Episcopal Conference of Malawi

Loading

UTHENGA WA PA TSIKU LOKUMBUKILA ZA MATENDA A EDZI

UTHENGA WA PA TSIKU LOKUMBUKILA ZA MATENDA A EDZI

CathhealthCommKUDZIPEREKA POPEWA KA CHIROMBO KA HIV: MGWIRIZANO WOTHETSA MATENDA A AIDS
-‘Osatopa pochita zabwino’ (2 Thess. 3:13)
Uthenga wa HIV/AIDS kwa aliyense mchaka cha 2016
Kuchokera ku ECM Health Commission

1.0 CHIYAMBI
Lero mu kalendala wa mapemphero a Mpingo wa Katolika, ndi lamulungu loyamba la Adventi. mpingowu ukuyamba mapemphero astopano a pachaka umene uli ulendo watsopano wa chikhulupiriro. Pamene Mpingo ukuyamba kalenda yatsopano yapa chaka, mpingo umakumbukira nawo matenda a EDZI pamodzi ndi dziko lonse la pansi.Tsiku lokumbukira mataenda a EDZI limakhala pa 1 Disembala chaka chilichonse,tsikuli linakhazikitsidwa m’dziko lonse lapansi pofuna kudziwitsa anthu,kuthana ndi tsankho ndi kupititsa maphunziro patsogolo pa nkhani za EDZI, ndimwayi wawukulu pamene maiko, ma pologalamu oyang’anira zamatenda a AIDS, a mabungwe komanso anthu osiyanasiyana pa dziko lapansi akuganizilapo, ndikutengapo mbali mwachidwi pa nkhani ya mliri wa kachilombo ka HIV, makamaka pofufuza njira za tanthauzo ndiponso zodalilika pofuna kubweretsa mayankho oyenera pothana ndi EDZI. Monga akhirisitu tsiku lokumbukira matenda a EDZI limatipatsa nthawi ya mtengowapatali kuti tiunikire za matenda a EDZI ndikutikumbutsa udindo wathu polimbana ndi mliri wa matenda a EDZI. Chaka chino tilingalira pa mutu wakuti “Kudzipereka popewa ka chirombo ka HIV”, Mutu umenewu utipangitsa ife ngat mpingo ndi anthu ake kuti tilingalire udindo wathu polimbana ndi mliri wa EDZI , ndikufuna kuthetsa mliriwu chikamafika chaka cha 2030.

1.1 KUDZIPEREKA POPEWA KA CHIROMBO KA HIV

Muno m’Malawi, chiwerengero cha anthu otenga kachilombo ka HIV chatsika kuchokera pa 42,000 mu 2014 kufika pafupifupi 33,000 mu chaka cha 2015. Kuchepa kwa kufala kwa tizilombo ta HIV pakati pa anthu akuluakulu padziko lonse lapansi kwatsikanso. Tikhoza kuthetsa kufala kwa mlili wa EDZI tikamafika chaka cha 2030. “Tidzipereke popewa kufala kwa HIV” ndi kampeni yomwe ikulimbana ndi ka kachilombo ka HIV ndi mmene matendawa amakhudzira anthu osiyanasiyana.

2.0 Dongosolo la kagwiridwe ka ntchito
Pokumbukira matenda a EDZI m’dziko lapansi, ife a “Catholic Health Commission” tikuitana atsogoleri azipembedzo nonse, ndi anthu onse akufuna kwa bwino potengapo gawo polimbana ndi matenda a EDZI, monga mpingo tikhoza kutengapo gawo pogwirana nawo manja polimbana ndi matenda a EDZI , tikhoza kutero pochita izi:
• Kayezetsa magazi athu, kuti tidziwe mmene m’thupi mulili; kuyezetsa magazi ndi kwaulere mzipatala zonse zimene amayeza magazi.
• Kulimbikitsa akhiritu anzathu kukayezetsa magazi ndi kukalandira uphungu wabwino
• Kumwa mankhwala mwa ndondomeko kwa anthu amene apezeka nako kachirombo ka HIV kutha kuchepetsa mliri komanso kufala kwa kachilombo koyambitsa EDZI
• Kukhazikitsa mapulogalamu olimbikitsa achinyamata kuti adzidziletsa kuti apewe kutenga kapena kupatsirana kachilomboka
• kulimbikitsa anthu a pa banja kukhala okhupirika kwa wina ndi mzake
• kukambirana nkhani zokhudza kugonana ndi achinyamata
• kuphatikiza nkhani za EDZI makamaka nkhani zopewa EDZI muntchito zonse zomwe azibusa amagwira.
• kufuna kupititsa patsogolo luso kwa azibusa opereka uphungu kwa anthu
• Kukhazikitsa maphunziro a uphungu kwa ansembe, agulupa, atsogoleri a mipingo, ndi atsogoleri athu kumudzi;
• Kukonza tsiku lotsegulira magulu osiyanasiyana pa parishi;
• kupanga magulu a achinyamata
• Kukambirana momasuka pa maphunziro ogonana, ndi kachilombo koyambitsa EDZI m’banja.

Tiyeni tonse titengepo mbali pa kampeni wa “KUDZIPEREKA POPEWA KA CHIROMBO KA HIV” ndipo tiwonjezere mphamvu polimbana ndi kachilombo ka HIV kuti katheretu pofika chaka cha 2030.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

× How can we help you?