzidzi womwe unachitikira ku Catholic Secretariat ku Lilongwe pa 20 April, 2018. Monga adachitira a Bishop a Dayosezi ya Zomba, tonsefe sitikumvetsa ndipo ndife okhumudwa ndi ozizidwa nkhongono ndi mlandu ndi m’chitidwe woopsa ngati umenewu. Ngati Aepiskopi Achikatolika m’Malawi, tikupepesa kuchokera pansi pamtima banja ndi abale ake a malemu McDonald Masambuka ndiponso abale ena onse a anzathu amene adachitiridwa nkhanza za mtundu woterewu.

Ndife okhumudwa ndi achisoni kwambiri kuti wansembe wathu akuganiziridwa kuti nkhaniyi ikumukhudza.

Mogwirizana ndi a Bishop a Dayosezi ya Zomba, tikudzudzula mwamphamvu mkhalidwe woipa ngati umenewu ndipo tidzapitiriza kudzudzula mchitidwewu nthawi zonse. Mpingo Wakatolika umalemekeza ndi kuteteza ulemelero wa munthu aliyense ndipo kupha kwa anthu achialubino ndi tchimo lalikulu lolephera kulemekeza ulemelero wa munthu. Kwa abale ndi alongo athu achialubino, tikukutsimikizirani kuti tidzapitiriza kukuthandizani, kukutetezani ndi kuonetsetsa kuti simuli pachiopsezo ai. Kwa Akatolika onse, ngakhale kuti tonse nkhaniyi yatifowola ndi kutitayitsa mtima, tikukutsimikizirani kuti chilungamo chiyenera kuchitika pa nkhaniyi ndipo malamulo a dziko ayenera kutsatidwa mosachotsera.

Tikupempha Akatolika onse kuti akhale olimba m’chikhulupiriro ndi kumapemphererana. Kwa Ansembe ndi onse am’Zipani za mu Mpingo, tisamaiwale kuti, ngati atsogoleri azauzimu, tili ndi udindo wothandiza anthu kuti asendere pafupi ndi Mulungu. “Tikuyenera kukhulupirira zomwe timawerenga mu Mthenga wa Yesu Khristu, komanso tikuyenera kuphunzitsa zomwe timakhulupirira ndikuchita zomwe timaphunzitsazo”.

Tikufuna kutsindikanso kuti, sitidzatenga nao mbali ina iliyonse kutchinjiriza kuti chilungamo chisaoneke ndipo tikupemphera kuti chilungamo chichitike kwa wina aliyense.

Yalembedwa pa 20 April, 2018

Most Rev. Thomas Luke Msusa

Rt. Rev. Martin Mtumbuka

Most Rev. Tarcizio G. Ziyaye

Rt. Rev. Peter Musikuwa

Rt. Rev. Montfort Stima

Rt. Rev. George Tambala

Rt. Rev. John Ryan

Very Rev. Msgr. John Chithonje

 

 

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *